YouVersion Logo
Search Icon

MACHITIDWE A ATUMWI 9

9
Kusandulika mtima kwa Paulo pa njira ya ku Damasiko
1 # Agal. 1.13 Koma Saulo, wosaleka kupumira pa ophunzira a Ambuye kuopsa ndi kupha, ananka kwa mkulu wa ansembe, 2napempha kwa iye akalata akunka nao ku Damasiko ku masunagoge, kuti akapeza ena otsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nao omangidwa ku Yerusalemu. 3#Mac. 22.6-11Ndipo poyenda ulendo wake, kunali kuti iye anayandikira Damasiko: ndipo mwadzidzidzi kudawala momzingira kuunika kochokera kumwamba; 4#Mat. 25.40ndipo anagwa pansi, namva mau akunena naye, Saulo, Saulo, Undilondalonderanji? 5Koma anati, Ndinu yani Mbuye? Ndipo anati, Ndine Yesu amene umlondalonda; 6komatu, uka, nulowe m'mudzi, ndipo kudzanenedwa kwa iwe chimene uyenera kuchita. 7Ndipo amunawo akumperekeza iye anaima duu, atamvadi mau, koma osaona munthu. 8Ndipo Saulo anauka; koma potseguka maso ake, sanapenya kanthu; ndipo anamgwira dzanja, namtenga nalowa naye m'Damasiko. 9Ndipo anakhala masiku atatu wosaona, ndipo sanadya kapena kumwa.
10Koma ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lake Ananiya; ndipo Ambuye anati kwa iye m'masomphenya, Ananiya. Ndipo anati, Ndili pano, Ambuye, 11#Mac. 21.39Ndipo Ambuye anati kwa iye, Tauka, pita ku khwalala lotchedwa Lolunjika, ndipo m'nyumba ya Yudasi ufunse za munthu dzina lake Saulo, wa ku Tariso: pakuti taona, alikupemphera 12ndipo anaona mwamuna dzina lake Ananiya, alikulowa, namuika manja, kuti apenyenso. 13Ndipo Ananiya anayankha nati, Ambuye, ndamva ndi ambiri za munthu uyu, kuti anachitiradi choipa oyera mtima anu m'Yerusalemu; 14ndi kuti pano ali nao ulamuliro wa kwa ansembe aakulu wakumanga onse akuitana pa dzina lanu. 15#Mac. 13.2; 22.21Koma Ambuye anati kwa iye, Pita; pakuti iye ndiye chotengera changa chosankhika, chakunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israele; 16#Mac. 20.23pakuti Ine ndidzamuonetsa iye zinthu zambiri ayenera iye kuzimva kuwawa chifukwa cha dzina langa. 17#Mac. 22.12-13Ndipo anachoka Ananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja ake pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani pa njira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera. 18Ndipo pomwepo padagwa kuchoka m'maso mwake ngati mamba, ndipo anapenyanso; ndipo ananyamuka nabatizidwa; 19ndipo analandira chakudya, naona nacho mphamvu.
Azunzika mzunziyo
Ndipo anakhala pamodzi ndi ophunzira a ku Damasiko masiku ena.
20Ndipo pomwepo m'masunagoge analalikira Yesu, kuti Iye ndiye Mwana wa Mulungu. 21#Agal. 1.13, 23Ndipo onse amene anamva anadabwa, nanena, Suyu iye amene anaononga m'Yerusalemu onse akuitana pa dzina ili? Ndipo wadza kuno kudzatero, kuti amuke nao omangidwa kwa ansembe aakulu. 22Koma Saulo anakula makamaka mumphamvu, nadodometsa Ayuda akukhala m'Damasiko, nawatsimikizira kuti ameneyo ndi Khristu.
23 # Mac. 23.12 Ndipo atapita masiku ambiri, Ayuda anapangana kuti amuphe iye; 24#2Ako. 11.32-33koma chiwembu chao chinadziwika ndi Saulo. Ndipo anadikiranso pazipata usana ndi usiku kuti amuphe; 25#2Ako. 11.32-33koma ophunzira ake anamtenga usiku, nampyoletsa palinga, namtsitsa mu dengu.
26 # Agal. 1.17-18 Koma m'mene anafika ku Yerusalemu, anayesa kudziphatika kwa ophunzira; ndipo anamuopa iye onse, osakhulupirira kuti ali wophunzira. 27#Mac. 13.2Koma Barnabasi anamtenga, napita naye kwa atumwi, nawafotokozera umo adaonera Ambuye m'njira, ndi kuti analankhula naye, ndi kuti m'Damasiko adanena molimbika mtima m'dzina la Yesu. 28Ndipo anali pamodzi nao, nalowa natuluka ku Yerusalemu, 29nanena molimbika mtima m'dzina la Ambuye; ndipotu analankhula natsutsana ndi Agriki; koma anayesayesa kumupha iye. 30Koma m'mene abale anachidziwa, anapita naye ku Kesareya, namtumiza achokeko kunka ku Tariso.
31 # Mac. 20.23 Pamenepo ndipo Mpingo wa m'Yudeya lonse ndi Galileya ndi Samariya unali nao mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m'kuopa kwa Ambuye ndi m'chitonthozo cha Mzimu Woyera, nuchuluka.
Achiritsidwa Eneya; aukitsidwa Tabita
32Koma kunali, pakupita Petro ponseponse, anatsikiranso kwa oyera mtima akukhala ku Lida. 33Ndipo anapeza kumeneko munthu dzina lake Eneya, amene anagonera pamphasa zaka zisanu ndi zitatu; amene anagwidwa manjenje. 34#Mac. 3.6, 16; 4.10Ndipo Petro anati kwa iye, Eneya, Yesu Khristu akuchiritsa iwe; uka, yalula mphasa yako. Ndipo anauka pomwepo. 35Ndipo anamuona iye onse akukhala ku Lida ndi ku Saroni, natembenukira kwa Ambuye amenewa.
36 # Tit. 3.8 Koma m'Yopa munali wophunzira dzina lake Tabita, ndilo kunena Dorika; mkazi ameneyo anadzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo zimene anazichita. 37Ndipo kunali m'masiku awa, kuti anadwala iye, namwalira; ndipo atamsambitsa iye anamgoneka m'chipinda chapamwamba. 38Ndipo popeza Lida ndi pafupi pa Yopa, m'mene anamva ophunzirawo kuti Petro anali pomwepo, anamtumizira anthu awiri, namdandaulira, Musachedwa mudze kwa ife. 39Ndipo Petro ananyamuka, napita nao. M'mene anafikako, anapita naye kuchipinda chapamwamba; ndipo amasiye onse anaimirirapo pali iye, nalira, namuonetsa malaya ndi zovala zimene Dorika adasoka, pamene anali nao pamodzi. 40#Mrk. 5.41-42Koma Petro anawatulutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ake; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga. 41#Mrk. 5.41-42Ndipo Petro anamgwira dzanja, namnyamutsa; ndipo m'mene adaitana oyera mtima ndi amasiye, anampereka iye wamoyo. 42#Yoh. 11.45Ndipo kudadziwika ku Yopa konse: ndipo ambiri anakhulupirira Ambuye. 43Ndipo kunali, kuti anakhala iye m'Yopa masiku ambiri ndi munthu Simoni wofufuta zikopa.

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in