YouVersion Logo
Search Icon

EKSODO 19

19
Mulungu alamulira anthu za ku Sinai
1Mwezi wachitatu atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito, tsiku lomwelo, analowa m'chipululu cha Sinai. 2#Eks. 3.1Pakuti anachoka ku Refidimu, nalowa m'chipululu cha Sinai, namanga tsasa m'chipululumo; ndipo Israele anamanga tsasa pamenepo pandunji pa phirilo. 3#Mac. 7.38Ndipo Mose anakwera kwa Mulungu; ndipo Yehova ali m'phirimo anamuitana, ndi kuti, Uzitero kwa mbumba ya Yakobo, nunene kwa ana a Israele, kuti, 4#Yes. 63.9; Deut. 32.11Inu munaona chimene ndinachitira Aejipito; ndi kuti ndanyamula inu monga pa mapiko a mphungu, ndi kubwera nanu kwa Ine ndekha. 5#Mas. 24.1; Mala. 3.17; Tit. 2.14Ndipo tsopano, ngati mudzamvera mau anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa cha padera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa; 6#1Pet. 2.5, 9ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika. Awa ndi mau amene ukalankhule ndi ana a Israele. 7Ndipo Mose anadza, naitana akulu a anthu, nawaikira pamaso pao mau awa onse amene Yehova adamuuza. 8#Eks. 24.3, 7Ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita. Ndipo Mose anabwera nao mau a anthu kwa Yehova. 9Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndikudza kwa iwe mu mtambo wakuda bii, kuti anthu amve pamene ndilankhula ndi iwe, ndi kuti akuvomereze nthawi zonse. Pakuti Mose adauza Yehova mau a anthuwo. 10#Aheb. 10.22Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka kwa anthuwo, nuwapatulitse lero ndi mawa, ndipo atsuke zovala zao. 11Nakonzekeretu tsiku lachitatu; pakuti tsiku lachitatu Yehova adzatsika pa phiri la Sinai pamaso pa anthu onse. 12#Aheb. 12.18, 20Ndipo ukalembere anthu malire pozungulira, ndi kuti, Muzichenjera musakwere m'phiri, musakhudza chilekezero chake; wokhudza phirilo adzaphedwa ndithu; 13dzanja lililonse lisalikhudze, wakulikhudza azimponyatu miyala, kapena kumpyoza; ngakhale choweta ngakhale munthu, zisakhale ndi moyo. Pamene lipenga libanika liu lake azikwera m'phirimo. 14Ndipo Mose anatsika m'phiri kunka kwa anthu, nawapatulitsa anthu; natsuka iwo zovala zao. 15Ndipo anati kwa anthu, Mukonzekeretu tsiku lachitatu nimusayandikiza mkazi. 16Ndipo kunali tsiku lachitatu, m'mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera. 17Ndipo Mose anatulutsa anthu kutsasa, kuti akomane ndi Mulungu; ndipo anaima patsinde pa phiri. 18#Mas. 68.8Ndipo phiri la Sinai linafuka monsemo, popeza Yehova anatsikira m'moto pamenepo; ndi utsi wake unakwera ngati utsi wa m'ng'anjo, ndi phiri lonse linagwedezeka kwambiri. 19Ndipo pamene liu la lipenga linamveka linakulirakulira, Mose ananena, ndi Mulungu anamyankha ndi mau. 20Ndipo Yehova anatsikira pa phiri la Sinai, pamutu pake pa phiri; ndipo Yehova anaitana Mose akwere pamutu pa phiri; ndi Mose anakwerapo. 21Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tsika, chenjeza anthu, kuti angapyolere kwa Yehova kudzaona, ndipo angagwe ambiri a iwowa. 22Ansembenso, akuyandikiza kwa Yehova adzipatulitse, angawapasule Yehova. 23Ndipo Mose anati kwa Yehova, Anthu sangathe kukwera m'phiri la Sinai; pakuti Inu mwatichenjeza, ndi kuti, Lemba malire m'phirimo, ndi kulipatula. 24Ndipo Yehova anati kwa iye, Muka, tsika; nukwere iwe ndi Aroni pamodzi ndi iwe; koma ansembe ndi anthu asapyole kukwera kwa Yehova, angawapasule. 25Pamenepo Mose anawatsikira anthu, nanena nao.

Currently Selected:

EKSODO 19: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in