GENESIS 14
14
Abramu alanditsa Loti
1Ndipo panali masiku a Amurafere mfumu ya Sinara, ndi Ariyoki mfumu ya Elasara, ndi Kedorilaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu, 2iwo anathira nkhondo pa Bera mfumu ya Sodomu, ndi pa Birisa, mfumu ya Gomora, ndi pa Sinabe mfumu ya Adima, ndi pa Semebera mfumu ya Zeboimu, ndi pa mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zowari). 3Onse amenewo anadziphatikana pa chigwa cha Sidimu (pamenepo ndi pa Nyanja ya Mchere). 4Zaka khumi ndi ziwiri iwo anamtumikira Kedorilaomere, chaka chakhumi ndi chitatu anapanduka. 5Chaka chakhumi ndi chinai ndipo anadza Kedorilaomere ndi mafumu amene anali naye, nawakantha Arefaimu m'Asiteroti-Karanaimu, ndi Azuzimu m'Hamu, ndi Aemimu m'Savekiriyataimu, 6ndi Ahori pa phiri lao Seiri kufikira ku Eliparani, kumene kuli m'mbali mwa chipululu. 7Ndipo anabwera nafika ku Enimisipati (kumeneko ndi ku Kadesi), nakantha dziko lonse la Aamaleke, ndiponso Aamori amene akhala m'Hazazoni-Tamara. 8Ndipo anatuluka mfumu ya Sodomu, ndi ya Gomora, ndi mfumu ya Adima, ndi mfumu ya Zeboimu, ndi mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zowari) ndipo anawathira nkhondo m'chigwa cha Sidimu; 9ndi Kedorilaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu, ndi Amurafere mfumu ya Sinara, ndi Ariyoki mfumu ya Elasara; mafumu anai kugwirana ndi asanu. 10Chigwa cha Sidimu chinali ndi zitengetenge thoo; ndipo anathawa mafumu a ku Sodomu ndi Gomora nagwa m'menemo: amene anatsala anathawira kuphiri. 11Ndipo anatenga chuma chonse cha Sodomu ndi Gomora ndi zakudya zao zonse, namuka. 12Ndipo anagwira Loti mwana wa Abramu amene anakhala m'Sodomu, ndi chuma chake, namuka. 13Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Muhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure Mwamori, mkulu wake wa Esikolo, ndi mkulu wake wa Anere; amenewo ndiwo opangana naye Abramu. 14Pamene anamva Abramu kuti mphwake anagwidwa, anatuluka natsogolera anyamata ake opangika, obadwa kunyumba kwake, mazana atatu kudza khumi ndi asanu ndi atatu, nawalondola kufikira ku Dani. 15Ndipo anadzigawanizira iwo usiku, iye ndi anyamata ake, nawakantha, nawapirikitsa kufikira ku Hoba, ndiko ku dzanja lamanzere la ku Damasiko. 16Ndipo anabwera nacho chuma chonse, nabwera naye Loti yemwe ndi chuma chake, ndi akazi ndi anthu omwe.
Melkizedeki adalitsa Abramu
17Ndipo anatuluka mfumu ya Sodomu kukomana naye, atabwera anatha kuwakantha Kedorilaomere ndi mafumu amene anali naye, ku chigwa cha Save (ndiko ku chigwa cha mfumu), 18#Aheb. 7.1Ndipo Melkizedeki mfumu ya ku Salemu, anatuluka nao mkate ndi vinyo: iye ndiye wansembe wa Mulungu Wamkulukulu. 19Ndipo anamdalitsa iye, nati, Abramu adalitsike ndi Mulungu Wamkulukulu, mwini kumwamba ndi dziko lapansi; 20ayamikike Mulungu Wamkulukulu amene wapereka adani ako m'dzanja lako. Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse. 21Mfumu ya Sodomu ndipo inati kwa Abramu, Ndipatse ine anthu, nutenge chuma iwe wekha. 22#Eks. 6.8; Num. 14.30Ndipo Abramu anati kwa mfumu ya Sodomu, Dzanja langa ndamtukulira Yehova, Mulungu Wamkulukulu, mwini kumwamba ndi dziko lapansi 23kuti sindidzatenga ngakhale thonje ngakhale chingwe cha nsapato, ngakhale kanthu kalikonse kako, kuti unganene, Ndamlemeza Abramu; 24koma chokhachi anadya anyamata, ndi gawo lao la anthu amene ananka pamodzi ndi ine, Anere, Esikolo, ndi Mamure, iwo atenge gawo lao.
Currently Selected:
GENESIS 14: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi