YEREMIYA 40
40
Yeremiya apita kwa Gedaliya ku Mizipa
1 #
Yer. 39.14
Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, Nebuzaradani kapitao wa alonda atammasula pa Rama, pamene anamtenga iye womangidwa m'maunyolo pamodzi ndi am'nsinga onse a Yerusalemu ndi Yuda, amene anatengedwa am'nsinga kunka nao ku Babiloni. 2#Deut. 29.28Ndipo kapitao wa alonda anatenga Yeremiya, nati kwa iye, Yehova Mulungu wako ananenera choipa ichi malo ano; 3#Deut. 29.24-25; Dan. 9.11ndipo Yehova wachitengera, ndi kuchita monga ananena, chifukwa mwachimwira Yehova, ndi kusamvera mau ake, chifukwa chake chinthu ichi chakufikirani. 4#Gen. 20.15; Yer. 39.12Ndipo tsopano, taona, ndikumasula iwe lero maunyolo ali pa manja ako. Kukakukomera kudza nane ku Babiloni, idza, ndipo ndidzakusamalira bwino; koma kukakuipira kudza nane ku Babiloni, tsala; taona, dziko lonse lili pamaso pako; kulikonse ukuyesa kwabwino kapena koyenera kupitako, pita kumeneko. 5#2Maf. 25.22-25Tsono asanabwerere iye anati, Bweratu kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, amene mfumu ya ku Babiloni inamyesa wolamulira midzi ya Yuda, nukhale naye pakati pa anthu; kapena pita kulikonse ukuyesa koyenera kupitako. Ndipo kapitao wa alonda anampatsa iye phoso ndi mtulo, namleka amuke. 6#Yer. 39.14Ndipo Yeremiya ananka kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa, nakhala kumeneko kwa anthu otsala m'dziko.
7 #
2Maf. 25.22-25
Ndipo pamene akulu onse a makamu amene anali m'minda, iwo ndi anthu ao, anamva kuti mfumu ya ku Babiloni adamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu wolamulira dziko, nampatsira amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi aumphawi a m'dzikomo, a iwo amene sanatengedwe ndende kunka nao ku Babiloni; 8pamenepo anadza kwa Gedaliya ku Mizipa, Ismaele mwana wa Netaniya, ndi Yohanani ndi Yonatani ana a Kareya, ndi Seraya mwana wa Tanumeti, ndi ana a Efayi wa ku Netofa, ndi Yezaniya mwana wa munthu wa ku Maaka, iwo ndi anthu ao. 9Ndipo Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani anawalumbirira iwo ndi anthu ao, kuti, Musaope kuwatumikira Ababiloni; khalani m'dzikomu, mutumikire mfumu ya ku Babiloni, ndipo kudzakukomerani. 10Koma ine, taonani, ndidzakhala pa Mizipa, ndiima pamaso pa Ababiloni, amene adzadza kwa ife; koma inu sonkhanitsani vinyo ndi zipatso zamalimwe ndi mafuta, muziike m'mbiya zanu, nimukhale m'midzi imene mwailanda. 11Chomwecho pamene Ayuda onse okhala m'Mowabu ndi mwa ana a Amoni, ndi m'Edomu, ndi amene anali m'maiko monse, anamva kuti mfumu ya ku Babiloni inasiya otsala a Yuda, ndi kuti inamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani wolamulira wao; 12pamenepo Ayuda onse anabwerera kufumira ku malo onse kumene anawaingitsirako, nafika ku dziko la Yuda, kwa Gedaliya, ku Mizipa, nasonkhanitsa vinyo ndi zipatso zamalimwe zambiri.
13Ndiponso Yohanani mwana wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala m'minda, anadza kwa Gedaliya ku Mizipa, 14nati kwa iye, Kodi mudziwa kuti Baalisi mfumu ya ana a Amoni watumiza Ismaele mwana wa Netaniya kuti akupheni inu? Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sanamvere iwo. 15Ndipo Yohanani mwana wa Kareya ananena kwa Gedaliya ku Mizipa m'tseri, kuti, Ndimuketu, ndikaphe Ismaele mwana wa Netaniya, anthu osadziwa; chifukwa chanji adzakuphani inu, kuti Ayuda onse amene anakusonkhanira inu amwazike, ndi otsala a Yuda aonongeke? 16Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu anati kwa Yohanani mwana wa Kareya, Usachite ichi; pakuti unamizira Ismaele.
Currently Selected:
YEREMIYA 40: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi