YouVersion Logo
Search Icon

DANIELE 8

8
Masomphenya a nkhosa yamphongo ndi tonde
1Chaka chachitatu cha Belisazara mfumu masomphenya anandionekera kwa ine Daniele, atatha kundionekera oyamba aja. 2#Est. 1.2Ndipo ndinaona m'masomphenya; tsono kunali, pakuwaona ine ndinali m'Susa, m'nyumba ya mfumu, ndiwo m'dziko la Elamu; ndinaona m'masomphenya kuti ndinali kumtsinje Ulai. 3Ndipo ndinakweza maso anga ndi kupenya; taonani, panaima pamtsinje nkhosa yamphongo yokhala nazo nyanga ziwiri, ndi nyanga ziwirizo zinali za msinkhu wautali, koma imodzi inaposa inzake; yoposayo inaphuka m'mbuyo. 4Ndinaona nkhosa yamphongo ilikugunda kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera; ndipo panalibe zamoyo zokhoza kuima pamaso pake; panalibenso wakulanditsa m'dzanja lake; koma inachita monga mwa chifuniro chake, nidzikulitsa. 5Ndipo polingirirapo ine, taonani, wadza tonde wochokera kumadzulo, pa nkhope ya dziko lonse lapansi, wosakhudza nthaka; ndi mbuziyo inali ndi nyanga yooneka bwino pakati pa maso ake. 6Ndipo anadzera nkhosa yamphongoyo yokhala ndi nyanga ziwiri, imene ndidaiona ilikuima kumtsinje, naithamangira ndi mphamvu yake yaukali. 7Ndipo ndinamuona wayandikira pafupi pa nkhosa yamphongo, nawawidwa mtima nayo, naigunda nkhosa yamphongo, nathyola nyanga zake ziwiri; ndipo mphongoyo inalibe mphamvu yakuima pamaso pake, koma anaigwetsa pansi, naipondereza; ndipo panalibe wakupulumutsa mphongoyo m'dzanja lake. 8Ndipo tondeyo anadzikulitsa kwakukulu, koma atakhala wamphamvu, nyanga yake yaikulu inathyoka; ndi m'malo mwake munaphuka nyanga zinai zooneka bwino, zoloza kumphepo zinai za mlengalenga. 9Ndipo mu imodzi ya izi munaphuka nyanga yaing'ono, imene inakula kwakukulu ndithu, kuloza kumwera, ndi kum'mawa, ndi kudziko lokometsetsa. 10Nikula, kufikira khamu la kuthambo; ndi zina za khamulo ndi za nyenyezi inazigwetsa pansi, nizipondereza. 11#Ezk. 46.13Inde inadzikulitsa kufikira kwa kalonga wa khamulo, nimchotsera nsembe yopsereza yachikhalire, ndi pokhala malo ake opatulika panagwetsedwa. 12#Mas. 119.43, 142Ndipo khamulo linaperekedwa kwa iyo, pamodzi ndi nsembe yopsereza yachikhalire mwa kulakwa kwake, nigwetsa pansi choonadi, nichita chifuniro chake, nikuzika. 13Pamenepo ndinamva wina woyera alikunena; ndi wina woyera anati kwa iye uja wanenayo, Masomphenya a nsembe yopsereza yachikhalire, ndi cholakwa chakupululutsa cha kupereka malo opatulika ndi khamulo ziponderezedwe, adzakhala mpaka liti? 14Nati kwa ine, Mpaka masiku zikwi ziwiri mphambu mazana atatu usana ndi usiku; pamenepo malo opatulika adzayesedwa olungama.
15Ndipo kunali, nditaona masomphenyawo, ine Daniele ndinafuna kuwazindikira; ndipo taonani, panaima popenyana ndi ine ngati maonekedwe a munthu. 16#Dan. 9.21; Luk. 1.19, 26Ndipo ndinamva mau a munthu pakati pa magombe a Ulai, naitana, nati, Gabriele, zindikiritsa munthuyu masomphenyawo. 17Nayandikira iye poima inepo; atadza iye tsono ndinachita mantha, ndinagwa nkhope pansi; koma anati kwa ine, Zindikira, wobadwa ndi munthu iwe, pakuti masomphenyawo anena za nthawi ya chimaliziro. 18Ndipo m'mene analikulankhula ndi ine ndinagwidwa ndi tulo tatikulu, nkhope yanga pansi; koma anandikhudza, nandiimiritsa pokhala inepo. 19Ndipo anati, Taona, ndidzakudziwitsa chimene chidzachitika pa chitsiriziro cha mkwiyowo; pakuti pa nthawi yoikika mpakutha pake. 20#Dan. 8.3Nkhosa yamphongo waiona ya nyanga ziwiri ndizo mafumu a Mediya ndi Persiya. 21#Dan. 8.5Ndi tonde wamanyenje ndiye mfumu ya Agriki, ndi nyanga yaikulu ili pakati pa maso ake ndiyo mfumu yoyamba. 22Ndi kuti zinaphuka zinai m'malo mwake mwa iyo itathyoka, adzauka maufumu anai ochokera mu mtunduwu wa anthu, koma osakhala nayo mphamvu ya uja. 23Ndipo potsiriza pake pa ufumu wao, atakwanira olakwa, idzauka mfumu ya nkhope yaukali yakuzindikira zinsinsi. 24#Chiv. 17.13, 17Ndi mphamvu yake idzakhala yaikulu, koma si mphamvu yakeyake ai, nidzaononga modabwitsa, nidzakuzika, ndi kuchita, ndi kuononga amphamvuwo, ndi anthu opatulikawo. 25#Dan. 2.34Ndipo mwa kuchenjera kwake adzapindulitsa chinyengo m'dzanja mwake, nadzadzikuza m'mtima mwake; ndipo posatekeseka anthu, adzaononga ambiri; adzaukiranso kalonga wa akalonga, koma adzathyoledwa popanda dzanja. 26Ndipo masomphenya a madzulo ndi mamawa adanenawo ndi oona; koma iwe ubise masomphenyawo, popeza adzachitika atapita masiku ambiri. 27Ndipo ine Daniele ndinakomoka ndi kudwala masiku ena; pamenepo ndinauka ndi kuchita ntchito ya mfumu; ndipo ndinadabwa nao masomphenyawo, koma panalibe wakuwazindikiritsa.

Currently Selected:

DANIELE 8: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in