YouVersion Logo
Search Icon

1 MAFUMU 5

5
Solomoni apangana ndi Hiramu za mirimo yomanga nayo Kachisi
1 # 2Sam. 5.11; 2Mbi. 2.3 Ndipo Hiramu mfumu ya ku Tiro anatuma anyamata ake kwa Solomoni, popeza anamva kuti adamdzoza mfumu m'malo mwa atate wake; pakuti Hiramu adakondana ndi Davide masiku onse. 2Ndipo Solomoni anatumiza mau kwa Hiramu, nati, 3#1Mbi. 22.8Mudziwa inu kuti atate wanga Davide sanathe kumangira dzina la Yehova Mulungu wake nyumba, chifukwa cha nkhondo zakumzinga konseko, mpaka atawaika Yehova pansi pa mapazi ake. 4#1Maf. 4.24Koma tsopano Yehova Mulungu wanga wandipumulitsa ku mbali zonse; palibe wotsutsana nane, kapena choipa chondigwera. 5#2Sam. 7.13Ndipo taonani, ndikuti ndimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, monga Yehova anauza atate wanga Davide, ndi kuti, Mwana wako ndidzamuika pa mpando wako wachifumu m'malo mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumbayo. 6#2Mbi. 2.8, 10Ndipo tsono, lamulirani kuti anditemere mitengo yamkungudza ku Lebanoni, ndipo akapolo anga adzakhala ndi akapolo anu, ndipo ndidzakupatsani mphotho ya akapolo anu monga mudzanena; popeza mudziwa kuti pakati pa ife palibe mmisiri wakudziwa kutema mitengo ngati anthu a ku Sidoni. 7Ndipo kunachitika, pamene Hiramu anamva mau ake a Solomoni, anakondwera kwakukulu, nati, Alemekezeke Yehova lero amene wampatsa Davide mwana wanzeru akhale mfumu ya anthu aunyinji amenewa. 8Ndipo Hiramu anatumiza kwa Solomoni, nati, Ndazimva zija munatumiza kwa inezo, ndidzachita chifuniro chanu chonse, kunena za mitengo yamkungudza ndi mitengo yamlombwa. 9#2Mbi. 2.16Akapolo anga adzatsika nayo ku Lebanoni kufika nayo ku nyanja, ndipo ine ndidzaiyandamitsa paphaka kufikira komwe mudzandiuzako, ndi kumeneko ndidzaimasula, ndipo mudzaitenga; nimudzachita chifuniro changa, kumapatsa banja langa zakudya. 10Tsono Hiramu anapatsa Solomoni mitengo yamkungudza ndi mitengo yamlombwa monga momwe anafuniramo. 11#2Mbi. 2.10Ndipo Solomoni anapatsa Hiramu miyeso ya tirigu zikwi makumi awiri ndiyo zakudya za banja lake, ndi miyeso makumi awiri ya mafuta oyera; motero Solomoni anapatsa Hiramu chaka ndi chaka. 12#1Maf. 3.12Ndipo Yehova anapatsa Solomoni nzeru monga momwe adamlonjezera; ndipo panali mtendere pakati pa Hiramu ndi Solomoni, iwo awiri napangana pamodzi. 13Ndipo mfumu Solomoni anasonkhetsa athangata mwa Aisraele onse, ndi athangatawo ndiwo anthu zikwi makumi atatu. 14Ndipo anawatuma ku Lebanoni mwezi umodzi zikwi khumi kuwasintha, mwezi umodzi iwo anali ku Lebanoni, miyezi iwiri anali kwao; ndipo Adoniramu anali kapitao wa athangata. 15#2Mbi. 2.17-18Ndipo Solomoni anawasenzetsa akatundu anthu zikwi makumi asanu ndi awiri, ndi anthu zikwi makumi asanu ndi atatu anatema m'mapiri; 16osawerenga akapitao a Solomoni akuyang'anira ntchito, ndiwo zikwi zitatu mphambu mazana atatu, amenewo analamulira anthu aja akugwira ntchito. 17#1Mbi. 22.2Ndipo mfumu inalamula iwo, natuta miyala yaikuluikulu ya mtengo wapatali, kuika maziko ake a nyumbayo ndi miyala yosemasema. 18Ndipo omanga nyumba a Solomoni ndi omanga nyumba a Hiramu ndi anthu a ku Gebala anaisema, naikonza mitengo ndi miyala yakumangira nyumbayo.

Currently Selected:

1 MAFUMU 5: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in