YouVersion Logo
Search Icon

HOSEYA 10

10
1 # Mas. 80.8-11 Israele ndi mpesa wotambalala, wodzibalira wokha zipatso; monga umo zinachulukira zipatso zake, momwemo anachulukitsa maguwa a nsembe ake; monga mwa kukoma kwake kwa dziko lake anapanga zoimiritsa zokoma. 2#1Maf. 18.21; Mat. 6.24Mtima wao wagawikana, tsopano adzapezeka opalamula, adzapasula maguwa ao a nsembe, nadzaononga zoimiritsa zao. 3Pakuti tsopano adzati, Tilibe mfumu, popeza sitiopa Yehova; ndi mfumu idzatichitira chiyani? 4Anena mau akulumbira monama, pakuchita mapangano momwemo; chiweruzo chiphuka ngati zitsamba zowawa m'michera ya munda. 5Okhala m'Samariya adzaopera chifanizo cha anaang'ombe a ku Betaveni; pakuti anthu ake adzamva nacho chisoni, ndi ansembe ake amene anakondwera nacho, chifukwa cha ulemerero wake, popeza unachichokera. 6Adzachitengeranso ku Asiriya chikhale mphatso ya kwa mfumu Yarebu; Efuremu adzatenga manyazi, ndi Israele adzachita manyazi ndi uphungu wake. 7Ndipo Samariya, mfumu yake yamwelera ngati thovu pamadzi. 8#Yes. 2.19; Luk. 23.30Ndipo misanje ya Aveni, ndiyo tchimo la Israele, idzaonongeka; minga ndi mitungwi idzamera pa maguwa ao a nsembe; ndipo adzati kwa mapiri, Tiphimbeni; ndi kwa zitunda, Tigwereni. 9#Hos. 9.9Israele, wachimwa kuyambira masiku a Gibea; pomwepo anaimabe; nkhondo ya ana a chosalungama siinawapeza ku Gibea. 10Pamene ndifuna ndidzawalanga, ndi mitundu ya anthu idzawasonkhanira pomangidwa iwo pa zolakwa zao ziwiri. 11Ndipo Efuremu ndiye ng'ombe yaikazi yaing'ono, yozereweredwa, yokonda kupuntha tirigu; koma ndapita pa khosi lake lokoma; ndidzamsenzetsa Efuremu goli; Yuda adzalima, Yakobo adzaphwanya chibuluma chake. 12#Miy. 11.18; Yer. 4.3Mudzibzalire m'chilungamo mukolole monga mwa chifundo; limani masala anu, pakuti yafika nthawi ya kufuna Yehova, mpaka afika Iye, navumbitsira inu chilungamo. 13#Miy. 22.8; Agal. 6.7-8Mwalima choipa, mwakolola chosalungama, mwadya zipatso za mabodza; pakuti watama njira yako ndi kuchuluka kwa anthu ako amphamvu. 14#2Maf. 17.3; Hos. 13.16Momwemo phokoso lidzaukira anthu ako, ndi malinga ako onse adzapasuka, monga Salimani anapasula Betaribele; tsiku la nkhondo amai anaphwanyika pamodzi ndi ana ake. 15Momwemo adzakuchitirani Betele, chifukwa cha choipa chanu chachikulu; mbandakucha mfumu ya Israele idzalikhika konse.

Currently Selected:

HOSEYA 10: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in