YouVersion Logo
Search Icon

MACHITIDWE A ATUMWI Mau Oyamba

Mau Oyamba
Buku la Machitidwe a Atumwi likungopitiriza nkhani yomwe idayamba kale mu Luka. Cholinga chenicheni cha bukuli ndicho kunena za m'mene otsatira a Yesu, motsogozedwa ndi Mzimu Woyera, anafalitsira Uthenga Wabwino wonena za Iye kuyambira “m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko”. (1.8) Imeneyi ndi mbiri ya chiyambi cha Chikhristu pakati pa Ayuda mpaka pamene chinafalikira pakati pa anthu a m'dziko lonse lapansi. Wolembayo amafunitsitsa kuwatsimikizira awerengi kuti akhristu sali ogalukira ulamuliro wa Aroma, koma kuti Chikhristu chikungokwaniritsa za m'chipembedzo cha Chiyuda.
Buku la Machitidwe lingathe kugawidwa m'magawo atatu akuluakulu, pofuna kuonetsa kulikonse kumene Uthenga Wabwino wa Yesu umalalikidwa ndipo mipingo imayamba, Chikhristu chimanka chikulirakulira: (1) Yesu akwera kunka kumwamba ndipo Chikhristu chiyamba ku Yerusalemu; (2) Mpingo ufalikira kumadera ozungulira Palestina; (3) Mpingo ukulabe, kufika ku Nyanja ya Meditereniyani mpaka ku Roma.
Chinthu chofunika kwambiri mu buku la Machitidwe ndicho ntchito ya Mzimu Woyera, amene anabwera ndi mphamvu pa okhulupirira ku Yerusalemu pa tsiku la Pentekoste ndipo akupitiriza kutsogolera ndi kulimbikitsa mpingo ndi atsogoleri ake kudzera mu zochitika zimene zalembedwa mu bukuli. Mauthenga a mpingo woyamba akulembedwa mwachidule mu maulaliki osiyanasiyana, ndipo zinthu zimene zalembedwa mu buku la Machitidwe zikuonetsa mphamvu ya uthengawu m'moyo wa okhulupirira ndi mu Mpingo.
Za mkatimu
Kukonzekera mboni 1.1-26
a. Lamulo ndi lonjezo lomaliza la Yesu 1.1-14
b. Asankha wolowa m'malo mwa Yudasi 1.15-26
Mboni za mu Yerusalemu 2.1—8.3
Mboni za mu Yudeya ndi mu Samariya 8.4—12.25
Utumiki wa Paulo 13.1—28.31
a. Ulendo woyamba 13.1—14.28
b. Msonkhano wa ku Yerusalemu 15.1-35
c. Ulendo wachiwiri 15.36—18.22
d. Ulendo wachitatu 18.23—21.16
e. Paulo aponyedwa m'ndende ku Yerusalemu, ku Kesareya ndi ku Roma 21.17—28.31

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in