LUKA 6
6
Yesu Mbuye wa tsiku la Sabata
(Mat. 12.1-8; Mrk. 2.21-28)
1Ndipo kunali tsiku la Sabata, Iye analinkupita pakati pa minda ya tirigu; ndipo ophunzira ake analinkubudula ngala za tirigu, nazifikisa m'manja mwao, nadya. 2#Eks. 20.10Koma Afarisi ena anati, Muchitiranji chosaloledwa kuchitika tsiku la Sabata? 3#1Sam. 21.1-6Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi simunawerenganso ngakhale chimene anachita Davide, pamene paja anamva njala, iye ndi iwo anali naye pamodzi; 4#Lev. 24.9kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, natenga mikate yoonetsera, nadya, napatsanso iwo anali naye pamodzi; imeneyi yosaloledwa kudya ena koma ansembe okha? 5Ndipo Iye ananena kwa iwo, kuti, Mwana wa Munthu ali Mbuye wa tsiku la Sabata.
Achiritsa munthu wa dzanja lopuwala
(Mat. 12.9-14; Mrk. 3.1-6)
6 #
Yoh. 9.16
Ndipo kunali tsiku lina la Sabata, Iye analowa m'sunagoge, naphunzitsa. Ndipo munali munthu momwemo, ndipo dzanja lake lamanja linali lopuwala. 7Ndipo alembi ndi Afarisi analikumzonda Iye, ngati adzachiritsa tsiku la Sabata; kuti akapeze chomneneza Iye. 8Koma Iye anadziwa maganizo ao; nati kwa munthuyo wa dzanja lake lopuwala, Nyamuka, nuimirire pakatipo. 9Ndipo Iye ananyamuka, naimirira. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ndikufunsani inu, Kodi nkulola tsiku la Sabata, kuchita zabwino, kapena kuchita zoipa? Kupulumutsa moyo, kapena kuuononga? 10Ndipo pamene anaunguzaunguza pa iwo onse, anati kwa iye, Tansa dzanja lako. Ndipo iye anatero, ndi dzanja lake linabwerera momwe. 11Koma iwowo anagwidwa misala; nalankhulana wina ndi mnzake kuti amchitire Yesu chiyani.
Yesu asankha ophunzira khumi ndi awiri
(Mat. 10.1-4; Mrk. 3.16-19)
12 #
Mat. 14.23
Ndipo kunali masiku awa, Iye anatuluka nanka kuphiri kukapemphera; nachezera usiku wonse m'kupemphera kwa Mulungu. 13Ndipo kutacha, anaitana ophunzira ake; nasankha mwa iwo khumi ndi awiri, amene anawatchanso dzina lao atumwi: 14#Yoh. 1.42Simoni, amene anamutchanso Petro, ndi Andrea mbale wake, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Filipo, ndi Bartolomeo, 15ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Simoni wotchedwa Zelote, 16#Yud. 1ndi Yudasi mwana wa Yakobo, ndi Yudasi Iskariote, amene anali wompereka Iye.
Chiphunzitso cha paphiri
(Mat. 5—7)
17 #
Mat. 4.25; Mrk. 3.7 Ndipo Iye anatsika nao, naima pachidikha, ndi khamu lalikulu la ophunzira ake, ndi unyinji waukulu wa anthu a ku Yudeya lonse ndi Yerusalemu, ndi a ku mbali ya nyanja ya ku Tiro ndi Sidoni, amene anadza kudzamva Iye ndi kudzachiritsidwa nthenda zao; 18ndipo ovutidwa ndi mizimu yonyansa anachiritsidwa, 19#Mat. 14.36; Mrk. 5.30ndi khamu lonse lija linafuna kumkhudza Iye; chifukwa munatuluka mphamvu mwa Iye, nichiritsa onsewa.
20 #
Mat. 5.3; Yak. 2.5 Ndipo Iye anakweza maso ake kwa ophunzira ake, nanena, Odala osauka inu; chifukwa uli wanu ufumu wa Mulungu. 21#Mat. 5.4, 6Odala inu akumva njala tsopano; chifukwa mudzakhuta. Odala inu akulira tsopano; chifukwa mudzaseka. 22#Mat. 5.11Odala inu, pamene anthu adzada inu, nadzapatula inu, nadzatonza inu, nadzalitaya dzina lanu monga loipa, chifukwa cha Mwana wa Munthu. 23#Mat. 5.12Kondwerani tsiku lomweli, tumphani ndi chimwemwe; pakuti onani, mphotho zanu nzazikulu Kumwamba; pakuti makolo ao anawachitira aneneri zonga zomwezo. 24#Mat. 6.2, 5, 16; Luk. 12.21; Yak. 5.1Koma tsoka inu eni chuma! Chifukwa mwalandira chisangalatso chanu. 25#Miy. 14.13Tsoka inu okhuta tsopano! Chifukwa mudzamva njala. Tsoka inu, akuseka tsopano! Chifukwa mudzachita maliro ndi kulira misozi. 26Tsoka inu, pamene anthu onse adzanenera inu zabwino! Pakuti makolo ao anawatero momwemo aneneri onama.
27 #
Mat. 5.44
Koma ndinena kwa inu akumva, Kondanani nao adani anu; chitirani zabwino iwo akuda inu, 28#Luk. 23.34; Mac. 7.60dalitsani iwo akutemberera inu, pemphererani iwo akuchitira inu chipongwe. 29#Mat. 5.39; 1Ako. 6.7Iye amene akupanda iwe pa tsaya limodzi umpatsenso linzake; ndi iye amene alanda chofunda chako, usamkanize malaya ako. 30#Mat. 5.42Munthu aliyense akakupempha kanthu, umpatse; ndi iye amene alanda zako, usazipemphanso. 31#Mat. 7.12Ndipo monga mufuna inu kuti anthu adzakuchitirani inu, muwachitire iwo motero inu momwe. 32#Mat. 5.46Ndipo ngati muwakonda iwo akukondana ndinu, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti ochimwa omwe akonda iwo akukondana nao. 33Ndipo ngati muwachitira zabwino iwo amene akuchitirani inu zabwino, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti anthu ochimwa omwe amachita chomwecho. 34#Mat. 5.42Ndipo ngati mukongoletsa kanthu kwa iwo amene muyembekeza kulandiranso, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti inde anthu ochimwa amakongoletsa kwa ochimwa anzao, kuti alandirenso momwemo. 35#Mat. 5.45; Luk. 6.27Koma takondanani nao adani anu, ndi kuwachitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekeza kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yaikulu, ndipo inu mudzakhala ana a Wamkulukuluyo; chifukwa Iye achitira zokoma anthu osayamika ndi oipa. 36Khalani inu achifundo monga Atate wanu ali wachifundo. Ndipo musamaweruza, ndipo simudzaweruzidwa. 37#Mat. 7.1Ndipo musawatsutsa, ndipo simudzamatsutsidwa. Khululukani, ndipo mudzakhululukidwa. 38#Miy. 19.17; Mat. 7.2; Mrk. 4.24; 2Ako. 9.6-9Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.
39 #
Mat. 15.14
Ndipo Iye ananenanso nao fanizo, Kodi munthu wakhungu angathe kutsogolera mnzake wakhungu? Kodi sadzagwa onse awiri m'mbuna? 40#Mat. 10.24; Yoh. 13.16Wophunzira saposa mphunzitsi wake; koma yense, m'mene atakonzedwa mtima, adzafanana ndi mphunzitsi wake. 41Ndipo uyang'aniranji kachitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda wa m'diso la iwe mwini suuzindikira? 42#Mat. 7.3-5Kapena ungathe bwanji kunena kwa mbale wako, Mbale iwe, leka ndichotse kachitsotso kali m'diso lako, wosayang'anira iwe mwini mtanda uli m'diso lako? Wonyenga iwe! Thanga wachotsa mtandawo m'diso lako, ndipo pomwepo udzayang'anitsa bwino kuchotsa kachitsotso ka m'diso la mbale wako. 43#Mat. 7.16-17Pakuti palibe mtengo wabwino wakupatsa zipatso zovunda; kapenanso mtengo woipa wakupatsa zipatso zabwino. 44#Mat. 12.33Pakuti mtengo uliwonse uzindikirika ndi chipatso chake. Pakuti anthu samatchera nkhuyu paminga, kapena pamtungwi samatchera mphesa. 45#Mat. 12.34-35Munthu wabwino atulutsa zabwino m'chuma chokoma cha mtima wake; ndi munthu woipa atulutsa zoipa m'choipa chake: pakuti m'kamwa mwake mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake.
46 #
Mat. 7.21
Ndipo munditchuliranji Ine, Ambuye, Ambuye, ndi kusachita zimene ndizinena? 47#Mat. 7.24Munthu aliyense wakudza kwa Ine, ndi kumva mau anga, ndi kuwachita, ndidzakusonyezani amene afanana naye. 48Iye afanafana ndi munthu wakumanga nyumba, amene anakumba pansi ndithu, namanga maziko a nyumbayo pathanthwe; ndipo pamene panadza chigumula, mtsinje unagunda pa nyumbayo, ndipo sunakhoza kuigwedeza; chifukwa idamangika bwino. 49Koma iye amene akumva, ndi kusachita, afanafana ndi munthu wakumanga nyumba pa nthaka yopanda maziko; pa imeneyo unagunda mtsinje, ndipo inagwa pomwepo; ndipo kugumuka kwake kwa nyumbayo kunali kwakukulu.
Currently Selected:
LUKA 6: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi