YouVersion Logo
Search Icon

OWERUZA 18

18
Ana a Dani alanda mafano a Mika
1Masiku ajawo panalibe mfumu m'Israele; masiku ajanso fuko la Adani anadzifunira cholowa chakukhalako; pakuti kufikira tsiku lija sichinawagwera cholowa chao pakati pa mafuko a Israele. 2#Num. 13.17Ndipo ana a Dani anatuma a banja lao amuna asanu a mwa iwo onse, anthu olimba mtima, a ku Zora, ndi a ku Esitaoli, kuzonda dziko ndi kufunafunamo; nanena nao, Mukani, mufunefune m'dziko. Nafika iwo ku mapiri a Efuremu kunyumba ya Mika, nagona komweko. 3Pokhala iwo m'nyumba ya Mika, anazindikira mau a mnyamata Mleviyo, napatukirako, nanena naye, Anadza nawe kuno ndani? Uchitanji muno? Ukhala nacho chiyani kuno? 4Ndipo ananena nao, Mika anandichitira chakutichakuti, napangana nane za ntchito, ndipo ndikhala wansembe wake. 5#1Maf. 22.5-6; Yes. 30.1Pamenepo ananena naye, Utifunsire kwa Mulungu, kuti tidziwe ngati ulendo wathu timukawo udzakoma. 6Nanena nao wansembeyo, Mukani mumtendere, ulendo wanu muyendawo uli pamaso pa Yehova.
7Pamenepo amuna asanuwa anachoka, nafika ku Laisi; naona anthu anali m'mwemo, kuti anakhala okhazikika mtima, monga anakhala Asidoni, odekha ndi osatekeseka; popeza m'dzikomo munalibe mwini bwalo wakuchititsa manyazi m'chinthu chilichonse; nasiyana kutali ndi Asidoni, ndipo analibe kanthu ndi munthu aliyense. 8Ndipo asanuwo anafikanso kwa abale ao ku Zora ndi Esitaoli; ndi abale ao ananena nao, Mutani inu? 9#Yos. 2.23-24Nati iwo, Taukani, tiwakwerere; pakuti tapenya dziko, ndipo taonani, ndilo lokoma ndithu; ndi inu muli chete kodi? Musamachita ulesi kumuka ndi kulowa kulandira dzikolo. 10#Deut. 8.9Pomuka inu mudzafikira anthu okhazikika mtima ndi dziko lachitando; pakuti Mulungu walipereka m'dzanja lanu; pamenepo mposasowa kanthu kalikonse kali pa dziko lapansi.
11Pamenepo amuna mazana asanu ndi limodzi, omangira zida za nkhondo m'chuuno, anaphumulako a banja la a Dani, anachokera ku Zora, ndi ku Esitaoli. 12Nakwera namanga misasa m'Kiriyati-Yearimu, m'Yuda; chifukwa chake anatcha dzina lake la malowo chigono cha Dani, mpaka lero; taona, ali m'tseri mwa Kiriyati-Yearimu. 13Ndipo anapitirira komweko kunka ku mapiri a Efuremu, nadza kunyumba ya Mika. 14Pamenepo anayankha amuna asanu anamukawo kukazonda dziko la Laisi, nanena ndi abale ao, Kodi mudziwa kuti m'nyumba izi muli chovala cha wansembe, ndi timafano ndi fano losema, ndi fano lonyenga? Ndipo tsopano dziwani choyenera inu kuchita. 15Napatuka iwo kumkako, nafika kunyumba ya mnyamata Mleviyo, ndiyo nyumba ya Mika, namfunsa ngati ali bwanji. 16Ndipo amuna mazana asanu ndi limodzi omangira zida zao za nkhondo m'chuuno, ndiwo a ana a Dani, analikuima polowera pa chipata; 17#Ower. 18.2koma amuna asanu omukawo kukazonda dziko anakwera analowako, natenga fano losema, ndi chovala cha wansembe ndi timafano, ndi fano loyenga; ndi wansembe anaima polowera pa chipata pamodzi ndi amuna mazana asanu ndi limodzi omangira zida za nkhondo m'chuuno. 18#Ower. 17.4-5Atalowa iwo m'nyumba ya Mika, natengako fano losema, chovala cha wansembe, ndi timafano, ndi fano loyenga, wansembeyo ananena nao, Muchitanji? 19#Ower. 17.10Ndipo ananena naye, Khala chete, tseka pakamwa pako, numuke nafe, nutikhalire atate ndi wansembe wathu; chikukomera nchiti, kukhala wansembe wa nyumba ya munthu mmodzi, kapena kukhala wansembe wa fuko ndi banja m'Israele? 20Nukondwera mtima wa wansembeyo, natenga iye chovala cha wansembe, ndi timafano ndi fano losema, nalowa pakati pa anthu. 21Atatero anabwerera, nachoka, natsogoza ana ang'ono ndi zoweta ndi akatundu. 22Atafika kutali ndi nyumba ya Mika, Mikayo anawamemeza amuna a m'nyumba zoyandikizana ndi yake, natsata ndi kuwapeza ana a Dani. 23Ndipo anafuula kwa ana a Dani. Nacheuka iwo nati kwa Mika, Chakusowa chiyani, kuti wamemeza anthu ako? 24#Gen. 31.30Nati iye, Mwanditengera milungu yanga ndinaipanga, ndi wansembe, ndi kuchoka; chinditsaliranso chiyani? Ndipo muneneranji kwa ine, Chakusowa nchiyani? 25Koma ana a Dani anati kwa iye, Mau ako asamveke ndi ife, angakugwere anthu owawa mtima, nukataya moyo wako ndi wa iwo a m'nyumba mwako. 26Nayenda ulendo wao ana a Dani; ndipo Mika pakuona kuti anamposa mphamvu, anatembenuka nabwerera kunyumba kwake. 27#Ower. 18.7, 10M'mwemo anatenga zimene Mika adachipanga, ndi wansembe anali naye, nafika ku Laisi, kwa anthu odekha ndi okhazikika mtima, nawakantha ndi lupanga lakuthwa, natentha mudzi wao ndi moto. 28Ndipo panalibe wolanditsa, popeza ku Sidoni nkutali, ndipo analibe kuyenderana ndi anthu ena; ndiko ku chigwa chokhala ku Beterehobu. Pamenepo anamanganso mudziwo, nakhala m'mwemo. 29#Ower. 18.7Ndipo analitcha dzina la mudziwo Dani, kutsata dzina la atate wao Dani wombala Israele; koma poyambapo dzina la mudzi linali Laisi. 30Ndipo ana a Dani anadziimitsira fano losemalo; ndi Yonatani mwana wa Geresomo mwana wa Manase, iye ndi ana ake amuna anali ansembe a fuko la Adani mpaka tsiku lija anatenga ndende anthu a m'dziko. 31#Yos. 18.1Motero anadziikira fano losema la Mika, limene adalipanga, masiku onse okhala nyumba ya Mulungu ku Silo.

Currently Selected:

OWERUZA 18: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for OWERUZA 18