GENESIS 26
26
Isaki akhala kwa Afilisti
1 #
Gen. 12.10
Ndipo panali njala padzikopo, yoyenjezeka ndi njala yoyamba ija imene inali masiku a Abrahamu, ndipo Isaki ananka kwa Abimeleki mfumu ya Afilisti ku Gerari. 2Ndipo Yehova anamuonekera iye nati, Usatsikire ku Ejipito, khala m'dziko m'mene ndidzakuuza iwe; 3#Gen. 13.15khala mlendo m'dziko muno, ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndipo ndidzadalitsa iwe chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako maiko onse awa, ndipo ndidzalimbikitsa chilumbiriro ndinachilumbirira kwa Abrahamu atate wako; 4#Gen. 12.3ndipo ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, ndipo ndidzapatsa mbeu zako maiko onsewa; m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa; 5#Gen. 22.18chifukwa kuti Abrahamu anamvera mau anga, nasunga chilangizo changa, ndi maweruziro anga, ndi malemba anga ndi malamulo anga. 6Ndipo Isaki anakhala m'Gerari; 7#Gen. 20.2ndipo anthu a kumeneko anamfunsa iye za mkazi wake; ndipo iye anati, Ndiye mlongo wanga: chifukwa kuti anaopa kunena, Mkazi wanga; anati, anthu a kumeneko angandiphe ine chifukwa cha Rebeka; popeza anali wokongola pakumuona. 8Ndipo panali atakhala komwe masiku ambiri, Abimeleki mfumu ya Afilisti, anayang'ana kunja kwa zenera, napenya, taona, Isaki analinkuseka ndi Rebeka mkazi wake. 9Ndipo Abimeleki anamuitana Isaki nati, Taona, uyo ndi mkazi wako ndithu: kodi bwanji unati, Ndiye mlongo wanga? Ndipo Isaki anati kwa iye, Chifukwa ndinati, Ndingafe chifukwa cha iye. 10Ndipo Abimeleki anati, Nchiyani chimenechi watichitira ife? Panatsala pang'ono ena a anthu akadagona naye mkazi wako, ndipo ukadatichimwitsa ife. 11Ndipo Abimeleki anauza anthu ake, nati, Aliyense amene akhudza mwamuna uyo kapena mkazi wake, zoonatu adzaphedwa. 12Ndipo Isaki anabzala m'dzikomo, nalandira za makumi khumi chaka chimenecho; ndipo Yehova anamdalitsa iye. 13Ndipo analemera munthuyo, nalemera ndithu kufikira kuti anakhala wolemera kwambiri: 14ndipo anali ndi chuma cha nkhosa, ndi chuma cha zoweta, ndi banja lalikulu: ndipo Afilisti anamchitira iye nsanje. 15#Gen. 21.30Ndipo zitsime zonse anakumba anyamata a atate wake, Abrahamuyo akali moyo, Afilisti anazitseka, nazikwirira ndi dothi. 16Ndipo Abimeleki anati kwa Isaki, Uchoke kwa ife chifukwa kuti iwe uli wamphamvu wopambana ife. 17Ndipo Isaki anachoka kumeneko, namanga hema wake m'chigwa cha Gerari, nakhala kumeneko. 18Ndipo Isaki anafukulanso zitsime za madzi, anazikumba masiku a Abrahamu atate wake; chifukwa kuti Afilisti anazitseka atafa Abrahamu: ndipo anazitcha maina monga maina omwe anazitcha atate wake. 19Ndipo anyamata a Isaki anakumba m'chigwa, napeza kumeneko chitsime cha madzi otumphuka. 20Ndipo abusa a Gerari anakangana ndi abusa a Isaki kuti, Madzi ndi athu; ndipo anatcha dzina la chitsimecho Eseke: chifukwa anakangana naye. 21Ndipo anakumbanso chitsime china, ndipo anakangana nachonso; natcha dzina lake Sitina. 22Ndipo anachoka kumeneko nakumba chitsime china; koma sanakangane nacho chimenecho; ndipo anatcha dzina lake Rehoboti; ndipo anati, Chifukwa kuti tsopano Yehova anatipatsa ife malo, ndipo tidzabalana m'dziko muno. 23Ndipo anachoka kumeneko nakwera kunka ku Beereseba. 24#Gen. 15.1Ndipo Yehova anamuonekera iye usiku womwewo, nati, Ine ndine Mulungu wa Abrahamu atate wako; usaope, chifukwa kuti Ine ndili ndi iwe, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kuchulukitsa mbeu zako, chifukwa cha Abrahamu kapolo wanga. 25#Gen. 12.7Ndipo anamanga kumeneko guwa la nsembe, naitana dzina la Yehova, namanga hema wake kumeneko: ndi pamenepo anyamata a Isaki anakumba chitsime.
Isaki apangana ndi Abimeleki
26Ndipo ananka kwa iye Abimeleki kuchokera ku Gerari, ndi Ahuzati bwenzi lake, ndi Fikolo, kazembe wa nkhondo yake. 27Ndipo Isaki anati kwa iwo, Mwandidzera chifukwa chiyani, inu akundida ine, ndi kundichotsa kwanu? 28Ndipo iwo anati, Kuona tinaona kuti Yehova ali ndi iwe; ndipo tinati, Tilumbiriranetu tonse awiri, ife ndi iwe, tichite pangano ndi iwe; 29kuti usatichitire ife zoipa, pakuti sitidakhudza iwe, sitidakuchitira kanthu koma kabwino ndiko, ndipo takulola umuke ndi mtendere; ndiwe tsopano wodalitsidwa ndi Yehova. 30Ndipo anakonzera iwo madyerero, ndipo anadya namwa. 31Ndipo analawira m'mamawa nalumbirirana wina ndi mnzake; ndipo Isaki anawalola amuke, ndipo anauka kuchokera kwa iye m'mtendere. 32Ndipo panali tsiku lomwelo anyamata ake a Isaki anadza namuuza iye za chitsime chimene anakumba, nati kwa iye, Tapeza madzi. 33Ndipo anatcha dzina lake Siba, chifukwa chake dzina la mudziwo ndi Beereseba kufikira lero lino.
34Pamene Esau anali wa zaka makumi anai, anakwatira Yuditi mwana wamkazi wa Beeri Muhiti, ndi Basemati mwana wamkazi wa Eloni Muhiti: 35#Gen. 27.46ndipo iwo anapweteka mtima wa Isaki ndi wa Rebeka.
Currently Selected:
GENESIS 26: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi