GENESIS 40
40
Yosefe m'kaidi amasulira maloto
1 #
Neh. 1.11
Ndipo panali zitapita izi, wopereka chikho wa mfumu ya Aejipito ndi wophika mkate wake anamchimwira mbuye wao mfumu ya Aejipito. 2Ndipo Farao anakwiyira akulu ake awiriwo wamkulu wa opereka chikho, ndi wamkulu wa ophika mkate. 3Ndipo anaika iwo asungidwe m'nyumba ya kazembe wa alonda, m'kaidi, umo anamangidwa Yosefe. 4Ndipo kazembe wa alonda anapereka iwo kwa Yosefe, ndipo iye anawatumikira iwo: ndipo anakhala nthawi mosungidwamo. 5Ndipo analota maloto onse awiri, yense loto lake, usiku umodzi, yense monga mwa kumasulira kwa loto lake, wopereka chikho ndi wophika mkate wa mfumu ya Aejipito, amene anamangidwa m'kaidi. 6Ndipo Yosefe analowa kwa iwo m'mawa, nawaona iwo, taonani, anali oziya. 7#Neh. 2.2Ndipo anafunsa akulu a Farao osungidwa naye m'nyumba ya mbuyake, kuti, Nkhope zanu zagwa bwanji lero? 8Ndipo iwo anati kwa iye, Ife talota maloto, ndipo tilibe wotimasulira. Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Kodi Mwini kumasulira si ndiye Mulungu? Mundifotokozeretu. 9Ndipo wopereka chikho wamkulu anafotokozera Yosefe loto lake, nati kwa iye, M'kulota kwanga, taona, mpesa unali pamaso panga: 10ndipo m'mpesamo munali nthambi zitatu: ndipo unali wonga unaphuka, ndipo maluwa ake anaphuka; nabala matsamvu ake mphesa zakucha; 11ndipo chikho cha Farao chinali m'dzanja langa: ndipo ndinatenga mphesa, ndi kufinyira m'chikho cha Farao ndi kupereka chikho m'dzanja la Farao. 12#Dan. 2.36Ndipo Yosefe anati kwa iye, Kumasulira kwake ndi uwu: nthambi zitatu ndizo masiku atatu; 13#2Maf. 25.27akali masiku atatu Farao adzatukula mutu wako, nadzabwezera iwe ntchito yako; ndipo udzapereka chikho cha Farao m'dzanja lake, monga kale lomwe m'mene unali wopereka chikho chake. 14Koma undikumbukire ine m'mene kudzakhala bwino ndi iwe, ndipo undichitiretu ine kukoma mtima: nunditchule ine kwa Farao, nunditulutse ine m'nyumbamu: 15chifukwa kuti ndinabedwa ndithu m'dziko la Ahebri; ndiponso pano sindinachite kanthu kakundiikira ine m'dzenjemu. 16Pamene wophika mkate anaona kuti kumasulira kwake kunali kwabwino, iye anati kwa Yosefe, Inenso ndinalimkulota, ndipo, taonani, malichero atatu a mikate yoyera anali pamtu panga; 17m'lichero lapamwamba munali mikate ya Farao ya mitundumitundu; ndipo mbalame zinadya ya m'lichero la pamutu panga. 18Ndipo Yosefe anayankha nati, Kumasulira kwake ndi uku: malichero atatu ndiwo masiku atatu; 19akali masiku atatu Farao adzakweza mutu wako ndi kuuchotsa, nadzakupachika iwe pamtengo: ndipo mbalame zidzadya mnofu wako. 20#Mrk. 6.21Ndipo panali tsiku lachitatu ndilo tsiku lakubadwa kwake kwa Farao, iye anakonzera anyamata ake madyerero, ndipo anakweza mutu wa wopereka chikho wamkulu ndi mutu wa wophika mkate wamkulu pakati pa anyamata ake. 21Ndipo anabwezanso wopereka chikho ku ntchito yake; ndipo iye anapereka chikho m'manja a Farao. 22Koma anampachika wophika mkate wamkulu; monga Yosefe anawamasulira. 23Koma wopereka chikho wamkulu sanakumbukire Yosefe, koma anamuiwala.
Currently Selected:
GENESIS 40: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi