YouVersion Logo
Search Icon

1 MAFUMU 7

7
Mamangidwe a nyumba ya Solomoni
1 # 2Mbi. 8.1 Koma nyumba ya iye yekha Solomoni anaimanga zaka khumi mphambu zitatu, natsiriza nyumba yake yonse. 2Anamanganso nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni, m'litali mwake munali mikono zana limodzi, kupingasa kwake mikono makumi asanu, ndi msinkhu wake mikono makumi atatu; naisanja pa mizere inai ya mapanda amkungudza, ndi mitanda yamkungudza, ndi mitanda yamkungudza yotanthalika mapandawo. 3Ndipo inayalidwa ndi mkungudza pamwamba pa zipinda makumi anai mphambu zisanu zolongosoledwa pa mapanda, mzere umodzi zipinda khumi mphambu asanu. 4Ndipo panali mazenera m'mizere itatuyo, zenera limodzi lopenyana ndi linzake mizere itatu. 5Ndipo makomo onse ndi mphuthu zonse zinali zaphwamphwa maonekedwe ake, ndipo zenera limodzi linapenyana ndi linzake mizere itatu. 6Ndipo anamanga khonde la nsanamira, m'litali mwake munali mikono makumi asanu, kupingasa kwake mikono makumi atatu; ndipo panali khonde lina patsogolo pake, ndi nsanamira ndi mitanda patsogolo pakepo. 7Ndipo anamanga khonde la mpando wachifumu loweruziramo iye, ndilo khonde la milandu, ndipo linayalidwa ndi mkungudza pansi ndi posanja. 8#2Mbi. 8.11Ndipo nyumba yake yakukhalamo iye, m'bwalo lina la m'tsogolo mwa khondelo, linamangidwa chimodzimodzi. Anammangiranso nyumba mwana wamkazi wa Farao, amene adamkwatira Solomoni, yofanafana ndi khonde limeneli. 9Izi zonse zinali za miyala ya mtengo wapatali yosemasema, malingana ndi miyeso yake, yocheka ndi mipeni ya manomano m'katimo ndi kunjako, kuyambira kumaziko kufikira kumutu, momwemonso kunjako ku bwalo lalikulu. 10Ndipo maziko ake anali a miyala ya mtengo wapatali, ndiyo miyala yaikulu, miyala ya mikono khumi, ndi miyala ya mikono isanu ndi itatu. 11Ndi pamwamba pake panali miyala ya mtengo wapatali, ndiyo miyala yosemasema monga muyeso wake, ndi mitengo yamkungudza. 12#Yoh. 10.23; Mac. 3.11Ndipo bwalo lalikulu lozingapo linali ndi mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungudza, monga bwalo la pakati pa nyumba ya Yehova, ndi chipinda cholowera cha nyumbayo.
Zokometsera ndi zipangizo za Kachisi
13 # 2Mbi. 2.13-14 Ndipo mfumu Solomoni anatuma anthu kukatenga Hiramu ku Tiro. 14#Eks. 31.3; 36.1Iyeyo anali mwana wake wa mkazi wamasiye wa fuko la Nafutali, atate wake anali munthu wa ku Tiro, mfundi wamkuwa; ndipo iye anadzala ndi nzeru ndi luntha ndi luso kugwira ntchito zonse za mkuwa. Ndipo anadza kwa mfumu Solomoni namgwirira ntchito zake zonse. 15#2Mbi. 3.15Popeza iyeyu anaunda nsanamira ziwiri zamkuwa, msinkhu wake wa imodzi unali mikono khumi mphambu isanu ndi itatu; ndipo chingwe cha mikono khumi mphambu iwiri chinayesa thupi la nsanamira imodzi. 16Ndipo anapanga mitu iwiri ya mkuwa wosungunula, kuiika pamwamba pa nsanamirazo, msinkhu wake wa mutu wina unali mikono isanu, ndi msinkhu wa mutu unzake mikono isanu. 17Ndipo panali maukonde olukaluka ndi zoyangayanga, zokolana za pa mitu imene inali pamwamba pa nsanamira; zisanu ndi ziwiri za pa mutu wina, ndi zisanu ndi ziwiri za pa mutu unzake. 18M'mwemo anapanga nsanamira, ndipo panali mizere iwiri yozungulira ukonde umodzi, kukuta ndi makangaza mituyi inali pamwambapo, nachita momwemo ndi mutu winawo. 19Ndipo mituyi inali pamwamba pa nsanamira za pa chipinda cholowera chinali ngati akakombo malembedwe ake, a mikono inai. 20#2Mbi. 3.16-17Ndipo panalinso mitu pamwamba pa nsanamira ziwirizo, pafupi pa mimbayo, inali m'mbali mwake mwa ukondewo; ndipo makangazawo anali mazana awiri, akukhala mizere yozinga ndanda mutu winawo. 21Ndipo anaimiritsa nsanamirazi pa chipinda cholowera cha Kachisi; naimiritsa nsanamira ya ku dzanja lamanja, natcha dzina lake Yakini; naimiritsa nsanamira yakumanzere, natcha dzina lake Bowazi. 22Ndipo pamwamba pa nsanamirazo panali ngati akakombo malembedwe ake; motero anaitsiriza ntchito ya nsanamirazo. 23#2Mbi. 4.2-5; Yer. 52.17Ndipo anayenganso thawale lamkuwa, kukamwa kwake kunali kwa mikono khumi, linali lozunguniza, ndi msinkhu wake unali mikono isanu; ndi chingwe cha mikono makumi atatu chinalizungulira. 24Ndipo m'khosi mwake munali ngati zikho zozinganiza m'mkono umodzi zikho khumi zakuzinganiza thawalelo; zikhozo zinayengedwa m'mizere iwiri poyengedwa thawalelo.
25Linasanjikika pa ng'ombe khumi mphambu ziwiri, zitatu zinapenya kumpoto, zitatu kumadzulo, zitatu kumwera, zitatu kum'mawa; ndipo thawalelo linakhazikika pamwamba pa izo; ndipo nkholo zao zinayang'anana. 26Ndipo kuchindikira kwake kunali ngati chikhato cha munthu, ndipo mlomo wake unasadamuka ngati mlomo wa chomwera, ngati maluwa akakombo, analowamo madzi a mitsuko yaikulu zikwi ziwiri. 27Ndipo anapanga maphaka khumi amkuwa, m'litali mwake mwa phaka limodzi mikono inai, ndi msinkhu wake mikono itatu. 28Ndipo mapangidwe a maphakawo anali otere: anali nao matsekerezo ao, ndipo matsekerezo anali pakati pa mbano. 29Ndipo pa matsekezerezo a pakati pa mbano panali ngati mikango ndi ng'ombe ndi akerubi, ndi pamwamba pa mbano panali chosanjikirapo; ndipo pansi pa mikango ndi ng'ombe panaphatikizika zotsetseremba zoyangayanga zokoloweka. 30Ndipo phaka lililonse linali ndi njinga zamkuwa zinai ndi mitanda yamkuwa, ndipo ngodya zake zinai zinali ndi mapewa; pansi pa thawale panali mapewa oyengeka pa mbali pa zophatikizika zonse. 31Ndipo pakamwa pake m'katimo pamwamba pa chosanjikira, panayesa mkono umodzi; koma pakamwa pake panali posadamuka, monga mapangidwe ake a chosanjikira, mkono umodzi ndi nusu; ndiponso pakamwa pake panali zolemba ndi matsekerezo ake anali aphwamphwa, si ozunguniza. 32Ndipo njinga zinai zinali pansi pa matsekerezo, ndi mitanda ya njinga inali m'mphakamo, ndi msinkhu wa njinga imodzi unali mkono umodzi ndi nusu. 33Ndipo mapangidwe a njinga analingana ndi mapangidwe a njinga za galeta, mitanda yake ndi mkombero wake ndi nthiti zake ndi mtima wake zonsezo zinayengedwa. 34Ndipo panali ngati mapewa anai pansi pangodya zinali za phaka limodzi, mapewawo anali a phaka lomwelo. 35Ndipo pamwamba pa phaka panali khoma lozunguniza, msinkhu wake nusu ya mkono; ndi pamwamba pa phaka panali mbano zake ndi matsekerezo a phaka lomwelo. 36Ndipo m'mapanthi mwa mbano zake ndi pa matsekerezo ake analemba ngati akerubi ndi mikango ndi migwalangwa, monga mwa malo ake a zonsezo, ndi zoyangayanga zozungulira.
37Motero anapanga maphaka khumiwo, anafanana mayengedwe ao muyeso wao ndi maonekedwe ao. 38Ndipo anapanga mbiya zaphwamphwa khumi zamkuwa; m'mbiya imodziyo munalowamo madzi a mitsuko yaikulu makumi anai, ndipo mbiya iliyonse inali ya mikono inai: pa phaka lililonse la maphaka aja khumi panakhala mbiya imodzi. 39Ndipo anaika maphaka asanu ku dzanja lamanja la nyumba, ndi maphaka asanu ku dzanja lamanzere la nyumba; naika thawalelo ku dzanja lamanja la nyumba kum'mawa kupenya kumwera. 40Ndipo Hiramu anayenga mbiyazo ndi zoolera ndi mbale zowazira. Motero Hiramu anatsiriza kupanga ntchito yonse anaichitira mfumu Solomoni ya m'nyumba ya Yehova. 41Nsanamira ziwirizo, ndi mbale za mitu inali pamwamba pa nsanamira ziwirizo, ndi maukonde awiri ophimbira mbale ziwiri za mitu inali pamwamba pa nsanamirazo, 42ndi makangaza mazana anai a maukonde awiriwo, mizere iwiri ya makangaza a ukonde umodzi kuphimbira mbale ziwiri za mitu inali pa nsanamirazo, 43ndi maphaka khumiwo ndi mbiya khumi zili pa maphakawo, 44ndi thawale limodzilo, ndi ng'ombe khumi mphambu ziwirizo pansi pa thawale; 45#Eks. 27.3ndi miphikayo, ndi zoolerazo, ndi mbalezo; inde zotengera zonse zimene Hiramu anampangira mfumu Solomoni za m'nyumba ya Yehova, zinali za mkuwa wonyezimira. 46#2Mbi. 4.17Mfumu inaziyenga pa chidikha cha ku Yordani, m'dothi ladongo, pakati pa Sukoti ndi Zaretani. 47Ndipo Solomoni anazileka zipangizo zonse osaziyesa, popeza zinachuluka ndithu; kulemera kwake kwa mkuwa wonsewo sikunayeseka. 48#Eks. 37.10-15, 25-28Ndipo Solomoni anapanga zipangizo zonse za m'nyumba ya Yehova: guwa la nsembe lagolide, ndi gome lagolide loikapo mikate yoonekera; 49ndi zoikapo nyali za golide woyengetsa, zisanu ku dzanja lamanja, zisanu kulamanzere, chakuno cha chipinda chamkati, ndi maluwa ndi nyali ndi mbano zagolide; 50ndi zikho, ndi zozimira nyali, ndi mbale, ndi zipande, ndi zopalira moto za golide woyengetsa, ndi zomangira zitseko zagolide, za zitseko za chipinda cha m'katimo, malo opatulika kwambiri, ndiponso za zitseko za nyumba ya Kachisi. 51#2Sam. 8.11; 2Mbi. 5.1Motero ntchito zonse zinatsirizika, zimene mfumu Solomoni anachitira nyumba ya Yehova. Ndipo Solomoni analonga zinthu adazipatula Davide atate wake, ndizo siliva ndi golide ndi zipangizo zomwe naziika mosungira chuma cha nyumba ya Yehova.

Currently Selected:

1 MAFUMU 7: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in