1 MAFUMU 2:2-4
1 MAFUMU 2:2-4 BLPB2014
Ndimuka ine njira ya dziko lonse: limba mtima tsono, nudzionetse umunthu; nusunge chilangizo cha Yehova Mulungu wako, kuyenda m'njira zake, kusunga malemba ndi malamulo ndi maweruzo ndi umboni wake, monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose, kuti ukachite mwa nzeru m'zonse ukachitazo, ndi kumene konse ukatembenukirako; kuti Yehova akakhazikitse mau ake adanenawo za ine, kuti, Ngati ana ako akasunga bwino njira zao, kuyenda moona pamaso pa Ine ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse, nditi sipadzakusowa mwamuna mmodzi pa mpando wachifumu wa Israele.