2 MBIRI 23
23
Yehoyada adzoza Yowasi akhale mfumu
1 #
2Maf. 11.4-20
Koma chaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anadzilimbitsa natenga atsogoleri a mazana, Azariya mwana wa Yerohamu, ndi Ismaele mwana wa Yehohanani, ndi Azariya mwana wa Obedi, ndi Maaseiya mwana wa Adaya, ndi Elisafati mwana wa Zikiri, apangane naye pamodzi. 2Ndipo iwo anayendayenda mwa Yuda, nasonkhanitsa Alevi m'midzi yonse ya Yuda, ndi akulu a nyumba za makolo m'Israele; nadza iwo ku Yerusalemu. 3Ndipo msonkhano wonse unapangana pangano ndi mfumu m'nyumba ya Mulungu. Ndipo ananena nao, Taonani, mwana wa mfumu adzakhala mfumu monga Yehova ananena za ana a Davide. 4#1Mbi. 9.25Chimene muzichita ndi ichi: limodzi la magawo atatu mwa inu olowera tsiku la Sabata, la ansembe ndi Alevi, akhale olindirira pakhomo; 5ndi limodzi la magawo atatu likhale kunyumba ya mfumu; ndi limodzi la magawo atatu ku Chipata cha Maziko; ndi anthu onse akhale m'mabwalo a nyumba ya Yehova. 6Koma asalowe mmodzi m'nyumba ya Yehova, ansembe okha, ndi Alevi otumikira, alowe iwowa; pakuti ndiwo opatulika; koma anthu onse asunge udikiro wa Yehova. 7Ndipo Alevi amzinge mfumu pozungulirapo, yense ndi zida zake m'dzanja mwake; ndipo aliyense wolowa m'nyumba aphedwe; nimukhale inu pamodzi ndi mfumu pakulowa ndi pakutuluka iye. 8#1Mbi. 24.25-26Momwemo Alevi ndi Ayuda onse anachita monga mwa zonse anawauza Yehoyada wansembe; natenga yense amuna ake alowe tsiku la Sabata pamodzi ndi otuluka tsiku la Sabata; pakuti Yehoyada wansembe sanamasule zigawo. 9Ndi Yehoyada wansembe anapereka kwa akazembe a mazana mikondo, ndi zikopa, ndi malaya achitsulo, zinali za mfumu Davide, zokhala m'nyumba ya Mulungu. 10Ndipo anaika anthu onse, yense ndi chida chake m'dzanja lake, amzinge mfumu, kuyambira mbali ya kudzanja lamanja la nyumba kufikira mbali ya kudzanja lamanzere la nyumba, kuloza kuguwa la nsembe ndi kunyumba. 11#Deut. 17.18-19Pamenepo anatulutsa mwana wa mfumu, namveka korona, nampatsa mboni, namlonga ufumu; ndi Yehoyada ndi ana ake anamdzoza, nati, Ikhale ndi moyo mfumu.
Aphedwa Ataliya
12Ndipo pamene Ataliya anamva phokoso la anthu alikuthamanga ndi kulemekeza mfumu, anadza kwa anthu m'nyumba ya Yehova; 13napenya, ndi kuona mfumu inaima pa nsanamira yake polowera; ndi atsogoleri, ndi malipenga, anali kwa mfumu; ndi anthu onse a m'dziko anakondwera, naomba amalipenga; oimbira omwe analiko ndi zoimbirazo, nalangiza poimbira cholemekeza. Pamenepo Ataliya anang'amba zovala zake, nati, Chiwembu, chiwembu. 14Koma Yehoyada wansembe anatuluka nao atsogoleri a mazana akuyang'anira khamu la nkhondo, nanena nao, Mtulutseni mkaziyo pakati pa mipambo; ndipo aliyense womtsata aphedwe ndi lupanga; pakuti wansembe adati, Msamphere m'nyumba ya Yehova. 15Ndipo anampisa malo; namuka iye kolowera ku Chipata cha Akavalo kunyumba ya mfumu; ndi pomwepo anamupha.
Pangano la Yehoyada wansembe
16Ndipo Yehoyada anachita pangano pakati pa iye, ndi anthu onse, ndi mfumu, kuti adzakhala anthu a Yehova. 17#Deut. 13.6, 9Ndi anthu onse anamuka kunyumba ya Baala, naipasula, naphwanya maguwa ake a nsembe, ndi mafano ake; namupha Matani wansembe wa Baala kumaguwa a nsembe. 18Ndipo Yehoyada anaika mayang'aniro a nyumba ya Yehova m'dzanja la ansembe Aleviwo, amene Davide anawagawa, ayang'anire nyumba ya Yehova; napereka nsembe zopsereza za Yehova monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose, ndi kukondwera ndi kuimbira, monga mwa chilangizo cha Davide. 19Ndipo anaika odikira kumakomo a nyumba ya Yehova, kuti wodetsedwa nako kanthu kalikonse asalowemo. 20#2Maf. 11.19Natenga atsogoleri a mazana, ndi omveka, ndi akazembe a anthu, ndi anthu onse a m'dziko, natsika ndi mfumu kunyumba ya Yehova; nalowera pa chipata cha kumtunda m'nyumba ya mfumu, namkhalitsa mfumu pa mpando wa ufumu. 21Ndipo anthu onse a m'dziko anakondwera; ndi m'mudzi munali chete, atamupha Ataliya ndi lupanga.
Currently Selected:
2 MBIRI 23: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi