EZARA Mau Oyamba
Mau Oyamba
Nkhani imene ili mu buku la Ezara ikutsatana ndi nkhani za m'mabuku awiri a Mbiri, ndipo ikulongosola za kubwerera kwa ena mwa Ayuda kuchokera ku Babiloni kumene anatengedwa ngati akapolo. Bukuli likufotokozanso za kubwezeretsedwa kwa moyo ndi chipembedzo mu Yerusalemu. Nkhanizi zaperekedwa m'magawo atatu: Gawo loyamba ndi la gulu la Ayuda amene anabwerera kuchokera ku Babiloni potsatira lamulo limene adapereka Kirusi amene anali mfumu ya Persiya. Gawo lachiwiri likunena za kumangidwanso ndi kupatulidwa kwa Kachisi komanso za kukonzedwanso kwa chipembedzo cha Mulungu ku Yerusalemu. Gawo lachitatu likunena gulu lina la Ayuda amene anabwerera ku Yerusalemu motsogozedwa ndi Ezara, amene anali katswiri pa Malamulo a Mulungu, ndipo iye anawathandiza anthu kuti akonzenso chikhalidwe ndi moyo wa chipembedzo pofuna kusunga miyambo ya chipembedzo mu Israele.
Za mkatimu
Gulu loyamba la anthu libwerera 1.1—2.70
Kachisi amangidwanso napatulidwa 3.1—6.22
Ezara abwerera ndi anthu ena7.1—10.44
Currently Selected:
EZARA Mau Oyamba: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi