YOHANE 20
20
Yesu auka kwa akufa
(Mat. 28.1-10; Mrk. 16.1-14; Luk. 24.1-43)
1 #
Mat. 28.1
Koma tsiku loyamba la Sabata anadza Maria wa Magadala mamawa, kusanayambe kucha, kumanda, napenya mwala wochotsedwa kumanda. 2#Yoh. 19.26Pomwepo anathamanga nadza kwa Simoni Petro ndi kwa wophunzira wina amene Yesu anamkonda, nanena nao, Anachotsa Ambuye kumanda, ndipo sitidziwa kumene anamuika Iye. 3#Luk. 24.12Anatuluka tsono Petro ndi wophunzira winayo, nalinkupita kumanda. 4Koma anathamanga onse awiri pamodzi; ndipo wophunzira winayo anathamanga naposa Petro, nayamba kufika kumanda; 5#Yoh. 19.40ndipo m'mene anawerama chosuzumira anaona nsalu zabafuta zitakhala, komatu sanalowamo. 6Pamenepo anadzanso Simoni Petro alikumtsata iye, nalowa m'manda; ndipo anaona nsalu zabafuta zitakhala, 7#Yoh. 11.44ndi mlezo, umene unali pamutu pake, wosakhala pamodzi ndi nsalu zabafuta, koma wopindika padera pamalo pena. 8Pamenepo tsono analowanso wophunzira winayo, amene anayamba kufika kumanda, ndipo anaona, nakhulupirira. 9#Mas. 16.10; Mac. 2.25-31Pakuti kufikira pomwepo sanadziwa lembo lakuti ayenera Iye kuuka kwa akufa. 10Chifukwa chake ophunzirawo anachokanso, kunka kwao.
Yesu aonekera kwa Maria wa Magadala
11 #
Luk. 24.16-31; Yoh. 21.4 Koma Maria analikuima kumanda kunja, alikulira. Ndipo m'mene alikulira anawerama chisuzumirire kumanda; 12ndipo anaona angelo awiri atavala zoyera, alikukhala mmodzi kumutu, ndi wina kumiyendo, kumene mtembo wa Yesu udagona. 13Ndipo iwowa ananena kwa iye, Mkazi, uliranji? Ananena nao, Chifukwa anachotsa Ambuye wanga, ndipo sindidziwa kumene anamuika Iye. 14#Luk. 24.16-31; Yoh. 21.4M'mene adanena izi, anacheuka m'mbuyo, naona Yesu ali chilili, ndipo sanadziwa kuti ndiye Yesu. 15Yesu ananena naye, Mkazi, uliranji? Ufuna yani? Iyeyu poyesa kuti ndiye wakumunda, ananena ndi Iye, Mbuye ngati mwamnyamula Iye, ndiuzeni kumene mwamuika Iye, ndipo ndidzamchotsa. 16Yesu ananena naye, Maria. Iyeyu m'mene anacheuka, ananena ndi Iye m'Chihebri, Raboni; chimene chinenedwa, Mphunzitsi. 17#Mat. 28.10Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sinditha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Mulungu wanu. 18#Mat. 28.10; Yoh. 16.28Maria wa Magadala anapita, nalalikira kwa ophunzirawo, kuti, Ndaona Ambuye; ndi kuti ananena izi kwa iye.
Yesu aonekera kwa ophunzira, Tomasi palibe
19 #
Mrk. 16.14; 1Ako. 15.5 Pamenepo, pokhala madzulo, tsiku lomwelo, loyamba la Sabata, makomo ali chitsekere, kumene anakhala ophunzira, chifukwa cha kuopa Ayuda, Yesu anadza naimirira pakati pao, nanena nao, Mtendere ukhale ndi inu. 20#Yoh. 16.22Ndipo pamene adanena ichi, anaonetsa iwo manja ake ndi nthiti zake. Pamenepo ophunzira anakondwera pakuona Ambuye. 21#Mat. 28.18; Yoh. 17.18; 20.19, 26Chifukwa chake Yesu anatinso kwa iwo, Mtendere ukhale ndi inu; monga Atate wandituma Ine, Inenso ndituma inu. 22Ndipo pamene anati ichi anawapumira, nanena nao, Landirani Mzimu Woyera. 23#Mat. 16.19; 18.18Zochimwa za anthu ali onse muwakhululukira, zikhululukidwa kwa iwo; za iwo amene muzigwiritsa, zagwiritsidwa.
24 #
Yoh. 11.16
Koma Tomasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, wotchedwa Didimo, sanakhala nao pamodzi, pamene Yesu anadza. 25Chifukwa chake ophunzira ena ananena naye, Tamuona Ambuye. Koma iye anati kwa iwo, Ndikapanda kuona m'manja ake chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika chala changa m'chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika dzanja langa kunthiti yake; sindidzakhulupirira.
Yesu aonekera kwa ophunzira, Tomasi ali nao
26Ndipo pakupita masiku asanu ndi atatu ophunzira ake analinso m'nyumbamo, ndi Tomasi pamodzi nao. Yesu anadza, makomo ali chitsekere, naimirira pakati, nati, Mtendere ukhale ndi inu. 27#1Yoh. 1.1Pomwepo ananena kwa Tomasi, Bwera nacho chala chako kuno, nuone manja anga, ndipo bwera nalo dzanja lako, nuliike kunthiti yanga, ndipo usakhale wosakhulupirira, koma wokhulupirira. 28Tomasi anayankha nati kwa Iye, Ambuye wanga, ndi Mulungu wanga. 29#2Ako. 5.7Yesu ananena kwa iye, Chifukwa wandiona Ine, wakhulupirira; odala iwo akukhulupirira, angakhale sanaona.
30 #
Yoh. 21.25
Ndipo zizindikiro zina zambiri Yesu anazichita pamaso pa ophunzira ake, zimene sizinalembedwa m'buku ili; 31#Luk. 1.4; Yoh. 3.15-16; 1Pet. 1.8-9koma zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Khristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupirira mukhale nao moyo m'dzina lake.
Currently Selected:
YOHANE 20: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi