YouVersion Logo
Search Icon

2 SAMUELE 10

10
Davide akantha Aamoni ndi Aaramu
1Ndipo kunali zitapita izi, mfumu ya ana a Amoni inamwalira, ndipo Hanuni mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. 2Ndipo Davide anati, Ndidzachitira Hanuni mwana wa Nahasi zokoma, monga atate wake anandichitira ine zokoma. Chomwecho Davide anatumiza ndi dzanja la anyamata ake kuti akamsangalatse chifukwa cha atate wake. Ndipo anyamata a Davide anafika ku dziko la ana a Amoni. 3Koma akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni mbuye wao, Kodi muganiza kuti Davide alemekeza atate wanu, popeza anakutumizirani osangalatsa? Kodi Davide sanatumize anyamata ake kwa inu, kuti ayang'ane mudziwo ndi kuuzonda ndi kuupasula? 4Chomwecho Hanuni anatenga anyamata a Davide nawameta ndevu zao mbali imodzi, nadula zovala zao pakati, kufikira m'matako ao, nawaleka amuke. 5Pamene anachiuza Davide iye anatumiza anthu kukakomana nao; pakuti amunawo anachita manyazi akulu. Niti mfumu, Bakhalani ku Yeriko kufikira zamera ndevu zanu; zitamera mubwere. 6Ndipo pamene ana a Amoni anazindikira kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, ana a Amoniwo anatumiza nadzilembera Aaramu a ku Beterehobu, ndi Aaramu a ku Zoba, oyenda pansi zikwi makumi awiri, ndi mfumu ya ku Maaka ndi anthu chikwi chimodzi, ndi anthu a mfumu ya ku Tobu zikwi khumi ndi ziwiri. 7#2Sam. 23.8Ndipo pamene Davide anachimva, anatumiza Yowabu ndi khamu lonse la anthu amphamvu. 8Ndipo ana a Amoni anatuluka, nandandalitsa nkhondo polowera kuchipata. Ndipo Aaramu a ku Zoba ndi a ku Rehobu, ndi anthu a Tobu ndi Maaka, anali pa okha kuthengo. 9Ndipo pamene Yowabu anaona kuti nkhondo inamdzera kumaso ndi kumbuyo, iye anasankha amuna osankhidwa onse a Israele, nawandandalitsa cha kwa Aramu. 10Koma anthu otsalawo anawapereka kwa Abisai mbale wake, amene anawandandalitsa cha kwa Amoni. 11Ndipo iye anati, Aaramu akandipambana ine, udzandithandiza ndiwe, koma ana a Amoni akapambana iwe, tsono ndidzabwera ine kukuthandiza. 12#Deut. 31.6; 1Sam. 3.18; 1Ako. 16.13Ulimbike mtima, ndipo tichite chamuna lero chifukwa cha anthu athu ndi midzi ya Mulungu wathu; Yehova nachite chomkomera. 13Chomwecho Yowabu ndi anthu amene anali naye anayandikira kuponyana nkhondo ndi Aaramu. Ndipo iwowa anathawa pamaso pake. 14Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti Aaramu anathawa, iwonso anathawa pamaso pa Abisai, nalowa m'mudzimo. Ndipo Yowabu anabwera kuchokera kwa ana a Amoni, nafika ku Yerusalemu. 15Ndipo pamene Aaramu anaona kuti Aisraele anawathyola, anasonkhana pamodzi. 16#2Sam. 8.3Ndipo Hadadezere anatumiza mthenga nakatenga Aaramu a ku tsidya la chimtsinje; iwo nafika ku Helamu, ndi Sobaki kazembe wa khamu la nkhondo la Hadadezere anawatsogolera. 17Ndipo wina anauza Davide; iye nasonkhanitsa Aisraele onse, naoloka Yordani nafika ku Helamu. Ndipo Aaramu anandandalitsa nkhondo yao pa Davide namenyana naye. 18Ndipo Aaramu anathawa pamaso pa Israele; Davide naphapo Aaramu apamagaleta mazana asanu ndi awiri, ndi apakavalo zikwi makumi anai, nakantha Sobaki kazembe wa khamu lao, nafa iye pomwepo. 19#2Sam. 8.6Ndipo pamene mafumu onse, otumikira Hadadezere, anaona kuti Aisraele anawapambana, iwo anapangana mtendere ndi Aisraele, nawatumikira. Chomwecho Aaramu anaopa kuwathandizanso ana a Amoni.

Currently Selected:

2 SAMUELE 10: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in