YouVersion Logo
Search Icon

2 MBIRI 35

35
Yosiya achita Paska ku Yerusalemu
1 # 2Maf. 23.21-23 Pamenepo Yosiya anachitira Yehova Paska m'Yerusalemu, naphera Paska tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi woyamba. 2#2Mbi. 29.11Ndipo anaika ansembe pa udikiro wao, nawalimbikitsa achite utumiki wa nyumba ya Yehova. 3#1Mbi. 23.26; Mala. 2.7Nati kwa Alevi akuphunzitsa Aisraele onse, ndiwo opatulikira Yehova, Ikani likasa lopatulika m'nyumba imene Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israele anaimanga; silikhalanso katundu pa mapewa anu; tsopano mutumikire Yehova Mulungu wanu, ndi anthu ake Israele. 4#2Mbi. 8.14Ndipo mudzikonzere monga mwa nyumba za makolo anu, m'zigawo zanu, monga umo adalembera Davide mfumu ya Israele, ndi umo adalembera Solomoni mwana wake. 5Ndipo muimirire m'malo opatulika, monga mwa magawidwe a nyumba za makolo za abale anu ana a anthu, akhale nalo onse gawo la nyumba ya makolo ya Alevi. 6#2Mbi. 29.5Ndipo muphere Paska, nimudzipatule ndi kukonzera abale anu, kuchita monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose. 7#2Mbi. 30.24Ndipo Yosiya anapatsa ana a anthu zoweta, anaankhosa ndi a mbuzi zikhale zonsezo za nsembe za Paska kwa aliyense anali komweko; zinafikira zikwi makumi atatu, ndi ng'ombe zikwi zitatu, ndizo zotapa pa chuma cha mfumu. 8Ndi akulu ake anapatsa nsembe yaufulu kwa anthu, kwa ansembe, ndi kwa Alevi. Hilikiya ndi Zekariya ndi Yehiyele, atsogoleri a m'nyumba ya Mulungu, anapatsa ansembe zoweta zazing'ono zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi, ndi ng'ombe mazana atatu, zikhale nsembe za Paska. 9Konaniyanso, ndi Semaya, ndi Netanele, abale ake, ndi Hasabiya, ndi Yeiyele, ndi Yozabadi, akulu a Alevi, anapatsa Alevi zoweta zazing'ono zikwi zisanu, ndi ng'ombe mazana asanu, zikhale nsembe za Paska. 10Momwemo anakonzera kutumikiraku, naima ansembe pokhala pao, ndi Alevi m'zigawo zao, monga umo adawauzira mfumu. 11#2Mbi. 29.34Pamenepo anaphera Paska; ndi ansembe anawaza mwazi adaulandira m'manja mwa Alevi amene anasenda nsembezo. 12Ndipo anachotsapo nsembe zopsereza, kuti azipereke kwa ana a anthu monga mwa magawidwe a nyumba za makolo; azipereke kwa Yehova monga mulembedwa m'buku la Mose. Natero momwemo ndi ng'ombezo. 13#Eks. 12.8-9; 1Sam. 2.13-15Ndipo anaotcha Paska pamoto, monga mwa chiweruzo; koma zopatulikazo anaziphika m'miphika, ndi m'mitsuko, ndi m'ziwaya; nazipereka msanga kwa ana onse a anthu. 14Ndi pambuyo pake anadzikonzera okha ndi ansembe; popeza ansembe, ana a Aroni, analikupereka nsembe zopsereza ndi mafuta mpaka usiku; chifukwa chake Alevi anadzikonzera okha ndi ansembe ana a Aroni. 15#1Mbi. 25—26Ndi oimbira, ana a Asafu, anali pokhala pao, monga adalamulira Davide, ndi Asafu, ndi Hemani, ndi Yedutuni mlauli wa mfumu; ndi olindirira anali pa zipata zonse, analibe kuleka utumiki wao; pakuti abale ao Alevi anawakonzera. 16Momwemo kutumikira konse kwa Yehova kunakonzeka tsiku lomwelo, kuchita Paska, ndi kupereka nsembe zopsereza pa guwa la nsembe la Yehova, monga analamulira mfumu Yosiya. 17Ndipo ana a Israele okhalako anachita Paska nthawi yomweyo, ndi chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri. 18#2Maf. 23.22-23Panalibe Paska wochitika m'Israele wonga ameneyu, kuyambira masiku a Samuele mneneri; panalibenso wina wa mafumu a Israele anachita Paska wotere, ngati ameneyu anachita Yosiya, ndi ansembe, ndi Alevi, ndi Ayuda onse, ndi Aisraele opezekako, ndi okhala m'Yerusalemu. 19Yosiya atakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri anachita Paska amene.
Yosiya ayambana ndi Neko mfumu ya Aejipito, naphedwa
20 # 2Maf. 23.29-30 Chitatha ichi chonse, Yosiya atakonza nyumbayi, Neko mfumu ya Aejipito anakwera kuyambana ku Karikemisi ku Yufurate; ndipo Yosiya anamtulukira kuyambana naye. 21Koma Neko anatuma mithenga kwa iye, ndi kuti, Ndili ndi chiyani ndi inu, mfumu ya Yuda? Sindinafika kuyambana ndi inu lero, koma ndi nyumba imene ndili nayo nkhondo; ndipo Mulungu anati ndifulumire; lekani kuvutana ndi Mulungu amene ali nane, Iye angakuonongeni. 22#1Maf. 22.30Koma Yosiya sanatembenuke nkhope yake kumleka, koma anadzizimbaitsa kuti ayambane naye, osamvera mau a Neko ochokera m'kamwa mwa Mulungu; nadza kuyambana naye m'chigwa cha Megido. 23Ndipo oponya anayang'anitsa mivi pa mfumu Yosiya, niti mfumu kwa anyamata ake, Ndichotseni ndalasidwa ndithu. 24#Zek. 12.11Pamenepo anyamata ake anamtulutsa m'galeta, namuika m'galeta wachiwiri anali naye, nabwerera naye ku Yerusalemu; nafa iye naikidwa m'manda a makolo ake. Ayuda onse ndi Yerusalemu nalira Yosiya. 25#Mat. 9.23; Yer. 22.20Ndipo Yeremiya anamlembera Yosiya nyimbo yomlira; ndi oimbira onse, amuna ndi akazi, amanena za Yosiya nyimbo za maliro zao mpaka lero lino; naziika zikhale lemba m'Israele; taonani, zilembedwa m'Nyimbo za Maliro. 26Machitidwe ena tsono a Yosiya, ndi ntchito zake zokoma, monga mulembedwa m'chilamulo cha Yehova, 27ndi zochita iye, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m'buku la mafumu a Israele ndi Yuda.

Currently Selected:

2 MBIRI 35: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in