EZEKIELE 4
4
Aneneratu mophiphiritsa za kumangidwa misasa Yerusalemu
1Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, dzitengere njerwa, nuiike pamaso pako, nulembepo mudzi, ndiwo Yerusalemu; 2nuuzinge, nuumangire nsanja zouzinga, nuundire nthumbira, ndi kuumangira misasa, nuuikire zogumulira pozungulira pake. 3Nudzitengere chiwaya chachitsulo, ndi kuchiika ngati khoma lachitsulo pakati pa iwe ndi mudziwo; nuulozetsere nkhope yako kuti umangidwire misasa, ndipo udzamangira misasa. Ichi chikhale chizindikiro cha nyumba ya Israele.
4 #
Num. 14.34
Ndipo iwe ugonere pansi mbali yako ya kumanzere, nuikepo mphulupulu ya nyumba ya Israele; monga mwa kuwerenga kwa masiku amene udzagonapo udzasenza mphulupulu yao. 5#Num. 14.34Ndipo Ine ndakuikira zaka za mphulupulu yao ngati masiku, ndiwo masiku mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai, kuti usenze mphulupulu ya nyumba ya Israele. 6Ndipo utatsiriza awa, ugonerenso mbali yako ya kumanja, ndi kusenza mphulupulu ya nyumba ya Yuda; ndakuikira masiku makumi anai, kuliyesa tsiku limodzi ngati chaka chimodzi. 7Ndipo ulozetse nkhope yako kuzingidwa kwake kwa Yerusalemu, ndi dzanja lako losafundika, nuunenere. 8#Ezk. 3.25Ndipo taona ndidzakumanga ndi zingwe zolimba kuti usakunkhulire, mpaka watsiriza masiku a kuzingidwa kwako. 9Udzitengerenso tirigu, ndi barele, ndi nyemba, ndi mphodza, ndi mapira, ndi mawere, nuziike m'mbale imodzi, ndi kudzipangira mkate nazo; uzidyako monga mwa kuwerenga kwa masiku udzagonawo pambali pako, ndiwo masiku mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai, 10Ndipo chakudya chako uzichidya chiyesedwe masekeli makumi awiri tsiku limodzi; uzidyako tsiku ndi tsiku pa nthawi yake. 11Uzimwanso madzi monga mwa muyeso, limodzi la magawo asanu ndi limodzi la hini; uzimwako tsiku ndi tsiku pa nthawi yake. 12Ndipo uzichidya ngati timikate ta barele, ndi kutiocha pamaso pao ndi zonyansa za munthu. 13#Hos. 9.3Ndipo Yehova anati, Motero ana a Israele adzadya chakudya chao chodetsedwa, mwa amitundu kumene ndidzawaingitsirako. 14#Mac. 10.14Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Taonani, moyo wanga sunadetsedwa, pakuti chiyambire ubwana wanga mpaka tsopano sindinadye chinthu chakufa chokha, kapena chogwidwa ndi chilombo; simunalowanso m'kamwa mwanga nyama yonyansa. 15Ndipo anati kwa ine, Taona ndakuninkha ndowe ya ng'ombe m'malo mwa zonyansa za munthu, uotche mkate wako pamenepo. 16#Lev. 26.26; Mas. 105.16Nanenanso nane, Wobadwa ndi munthu iwe, taona, ndidzathyola mchirikizo, ndiwo chakudya, m'Yerusalemu; ndipo adzadya chakudyacho monga mwa muyeso, ndi mosamalira, nadzamwa madzi monga mwa muyeso, ndi kudabwa; 17#Lev. 26.39kuti asowe chakudya ndi madzi, nasumwesumwe, naondetse mu mphulupulu zao.
Currently Selected:
EZEKIELE 4: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi