GENESIS 34
34
Dina ndi a Sekemu
1Ndipo Dina mwana wamkazi wa Leya, amene anambalira Yakobo, ananka kukaona akazi a kumeneko. 2Pamene anamuona iye Sekemu, mwana wake wamwamuna wa Hamori Muhivi, kalonga wa dzikolo, anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa. 3Ndipo mtima wake unakhumba Dina mwana wake wamkazi wa Yakobo, ndipo anamkonda namwaliyo, nanena momkopa namwaliyo. 4Ndipo anati Sekemu kwa atate wake Hamori kuti, Munditengere ine mkazi uyo akhale mkazi wanga. 5Ndipo anamva Yakobo kuti anamuipitsa Dina, mwana wake wamkazi; ana ake amuna anali ndi zoweta zake kudambo: ndipo Yakobo anakhala chete mpaka anafika iwo. 6Ndipo Hamori atate wake wa Sekemu anatuluka kunka kwa Yakobo kukanena ndi iye. 7Ndipo pakumva icho ana ake amuna a Yakobo anabwera pochokera kudambo: amunawo ndipo anapwetekwa mtima, nakwiya kwambiri, chifukwa iyeyo anachita chopusa choipira Israele pakugona ndi mwana wamkazi wa Yakobo; ndicho chosayenera kuchita. 8Ndipo Hamori ananena ndi iwo, kuti, Mtima wa Sekemu mwana wanga umkhumba mwana wako wamkazi: umpatsetu kuti akhale mkazi wake. 9Mukwatirane ndi ife: tipatseni ife ana anu akazi, ndiponso dzitengereni ana athu akazi. 10Ndipo mudzakhala pamodzi ndi ife, dziko lidzakhala pamaso panu; khalani m'menemo ndi kuchita malonda, ndi kukhala nazo zanuzanu m'menemo. 11Ndipo Sekemu anati kwa atate wake wa mkazi ndi kwa abale ake, Tipeze ufulu pamaso panu, chimene mudzanena kwa ine ndidzapereka. 12#Eks. 22.16Mundipemphe ine za mitulo ndi zaulere zambirimbiri, ndipo ndidzapereka monga mudzanena kwa ine; koma mundipatse ine namwaliyo akhale mkazi wanga. 13Ndipo ana ake amuna a Yakobo anayankha Sekemu ndi Hamori atate wake monyenga, nanena, popeza anamuipitsa Dina mlongo wao, 14#Yos. 5.9nati kwa iwo, Sitingathe kuchita ichi, kupereka mlongo wathu kwa mwamuna wosadulidwa; chifukwa kumeneko ndiko kutichepetsa ife. 15Koma apa pokha tidzakuvomerezani: ngati mudzakhala onga ife ndi kudulidwa amuna onse; 16pamenepo tidzakupatsani inu ana athu akazi, ndipo tidzadzitengera ana anu akazi, ndipo tidzakhala pamodzi ndi inu, ndi kukhala mtundu umodzi. 17Koma mukapanda kutimvera ndi kusadulidwa, pamenepo tidzatenga mwana wathu wamkazi, ndi kumuka naye. 18Mau ao ndipo anakomera Hamori ndi Sekemu mwana wake wa Hamori. 19#1Mbi. 4.9Ndipo mnyamatayo sanachedwe kuchichita popeza anakondwera ndi mwana wake wamkazi wa Yakobo; ndipo iye anali wolemekezedwa woposa onse a pa banga la atate wake. 20#Gen. 32.7, 24Ndipo Hamori ndi Sekemu mwana wake anafika ku chipata cha mudzi wao, nalankhulana ndi anthu a mudzi wao, kuti, 21Anthu amenewa ali amtendere pamodzi ndi ife; chifukwa chake akhale m'dzikomo, achite malonda m'menemo: pakuti taonani dzikolo lili lalikulu lokwanira iwo; tidzitengere ana ao akazi akhale akazi athu, tiwapatse amenewa ana athu akazi. 22Anthuwo adzatiloleza ife tikhale nao anthu amodzi, pokhapo amuna onse a mwa ife adzadulidwa, monga iwo adulidwa. 23Kodi ng'ombe zao ndi chuma chao ndi zoweta zao sizidzakhala zathu? Pokhapo tivomerezana nao ndipo adzakhala pamodzi ndi ife. 24Ndipo onse amene anatuluka pa chipata cha mudzi wao anamvera Hamori ndi mwana wake Sekemu, nadulidwa amuna onse akutuluka pa chipata cha mudzi wao. 25Ndipo panali tsiku lachitatu pamene anamva kuwawa, ana amuna awiri a Yakobo, Simeoni ndi Levi, abale ake a Dina, anatenga wina lupanga lake wina lake, nalimbika mtima nalowa m'mudzi napha amuna onse. 26Ndipo anapha Hamori ndi Sekemu mwana wake ndi lupanga, natulutsa Dina m'nyumba ya Sekemu nachoka naye. 27Ndipo ana amuna a Yakobo anadza kwa ophedwa nafunkha mudzi chifukwa anamuipitsa mlongo wao. 28Ndipo analanda nkhosa zao ndi zoweta zao ndi abulu ao, ndi za m'mudzi, ndi za m'munda; 29ndi chuma chao chonse ndi ana ao ndi akazi ao anawagwira, nafunkha zonse za m'nyumba. 30Ndipo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, Mwandisautsa ndi kundinukhitsa ine mwa anthu okhala m'dzikomu, mwa Akanani ndi mwa Aperizi; ndipo ine ndine wa anthu owerengeka, adzandisonkhanira ine ndi kundikantha: ndipo ndidzapasulidwa ine ndi a pa nyumba yanga. 31Ndipo iwo anati, Kodi iye ayenera kusandutsa mlongo wathu wadama?
Currently Selected:
GENESIS 34: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi