MALAKI Mau Oyamba
Mau Oyamba
Mneneri Malaki adalalikira nthawi imene Ayuda anali atamanganso Kachisi wa Yehova ku Yerusalemu. Iye analangiza ansembe ndi anthu ao, kuti adziperekenso kwa Yehova ndi kumamutumikira mokhulupirika, ndi kuti apewe ziphuphu, zachiphamaso ndi kunyenga kulikonse, ndipo asamale za chipembedzo.
Ansembe ndi anthu ena amachita chinyengo pa zopereka zao kwa Mulungu, ndipo samatsana chiphunzitso cha Mulungu.
Mneneriyo anawauzanso kuti lidzafika tsiku limene Yehova adzabwera kudzazenga mlandu ndi kuyeretsa anthu ake, ndipo adachita izi potumiza wamthenga wake kuti akakonze njira ndi kunenera za chipangano chake.
Za mkatimu
Kuchimwa kwa Aisraele pa zinthu zina ndi zina 1.1—2.16
Yehova akubwera kudzaweruza ndi kuyeretsa anthu ake 2.17—4.6
Currently Selected:
MALAKI Mau Oyamba: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi