1 SAMUELE 11
11
Saulo alanditsa Yabesi-Giliyadi m'manja mwa Aamoni
1 #
Eks. 23.32
Pamenepo Nahasi Mwamoni anakwera, namanga Yabesi-Giliyadi zithando; ndipo anthu onse a ku Yabesi anati kwa Nahasi, Mupangane chipangano ndi ife, ndipo tidzakutumikirani inu. 2Ndipo Nahasi Mwamoni ananena nao, Ndidzapangana nanu, ngati mulola kuti maso a ku dzanja lamanja anu onse akolowoledwe; potero ndidzanyazitsa Aisraele onse. 3Ndipo akulu a ku Yabesi ananena naye, Mutipatse masiku asanu ndi awiri, kuti titumize mithenga m'malire onse a Israele; ndipo pakapanda kuoneka wotipulumutsa ife, tidzatulukira kwa inu. 4#Ower. 2.4; 1Sam. 10.26Tsono mithengayo inafika ku Gibea kwa Saulo, nalankhula mau amenewa m'makutu a anthu; ndipo anthu onse anakweza mau, nalira misozi. 5Ndipo, onani, Saulo anachokera kumunda alikutsata ng'ombe; nati Saulo, Choliritsa anthu misozi nchiyani? Ndipo anamuuza mau a anthu a ku Yabesi. 6#1Sam. 10.10Ndipo mzimu wa Mulungu unamgwera Saulo mwamphamvu, pamene anamva mau awa, ndi mkwiyo wake unayaka kwambiri. 7#Ower. 19.29; 21.5Natenga ng'ombe ziwiri nazidula nthulinthuli, nazitumiza m'malire monse mwa Israele, ndi dzanja la mithenga, nati, Amene sakudza pambuyo pa Saulo ndi pa Samuele, adzatero nazo ng'ombe zake. Ndipo kuopsa kwa Yehova kunawagwera anthu, natuluka ngati munthu mmodzi. 8Ndipo anawawerenga ku Bezeki; ndipo ana a Israele anali zikwi mazana atatu, ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi makumi atatu. 9Ndipo anati kwa mithenga inadzayi, Muzitero kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi, Mawa litatentha dzuwa, mudzaona chipulumutso. Ndipo mithenga inadza niuza a ku Yabesi; nakondwera iwowa. 10#1Sam. 11.3Chifukwa chake anthu a ku Yabesi anati, Mawa tidzatulukira kwa inu, ndipo mudzatichitira chokomera inu. 11Ndipo m'mawa mwake Saulo anagawa anthu magulu atatu; ndipo iwowa anafika pakati pa zithandozo m'ulonda wa mamawa, nakantha Aamoni kufikira kutentha kwa dzuwa. Ndipo otsalawo anabalalika, osatsala pamodzi ngakhale awiri. 12#Luk. 19.27Ndipo anthu anati kwa Samuele, Ndani iye amene anati, Kodi Saulo adzatiweruza ife? Tengani anthuwo kuti tiwaphe. 13#1Sam. 19.5; 2Sam. 19.22Koma Saulo anati, Sadzaphedwa lero munthu; pakuti lero Yehova anachita chipulumutso m'Israele.
14Ndipo Samuele ananena kwa anthuwo, Tiyeni tipite ku Giligala, kukonzanso ufumu kumeneko. 15#1Sam. 10.8Ndipo anthu onse anapita ku Giligala; ndi kumeneko analonga Saulo mfumu pamaso pa Yehova m'Giligala; ndi pamenepo anaphera nsembe zoyamika pamaso pa Yehova; ndi pomwepo Saulo ndi anthu onse a Israele anakondwera kwakukulu.
Currently Selected:
1 SAMUELE 11: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi