ESTERE 3
3
Mordekai akana kugwadira Hamani
1 #
Num. 24.7; 1Sam. 15.8 Zitatha izi, mfumu Ahasuwero anamkuza Hamani mwana wa Hamedata, wa ku Agagi, namkweza, naika mpando wake upose akalonga onse okhala naye. 2#Est. 2.19Ndipo anyamata onse a mfumu okhala m'chipata cha mfumu anamweramira, namgwadira Hamani; pakuti mfumu idalamulira chotero za iye. Koma Mordekai sanamweramire kapena kumgwadira. 3Ndipo anyamata a mfumu okhala m'chipata cha mfumu anati kwa Mordekai, Ulakwiranji pa lamulo la mfumu? 4Kunali tsono, pomalankhula naye tsiku ndi tsiku, osawamvera iye, anauza Hamani, kuona ngati mlandu wa Mordekai udzakoma; popeza iye adawauza kuti ali Myuda. 5#Est. 5.9Ndipo Hamani, pakuona kuti Mordekai sanamweramire kapena kumgwadira, mtima wake unadzala mkwiyo. 6#Mas. 83.4Koma anachiyesa chopepuka kumthira manja Mordekai yekha; pakuti adamfotokozera mtundu wake wa Mordekai; potero Hamani anafuna kuononga Ayuda onse okhala m'ufumu wonse wa Ahasuwero, ndiwo a mtundu wa Mordekai.
Hamani apangira mfumu kuti uphedwe mtundu wonse wa Ayuda
7 #
Est. 9.24
Mwezi woyamba ndiwo mwezi wa Nisani, chaka chakhumi ndi chiwiri cha mfumu Ahasuwero, anaombeza Puri, ndiwo ula, pamaso pa Hamani tsiku ndi tsiku, mwezi ndi mwezi, mpaka mwezi wakhumi ndi chiwiri, ndiwo mwezi wa Adara. 8#Ezr. 4.13; Mac. 16.20Ndipo Hamani anati kwa mfumu Ahasuwero, Pali mtundu wina wa anthu obalalika ndi ogawanikana mwa mitundu ya anthu m'maiko onse a ufumu wanu, ndi malamulo ao asiyana nao a anthu onse, ndipo sasunga malamulo a mfumu; chifukwa chake mfumu siiyenera kuwaleka. 9Chikakomera mfumu, chilembedwe kuti aonongeke iwo; ndipo ndidzapereka matalente a siliva zikwi khumi m'manja a iwo akusunga ntchito ya mfumu, abwere nao kuwaika m'nyumba za chuma cha mfumu. 10#Gen. 41.42Ndipo mfumu inavula mphete yake pa chala chake, naipereka kwa Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, mdani wa Ayuda. 11Ndipo mfumu idati kwa Hamani, siliva akhale wako, ndi anthu omwe; uchite nao monga momwe chikukomera. 12#Est. 8.9-15Pamenepo anaitana alembi a mfumu mwezi woyamba, tsiku lake lakhumi ndi chitatu, nalembera monga mwa zonse Hamani analamulira akazembe ndi ziwanga zoyang'anira maiko ali onse, ndi akalonga a mitundu iliyonse ya anthu, maiko ali onse monga mwa chilembedwe chao, ndi mitundu iliyonse ya anthu monga mwa chinenedwe chao; anazilemba m'dzina la mfumu Ahasuwero, nazisindikiza ndi mphete ya mfumu. 13Ndipo anatumiza akalata ndi amtokoma kumaiko onse a mfumu, kuti aononge, aphe, napulule Ayuda onse, ndiwo ana, ndi okalamba, makanda, ndi akazi, tsiku limodzi, ndilo tsiku lakhumi ndi chitatu la mwezi wakhumi ndi chiwiri, ndiwo mwezi wa Adara; nalande zao mofunkha. 14Mau a cholembedwacho, ndiwo kuti lichitike lamulo m'maiko onse, analalikidwa kwa anthu onse, kuti akonzekeretu tsiku lomwelo. 15Amtokoma anatuluka ofulumizidwa ndi mau a mfumu, ndi lamulo linabukitsidwa m'chinyumba cha ku Susa; ndipo mfumu ndi Hamani anakhala pansi kumwa; koma mudzi wa Susa unadodoma.
Currently Selected:
ESTERE 3: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi