MACHITIDWE A ATUMWI 8
8
Uthenga Wabwino pa Samariya. Simoni wanyanga
1 #
Mac. 7.58; 11.19 Ndipo Saulo analikuvomerezana nao pa imfa yake. Ndipo tsikulo kunayamba kuzunza kwakukulu pa Mpingo unali m'Yerusalemu; ndipo anabalalitsidwa onse m'maiko a Yudeya ndi Samariya, koma osati atumwi ai. 2Ndipo anamuika Stefano anthu opembedza, namlira maliro akulu. 3#Mac. 11.19Ndipo Saulo anapasula Mpingo, nalowa nyumba ndi nyumba, nakokamo amuna ndi akazi, nawaika m'ndende.
4 #
Mat. 10.23; Mac. 11.19 Pamenepo ndipo iwo akubalalitsidwa anapitapita nalalikira mauwo. 5#Mac. 6.5Ndipo Filipo anatsikira kumudzi wa ku Samariya, nawalalikira iwo Khristu. 6Ndipo makamuwo ndi mtima umodzi anasamalira zonenedwa ndi Filipo, pamene anamva, napenya zizindikiro zimene anazichita. 7#Mrk. 16.17Pakuti ambiri a iwo akukhala nayo mizimu yonyansa inawatulukira, yofuula ndi mau akulu; ndipo ambiri amanjenje, ndi opunduka, anachiritsidwa. 8Ndipo panakhala chimwemwe chachikulu m'mudzimo.
9 #
Mac. 13.6
Koma panali munthu dzina lake Simoni amene adachita matsenga m'mudzimo kale, nadabwitsa anthu a Samariya, ndi kunena kuti iye yekha ndiye munthu wamkulu; 10ameneyo anamsamalira onsewo, kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu, ndi kunena, Uyu ndiye mphamvu ya Mulungu, yonenedwa Yaikulu. 11Ndipo anamsamalira iye, popeza nthawi yaikulu adawadabwitsa iwo ndi matsenga ake. 12Koma pamene anakhulupirira Filipo wakulalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi dzina la Yesu Khristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi. 13Ndipo Simoni mwini wake anakhulupiriranso: ndipo m'mene anabatizidwa, anakhalira ndi Filipo; ndipo pakuona zizindikiro ndi mphamvu zazikulu zilikuchitika, anadabwa.
14Koma pamene atumwi a ku Yerusalemu anamva kuti Samariya adalandira mau a Mulungu, anawatumizira Petro ndi Yohane; 15#Mac. 2.38amenewo, m'mene adatsikirako, anawapempherera, kuti alandire Mzimu Woyera: 16#Mac. 19.2pakuti kufikira pamenepo nkuti asanagwe pa wina mmodzi wa iwo; koma anangobatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu. 17#Mac. 6.6Pamenepo anaika manja pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera. 18Koma pakuona Simoni kuti mwa kuika manja a atumwi anapatsidwa Mzimu Woyera, anawatengera ndalama, 19nanena, Ndipatseni inenso ulamuliro umene, kuti amene aliyense ndikaika manja pa iye, alandire Mzimu Woyera. 20#Yes. 55.1Koma Petro anati kwa iye, Ndalama yako itayike nawe, chifukwa unalingirira kulandira mphatso ya Mulungu ndi ndalama. 21Ulibe gawo kapena cholandira ndi mau awa; pakuti mtima wako suli wolunjika pamaso pa Mulungu. 22#2Tim. 2.25Chifukwa chake lapa choipa chako ichi, pemphera Ambuye, kuti kapena akukhululukire iwe cholingirira cha mtima wako. 23#Aheb. 12.15Pakuti ndiona kuti wagwidwa ndi ndulu yowawa ndi nsinga ya chosalungama. 24#Yak. 5.16Ndipo Simoni anayankha nati, Mundipempherere ine kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi.
25Pamenepo iwo, atatha kuchita umboni ndi kulankhula mau a Ambuye, anabwera kunka ku Yerusalemu, nalalikira Uthenga Wabwino kumidzi yambiri ya Asamariya.
Filipo ndi mdindo wa ku Etiopiya
26Koma mngelo wa Ambuye analankhula ndi Filipo, nanena, Nyamuka, nupite mbali ya kumwera, kutsata njira yotsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Gaza; ndiyo ya chipululu. 27#Zef. 3.10; Yoh. 12.20Ndipo ananyamuka napita; ndipo taona munthu wa ku Etiopiya, mdindo wamphamvu wa Kandake, mfumu yaikazi ya Aetiopiya, ndiye wakusunga chuma chake chonse, amene anadza ku Yerusalemu kudzapemphera; 28ndipo analinkubwerera, nalikukhala pa galeta wake, nawerenga mneneri Yesaya. 29Ndipo Mzimu anati kwa Filipo, Yandikira, nudziphatike kugaleta uyu. 30Ndipo Filipo anamthamangira, namva iye alikuwerenga Yesaya mneneri, ndipo anati, Kodi muzindikira chimene muwerenga? 31Koma anati, Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine? Ndipo anapempha Filipo akwere nakhale naye. 32#Yes. 53.7-8Koma palembo pamene analikuwerengapo ndipo:
Ngati nkhosa anatengedwa kukaphedwa,
ndi monga mwanawankhosa ali duu pamaso pa womsenga,
kotero sanatsegula pakamwa pake.
33M'kuchepetsedwa kwake chiweruzo chake chinachotsedwa;
mbadwo wake adzaubukitsa ndani?
Chifukwa wachotsedwa kudziko moyo wake.
34Ndipo mdindoyo anayankha Filipo, nati, Ndikupempha, mneneri anena ichi za yani? Za yekha, kapena za wina? 35#Luk. 24.27Ndipo Filipo anatsegula pakamwa pake, nayamba pa lembo ili, nalalikira kwa iye Yesu. 36#Mac. 10.47Ndipo monga anapita panjira pao, anadza kumadzi akuti; ndipo mdindoyo anati, Taonapo madzi; chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe?#8.36 Mabuku ena akale amaonjezerapo vesi 37 Ndipo Filipo adamuyankha nati, “Ngati mukhulupirira ndi mtima wanu wonse mungathe kubatizidwa.” Ndipo iye anati, “Ndikhulupirira kuti Yesu Khristu ndiye Mwana wa Mulungu.” 38Ndipo anamuuza kuti aimitse galeta; ndipo anatsikira onse awiri kumadzi, Filipo ndi mdindoyo; ndipo anambatiza iye. 39#1Maf. 18.12; Ezk. 3.14Ndipo pamene anakwera kutuluka m'madzi, Mzimu wa Ambuye anakwatula Filipo; ndipo mdindo sanamuonanso, pakuti anapita njira yake wokondwera. 40Koma Filipo anapezedwa ku Azoto; ndipo popitapita analalikira Uthenga Wabwino m'midzi yonse, kufikira anadza iye ku Kesareya.
Currently Selected:
MACHITIDWE A ATUMWI 8: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi