LUKA 24
24
Yesu auka kwa akufa
(Mat. 28.1-16; Mrk. 16.1-8; Yoh. 20.1-18)
1 #
Luk. 23.56
Koma tsiku loyamba la sabata, mbandakucha, anadza kumanda atatenga zonunkhira adazikonza. 2#Mat. 27.60; Mrk. 16.4Ndipo anapeza mwala unakunkhunizidwa kuuchotsa pamanda. 3#Mrk. 6.5; Luk. 24.23Ndipo m'mene analowa sanapeze mtembo wa Ambuye Yesu. 4#Mac. 1.10Ndipo kunali, m'mene anathedwa nzeru nacho, taonani amuna awiri anaimirira pafupi pao atavala zonyezimira; 5ndipo m'mene anakhala ndi mantha naweramira pansi nkhope zao, anati kwa iwo, Mufuniranji wamoyo pa akufa? 6#Mat. 16.21; Mrk. 9.30-31Palibe kuno Iye, komatu anauka; kumbukirani muja adalankhula nanu, pamene analinso m'Galileya, 7#Mat. 16.21; Mrk. 9.30-31ndi kunena, kuti, Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa m'manja a anthu ochimwa, ndi kupachikidwa pamtanda, ndi kuuka tsiku lachitatu. 8#Yoh. 2.22Ndipo anakumbukira mau ake, 9nabwera kuchokera kumanda, nafotokozera zonse khumi ndi mmodziwo, ndi otsala onse omwe. 10#Luk. 8.3Koma panali Maria wa Magadala, ndi Yohana, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi akazi ena pamodzi nao amene ananena izi kwa atumwiwo. 11#Mrk. 16Ndipo mau awa anaoneka pamaso pao ngati nkhani zachabe, ndipo sanamvere akaziwo. 12Koma Petro ananyamuka nathamangira kumanda, ndipo powerama anaona nsalu zoyera pa zokha; ndipo anachoka nanka kwao, nazizwa ndi chija chidachitikacho.
Zochitika pa njira ya ku Emausi
13 #
Mrk. 16.12
Ndipo taonani, awiri a mwa iwo analikupita tsiku lomwelo kumudzi dzina lake Emausi, wosiyana ndi Yerusalemu mastadiya makumi asanu ndi limodzi. 14Ndipo iwowa anakambirana nkhani za izi zonse zidachitika. 15#Mat. 18.20Ndipo kunali m'kukambirana kwao ndi kufunsana, Yesu mwini anayandikira, natsagana nao. 16#Yoh. 20.14; 21.4Koma maso ao anagwidwa kuti asamzindikire Iye. 17Ndipo anati kwa iwo, Mau awa ndi otani mulandizanawo poyendayenda? Ndipo anaima ndi nkhope zao zachisoni. 18#Yoh. 19.25Ndipo mmodzi wa iwo, dzina lake Kleopa, anayankha nati kwa Iye, Kodi iwe wekha ndiwe mlendo m'Yerusalemu ndi wosazindikira zidachitikazi masiku omwe ano? 19#Mat. 21.11; Yoh. 6.14Ndipo anati kwa iwo, Zinthu zanji? Ndipo anati kwa Iye, Izi za Yesu Mnazarene, ndiye munthu mneneri wamphamvu m'ntchito, ndi m'mau, pamaso pa Mulungu ndi anthu onse; 20ndi kuti ansembe aakulu ndi akulu athu anampereka Iye ku chiweruziro cha imfa, nampachika Iye pamtanda. 21#Luk. 2.38; Mac. 1.6Ndipo tinayembekeza ife kuti Iye ndiye wakudzayo kudzaombola Israele. Komatunso, pamodzi ndi izi zonse lero ndilo tsiku lachitatu kuyambira zidachitika izi. 22#Mat. 28.8; Luk. 24.9-10Komatu akazi enanso a mwa ife anatidabwitsa, ndiwo amene analawirira kumanda; 23#Mat. 28.8; Luk. 24.9-10ndipo m'mene sanapeze mtembo wake, anadza, nanena kuti adaona m'masomphenya angelo, amene ananena kuti ali ndi moyo Iye. 24#Luk. 24.12; Yoh. 20.3Ndipo ena a iwo anali nafe anachoka kunka kumanda, napeza monga momwe akazi adanena; koma Iyeyo sanamuone. 25Ndipo Iye anati kwa iwo, Opusa inu, ndi ozengereza mtima kusakhulupirira zonse adazilankhula aneneri! 26#Luk. 24.46; Mac. 3.18; 17.3Kodi sanayenera Khristu kumva zowawa izi, ndi kulowa ulemerero wake? 27#Deut. 18.15; Mas. 22; Yes. 53Ndipo anayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse nawatanthauzira iwo m'malembo onse zinthu za Iye yekha. 28#Mrk. 6.48Ndipo anayandikira kumudzi umene analikupitako; ndipo anachita ngati anafuna kupitirira. 29Ndipo anamuumiriza Iye, nati, Khalani ndi ife; pakuti kuli madzulo, ndipo dzuwa lapendekatu. Ndipo analowa kukhala nao. 30#Mat. 14.19Ndipo kunali m'mene Iye anaseama nao pachakudya, anatenga mkate, naudalitsa, naunyema, napatsa iwo. 31Ndipo maso ao anatseguka, ndipo anamzindikira Iye; ndipo anawakanganukira Iye, nawachokera. 32Ndipo anati wina kwa mnzake, Mtima wathu sunali wotentha m'kati mwathu nanga m'mene analankhula nafe m'njira, m'mene anatitsegulira malembo? 33Ndipo ananyamuka nthawi yomweyo nabwera ku Yerusalemu, napeza khumi ndi mmodziwo, ndi iwo anali nao atasonkhana pamodzi, 34#1Ako. 15.5nanena, Ambuye anauka ndithu, naonekera kwa Simoni. 35Ndipo iwo anawafotokozera za m'njira, ndi umo anadziwika nao m'kunyema kwa mkate.
Yesu aonekera kwa khumi ndi mmodziwo
(Yoh. 20.19-23)
36 #
Mrk. 16.14
Ndipo pakulankhula izi iwowa, Iye anaimirira pakati pao; nanena nao, Mtendere ukhale nanu. 37#Mrk. 6.49Koma anaopsedwa ndi kuchita mantha, nayesa alikuona mzimu. 38Ndipo anati kwa iwo, Mukhala bwanji ovutika? Ndipo matsutsano amauka bwanji m'mtima mwanu? 39#Yoh. 20.20, 27Penyani manja anga ndi mapazi anga, kuti Ine ndine mwini: ndikhudzeni, ndipo penyani; pakuti mzimu ulibe mnofu ndi mafupa, monga muona ndili nazo Ine. 40Ndipo m'mene ananena ichi, anawaonetsera iwo manja ake ndi mapazi ake. 41#Yoh. 21.5Koma pokhala iwo chikhalire osakhulupirira chifukwa cha chimwemwe, nalikuzizwa, anati kwa iwo, Muli nako kanthu kakudya kuno? 42Ndipo anampatsa Iye chidutsu cha nsomba yokazinga. 43#Mac. 10.41Ndipo anachitenga, nachidya pamaso pao.
44 #
Mat. 16.21; Luk. 24.32 Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalmo. 45#Mat. 16.21Ndipo anawatsegulira mitima yao, kuti adziwitse malembo; 46#Deut. 18.15; Mas. 22; Yes. 53ndipo anati kwa iwo, Kotero kwalembedwa, kuti Khristu amve zowawa, nauke kwa akufa tsiku lachitatu; 47#Mat. 28.19; Mac. 13.38ndi kuti kulalikidwe m'dzina lake kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo kwa mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu. 48#Mac. 1.8; 5.31-32Inu ndinu mboni za izi. 49#Yow. 2.28; Mac. 2.1Ndipo onani, Ine nditumiza pa inu lonjezano la Atate wanga; koma khalani inu m'mudzi muno, kufikira mwavekedwa ndi mphamvu yochokera Kumwamba.
Yesu akwera kunka Kumwamba
(Mac. 1.9-11)
50Ndipo anatuluka nao kufikira ku Betaniya; nakweza manja ake, nawadalitsa. 51#Mrk. 16.19Ndipo kunali, pakuwadalitsa Iye analekana nao, natengedwa kunka Kumwamba. 52#Mat. 28.9, 17Ndipo anamlambira Iye, nabwera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu; 53#Mac. 2.46; 5.42ndipo anakhala chikhalire m'Kachisi, nalikuyamika Mulungu. Amen.
Currently Selected:
LUKA 24: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi