YouVersion Logo
Search Icon

1 MAFUMU 20

20
Nkhondo pakati pa Ahabu ndi Benihadadi
1Ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anamemeza khamu lake lonse la nkhondo; ndi mafumu makumi atatu mphambu awiri anali naye, pamodzi ndi akavalo ndi magaleta; nakamangira Samariya misasa, naponyana nao nkhondo. 2Natumiza mithenga kumudzi kwa Ahabu mfumu ya Israele, nati kwa iye, 3Atero Benihadadi, Siliva wako ndi golide wako ndi wanga, akazi ako ndi ana ako omwe okometsetsawo ndi anga. 4Ndipo mfumu ya Israele anayankha, nati, Monga mwanena, mbuye wanga mfumu, ndine wanu ndi zonse ndili nazo. 5Tsono mithenga ija inabwerera, niti, Atero Benihadadi, kuti, Ndinatumadi kwa iwe, ndi kuti, Uzindipatsa siliva wako, ndi golide wako, ndi akazi ako, ndi ana ako; 6koma mawa dzuwa lino ndidzatuma anyamata anga kwa iwe, nadzafunafuna m'nyumba mwako, ndi m'nyumba za anyamata ako; ndipo kudzakhala kuti chifuniro chonse cha maso ako adzachigwira ndi manja ao, nadzachichotsa. 7Pamenepo mfumu ya Israele anaitana akulu onse a dziko, nati, Tazindikirani inu, penyani kuti munthu uyu akhumba choipa; popeza anatuma kwa ine kulanda akazi anga, ndi ana anga, ndi siliva, ndi golide wanga; ndipo sindinamkaniza. 8Ndipo akulu onse ndi anthu onse anati kwa iye, Musamvere, musavomereze. 9Ndipo anati kwa mithenga ya Benihadadi, Kauzeni mbuye wanga mfumu, Zonse munayamba mundituma mtumiki wanu kuzifunsa ndidzachita, koma ichi sindingachichite. Nichoka mithengayo, nimbwezera mau. 10Ndipo Benihadadi anatuma kwa iye, nati, Milungu indilange, nionjezepo, ngati fumbi la Samariya lidzafikira kudzaza manja a anthu onse akutsata mapazi anga. 11Ndipo mfumu ya Israele anayankha, nati, Kamuuzeni, Wakumanga zida asadzikuze ngati wakuvulayo. 12#1Maf. 20.16Ndipo kunachitika, atamva Benihadadi mau awa, analikumwa nao mafumu m'misasa, ananena ndi anyamata ake, Nikani. Nandandalika pamudzipo. 13#1Maf. 20.28Ndipo taonani, mneneri anadza kwa Ahabu mfumu ya Israele, nati, Atero Yehova, Kodi waona unyinji uwu waukulu wonse? Taonani, ndidzaupereka m'dzanja mwako lero, kuti udziwe kuti ndine Yehova. 14Nati Ahabu, Mwa yani? Nati, Atero Yehova, Mwa anyamata a akalonga a madera. Natinso, Adzayamba kuponya nkhondo ndani? Nati, Iwe. 15Pamenepo anawerenga anyamata a akalonga a madera, nawapeza mazana awiri mphambu makumi atatu kudza awiri. Pamenepo anawerenganso anthu onse, ndiwo ana a Israele onse zikwi zisanu ndi ziwiri. 16#1Maf. 20.12Ndipo amenewo anatuluka usana. Koma Benihadadi analinkumwa naledzera m'misasamo, iye ndi mafumu aja makumi atatu mphambu awiri aja akumthandiza. 17Ndipo anyamata a akalonga a madera anayamba kutuluka, koma Benihadadi anatuma anthu, iwo nambwezera mau, kuti, M'Samariya mwatuluka anthu. 18Nati iye, Chinkana atulukira mumtendere, agwireni amoyo; chinkana atulukira m'nkhondo, agwireni, amoyo. 19Tsono anatuluka m'mudzi anyamata a akalonga a madera aja, ndi khamu la nkhondo linawatsata. 20Ndipo aliyense anapha munthu wake; ndipo Aaramu anathawa, Aisraele nawapirikitsa; ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anathawira pa kavalo pamodzi ndi apakavalo. 21Tsono mfumu ya Israele inatuluka, nikantha apakavalo ndi apamagaleta, nawapha Aaramuwo maphedwe akulu. 22#2Sam. 11.2Ndipo mneneri uja anayandikira kwa mfumu ya Israele, nati kwa iye, Kadzilimbitseni, mudziwe muchenjere ndi chimene muchichita; popeza chaka chikudzachi mfumu ya Aramu idzabweranso kulimbana nanu.
23Ndipo anyamata a mfumu ya Aramu anati kwa iye, Milungu yao nja kumapiri, ndimo m'mene atilakira; koma tikaponyana nao kuchidikha, zedi tidzaposa mphamvu. 24Tsono chitani ichi, chotsani mafumu aja yense ku malo ake, muike m'malo mwao akazembe. 25Ndipo mudziwerengere khamu la nkhondo longa khamu lija lidaonongekalo, ndi akavalo onga akavalo aja, ndi magaleta monga omwe aja; ndipo tikaponyane nao pachidikha tidzawapambana ndithu. Namvera iye mau ao, natero kumene. 26#1Maf. 20.13Tsono kunachitika, pakufikanso chaka Benihadadi anamemeza Aaramu nakwera ku Afeki kukaponyana ndi Aisraele. 27Ndipo Aisraele anamemezananso, anali naye kamba, nakakomana nao; ndipo Aisraele anamanga misasa yao pandunji pao, ngati timagulu tiwiri ta anaambuzi; koma Aaramu anadzaza dziko. 28Ndipo munthu uja wa Mulungu anafikako, nalankhula ndi mfumu ya Israele, nati, Atero Yehova, Popeza Aaramu amati, Yehova ndiye Mulungu wa kumapiri, osati Mulungu wa kuzigwa, mwa ichi ndidzapereka unyinji uwu waukulu m'dzanja mwako, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova. 29Ndipo awa anakhala m'misasa pandunji pa ajawo masiku asanu ndi awiri. Tsono kunali, tsiku lachisanu ndi chiwiri anayambana nkhondo; ndipo ana a Israele anaphako Aaramu tsiku limodzi anthu oyenda pansi zikwi zana limodzi. 30Ndipo otsalawo anathawira ku Afeki kumudzi, ndipo linga linawagwera anthu zikwi makumi awiri mphambu asanu ndi awiri amene adatsalawo. Ndipo Benihadadi anathawa, nalowa m'mudzi, m'chipinda cha m'katimo. 31Pamenepo anyamata ake anati kwa iye, Taonani, tidamva ife kuti mafumu a nyumba ya Israele ndi mafumu achifundo; tiyeni tivale chiguduli m'chuuno mwathu, ndi zingwe pamitu pathu, titulukire kwa mfumu ya Israele, kapena adzakusungirani moyo. 32Motero anavala chiguduli m'chuuno mwao, ndi zingwe pamitu pao, nafika kwa mfumu ya Israele, nati, Kapolo wanu Benihadadi ati, Ndiloleni ndikhale ndi moyo. Nati iye, Akali moyo kodi? Ndiye mbale wanga. 33Tsono anthuwo anamyang'anitsa, nafulumira kugwira mauwo ngati anaterodi; nati, Mbale wanu Benihadadi ali moyo, Nati, Kamtengeni. Pamenepo Benihadadi anatuluka, nadza kwa iye, ndipo iye anamkweza m'galeta mwake. 34#1Maf. 15.20Ndipo Benihadadi anati kwa iye, Ndidzabweza midzi ija atate wanga analanda kwa atate wanu; ndipo mudzikonzere mabwalo a malonda m'Damasiko, monga umo atate wanga anadzikonzera m'Samariya. Ndi ine, ati Ahabu, ndikulola umuke ndi pangano ili. Tsono anapangana naye, namlola amuke.
35Ndipo wina wa ana a aneneri ananena ndi mnzake mwa mau a Yehova, Undikanthe ine. Koma munthuyo anakana kumkantha. 36#1Maf. 13.24Ndipo ananena naye, Popeza sunamvera mau a Yehova, taona, utalekana nane mkango udzakupha. Ndipo m'mene atalekana naye, mkango unampeza, numupha. 37Ndipo amene uja anakomana ndi munthu wina, nati, Undikanthe. Namkantha munthuyu, namtema pomkantha. 38Pamenepo mneneriyo anamuka, nadikira mfumu pamseu, nadzizimbaitsa ndi mpango pamaso pake. 39#2Maf. 10.24Ndipo popitapo mfumu, anafuula kwa mfumu, nati, Kapolo wanu analowa pakati pa nkhondo, ndipo taonani, munthu anapatuka nabwera ndi munthu kwa ine, nati, Tasunga munthu uyu; akasowa ndi chifukwa chilichonse moyo wako udzakhala m'malo mwa moyo wake, kapena udzalipa talente la siliva, 40Tsono pochita kapolo wanu apo ndi apo ndapeza palibe. Ndipo mfumu ya Israele inati kwa iye, Mlandu wako ukutsutsa momwemo, wadziweruza wekha. 41Ndipo iye anafulumira kuchotsa mpango kumaso kwake, ndi mfumu ya Israele inaona kuti anali mmodzi wa aneneri. 42Niti kwa iye, Atero Yehova, Popeza wataya m'dzanja lako munthu uja ndinati ndimuononge konse, moyo wako udzakhala m'malo mwa moyo wake, ndi anthu ako m'malo mwa anthu ake. 43Pamenepo mfumu ya Israele inanka kwao wamsunamo ndi wokwiya, nafika ku Samariya.

Currently Selected:

1 MAFUMU 20: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in