2 SAMUELE 17
17
1Ndipo Ahitofele ananena ndi Abisalomu, Ndiloleni ndisankhe tsopano anthu zikwi khumi ndi ziwiri, ndipo ndidzanyamuka usiku womwe uno ndi kulondola Davide; 2#2Sam. 16.14ndipo ndidzamgwera ali wolema ndi wofooka, ndi kumuopsa; ndi anthu onse amene ali naye adzathawa; pamenepo ndidzakantha mfumu yokha; 3ndipo anthu onsewo ndidzabwera nao kwa inu; munthu mumfunayo ali ngati onse obwerera; momwemo anthu onse adzakhala mumtendere. 4Ndipo mauwa anamuyenerera Abisalomu, ndi akulu onse a Israele.
Uphungu wa Husai
5Pomwepo Abisalomu anati, Kaitane tsopano Husai Mwariki yemwe, timvenso chimene anene iye. 6Ndipo pakufika Husai kwa Abisalomu, Abisalomuyo ananena naye, Ahitofele analankhula mau akuti; tichite kodi monga mwa kunena kwake? Ngati iai, unene ndiwe. 7Ndipo Husai ananena ndi Abisalomu, Uphungu anaupangira lero Ahitofele suli wabwino. 8#Miy. 17.12; Hos. 13.8Husai anatinso, Mudziwa atate wanu ndi anthu ake kuti ndizo ngwazi, ndipo ali ndi mitima yowawa monga chimbalangondo chochilanda ana ake kuthengo; ndipo atate wanu ali munthu wodziwa nkhondo, sadzagona pamodzi ndi anthu. 9Onani, tsopanoli alikubisala kudzenje kapena kwina; ndipo kudzali poyamba kugwa ena, aliyense wakumva adzanena, Alikuphedwa anthu otsata Abisalomu. 10Ndipo ngakhale ngwazi imene mtima wake ukunga mtima wa mkango idzasungunuka konse, pakuti Aisraele onse adziwa atate wanu kuti ndiye munthu wamphamvu, ndi iwo ali naye ndiwo ngwazi. 11#Gen. 22.17Koma uphungu wanga ndiwo kuti musonkhanitse Aisraele onse kwa inu kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, monga mchenga uli panyanja kuchuluka kwao; ndi kuti mutuluke kunkhondo mwini wake. 12Chomwecho tidamvumbulukira pa malo akuti adzapezeka, ndipo tidzamgwera monga mame agwa panthaka, ndipo sitidzasiya ndi mmodzi yense wa iye ndi anthu onse ali naye. 13Ndiponso ngati walowa kumudzi wina, Aisraele onse adzabwera ndi zingwe kumudziko, ndipo tidzaukokera kumtsinje, kufikira sikapezeka kamwala kakang'ono kumeneko. 14#2Sam. 15.31, 34Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israele anati, Uphungu wa Husai Mwariki uposa uphungu wa Ahitofele. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofele kuti Yehova akamtengere Abisalomu choipa.
15 #
2Sam. 15.35-36
Pomwepo Husai ananena ndi Zadoki ndi Abiyatara ansembewo, Ahitofele anapangira Abisalomu ndi akulu a Israele zakutizakuti; koma ine ndinapangira zakutizakuti. 16#2Sam. 15.28Chifukwa chake tsono mutumize msanga nimuuze Davide kuti Musagona usiku uno pa madooko a kuchipululu, koma muoloke ndithu, kuti mfumu ingamezedwe ndi anthu onse amene ali naye. 17Ndipo Yonatani ndi Ahimaazi anakhala ku Enirogele; mdzakazi ankapita kuwauza; ndipo iwo anapita nauza mfumu Davide, pakuti sangaoneke iwowo alikulowa m'mudzi. 18Koma mnyamata wina anawaona nauza Abisalomu; ndipo ajawo anachoka msanga onse awiri, nafika kunyumba ya munthu ku Bahurimu, amene anali nacho chitsime pabwalo pake; ndipo anatsikira m'menemo. 19#Yos. 2.6Ndipo mkazi anatenga chivundikiro nachiika pakamwa pa chitsime, napapasapo lipande la tirigu; momwemo sichinadziwika. 20Ndipo anyamata a Abisalomu anafika kunyumba kwa mkaziyo; nati, Ali kuti Ahimaazi ndi Yonatani? Ndipo mkaziyo ananena nao, Anaoloka kamtsinje kamadzi. Ndipo atawafunafuna, osawapeza, anabwerera kunka ku Yerusalemu.
Davide ndi anthu ake aoloka Yordani
21Ndipo kunali, atapita iwo, ajawo anatuluka m'chitsime, namka nauza mfumu Davide; nati kwa Davide, Nyamukani nimuoloke madzi msanga; pakuti Ahitofele anapangira zotere pa inu. 22Pomwepo Davide ananyamuka ndi anthu onse amene anali naye, naoloka Yordani. Kutacha m'mawa sanasowe mmodzi wa iwo wosaoloka Yordani. 23#2Maf. 20.1; Mat. 27.5Ndipo Ahitofele, pakuona kuti sautsata uphungu wake anamanga bulu wake, nanyamuka, nanka kumudzi kwao, nakonza za pa banja lake, nadzipachika, nafa, naikidwa m'manda a atate wake.
Abisalomu ndi anthu ake aolokanso Yordani
24 #
Gen. 32.2
Ndipo Davide anafika ku Mahanaimu. Abisalomu naoloka Yordani, iye ndi anthu onse a Israele pamodzi naye. 25Ndipo Abisalomu anaika Amasa, kazembe wa khamulo, m'malo a Yowabu. Koma Amasayu ndiye mwana wa munthu dzina lake Yetere Mwismaele, amene analowa kwa Abigaile, mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wa Zeruya, amai a Yowabu. 26Ndipo Israele ndi Abisalomu anamanga zithando m'dziko la Giliyadi.
Nkhondo imlaka Abisalomu, naphedwa iye mwini
27 #
2Sam. 19.13-32
Ndipo kunali pakufika Davide ku Mahanaimu, Sobi mwana wa Nahasi wa ku Raba wa ana a Amoni, ndi Makiri mwana wa Amiyele wa ku Lodebara, ndi Barizilai Mgiliyadi wa ku Rogelimu, 28iwo anabwera nao makama, ndi mbale, ndi zotengera zadothi, ndi tirigu, ndi barele, ndi ufa, ndi tirigu wokazinga, ndi nyemba, ndi mphodza, ndi zokazinga zina, 29ndi uchi ndi mafuta, ndi nkhosa, ndi mase a ng'ombe, kuti adye Davide, ndi anthu amene anali naye; pakuti anati, Anthu ali ndi njala, olema, ndi aludzu m'chipululumo.
Currently Selected:
2 SAMUELE 17: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi