Masalimo 106
106
Salimo 106
1Tamandani Yehova.
Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
pakuti chikondi chake ndi chosatha.
2Ndani angathe kufotokoza za ntchito zamphamvu za Yehova
kapena kumutamanda mokwanira?
3Odala ndi amene amasunga chilungamo,
amene amachita zolungama nthawi zonse.
4Mundikumbukire Yehova, pamene mukuonetsa kukoma mtima kwanu kwa anthu anu,
bwerani mudzandithandize pamene mukuwapulumutsa iwo,
5kuti ndidzasangalale ndi chuma cha anthu anu osankhika,
kuti ndidzakhale nacho chimwemwe cha anthu anu
ndi kukhala pamodzi ndi cholowa chanu pa kukutamandani.
6Ife tachimwa monga momwe anachitira makolo athu;
tachita zolakwa ndipo tachita moyipa.
7Pamene makolo athu anali mu Igupto,
sanalingalire za zozizwitsa zanu;
iwo sanakumbukire kukoma mtima kwanu kochuluka,
ndipo anawukira Inu pa Nyanja Yofiira.
8Komabe Iye anawapulumutsa chifukwa cha dzina lake,
kuti aonetse mphamvu zake zazikulu.
9Anadzudzula Nyanja Yofiira, ndipo inawuma;
anawatsogolera mʼnyanja yakuya ngati akuyenda mʼchipululu.
10Anawapulumutsa mʼdzanja la amaliwongo;
anawawombola mʼdzanja la mdani.
11Madzi anamiza adani awo,
palibe mmodzi wa iwo anapulumuka.
12Kenaka iwo anakhulupirira malonjezo ake
ndi kuyimba nyimbo zamatamando.
13Koma posachedwa anayiwala zimene Iye anachita,
ndipo sanayembekezere uphungu wake.
14Mʼchipululu, anadzipereka ku zilakolako zawo;
mʼdziko lopanda kanthu anayesa Mulungu.
15Choncho Iye anawapatsa chimene anapempha,
koma anatumiza nthenda yowondetsa.
16Mʼmisasa, anachitira nsanje Mose ndi Aaroni,
amene Yehova anadzipatulira.
17Nthaka inatsekuka ndipo inameza Datani;
inakwirira gulu la Abiramu.
18Moto unayaka pakati pa otsatira awo;
lawi lamoto linapsereza anthu oyipa.
19Iwo anapanga mwana wangʼombe pa Horebu
ndi kulambira fano loyengedwa kuchokera ku chitsulo.
20Anasinthanitsa ulemerero wawo
ndi fano la ngʼombe yayimuna imene imadya udzu.
21Anayiwala Mulungu amene anawapulumutsa,
amene anachita zinthu zazikulu mu Igupto,
22zozizwitsa mʼdziko la Hamu
ndi machitidwe ake woopsa pa Nyanja Yofiira.
23Choncho Iye anawawuza kuti adzawawononga,
pakanapanda Mose, mtumiki wake wosankhidwa,
kuyima pamaso pake,
ndi kuletsa mkwiyo wake kuti usawawononge.
24Motero iwo ananyoza dziko lokoma;
sanakhulupirire malonjezo ake.
25Anangʼungʼudza mʼmatenti mwawo
ndipo sanamvere Yehova.
26Kotero Iye analumbira atakweza dzanja lake,
kuti adzachititsa kuti iwowo afere mʼchipululu,
27kuchititsa kuti zidzukulu zawo zifere pakati pa anthu a mitundu ina
ndi kuwabalalitsa mʼdziko lonse.
28Iwo anayamba kupembedza Baala-Peori
ndi kudya nsembe zoperekedwa kwa milungu yopanda moyo;
29anaputa mkwiyo wa Yehova pa machitidwe awo oyipa,
ndipo mliri unabuka pakati pawo.
30Koma Finehasi anayimirira ndi kulowererapo,
ndipo mliri unaleka.
31Chimenechi ndicho chinayesedwa chilungamo chake,
kwa mibado yosatha imene ikubwera.
32Pa madzi a ku Meriba iwo anakwiyitsa Yehova
ndipo mavuto anabwera kwa Mose chifukwa cha anthuwo,
33pakuti iwowo anawukira mzimu wa Mulungu,
ndipo pa milomo ya Mose panatuluka mawu osayenera.
34Aisraeliwo sanawononge mitundu ya anthu
monga momwe Yehova anawalamulira.
35Koma anasakanizana ndi anthu a mitundu inayo
ndi kuphunzira miyambo yawo.
36Ndipo anapembedza mafano awo,
amene anakhala msampha kwa iwowo.
37Anapereka nsembe ana awo aamuna
ndi ana awo aakazi kwa ziwanda.
38Anakhetsa magazi a anthu osalakwa,
magazi a ana awo aamuna ndi a ana awo aakazi,
amene anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanaani,
ndipo dziko linayipitsidwa ndi magazi awo.
39Iwo anadzidetsa okha ndi zimene anachita;
ndi machitidwe awo amakhala ngati munthu wachigololo.
40Tsono Yehova anakwiya ndi anthu ake
ndipo ananyansidwa ndi cholowa chake.
41Iye anawapereka kwa anthu a mitundu ina,
ndipo adani awo anawalamulira.
42Adani awo anawazunza
ndi kuwakhazika pansi pa mphamvu yawo.
43Iye ankawapulumutsa nthawi zambiri,
koma iwo ankatsimikiza za kuwukira
ndipo anawonongeka mʼmachimo awo.
44Koma Iye anaona kuzunzika kwawo
pamene anamva kulira kwawo;
45Chifukwa cha iwo Iye anakumbukira pangano lake
ndipo anawalezera mtima chifukwa cha kukula kwa chikondi chake.
46Iye anachititsa kuti amene anawagwira iwo ukapolo
awamvere chisoni.
47Tipulumutseni Inu Yehova Mulungu wathu,
ndipo mutisonkhanitse kuchoka kwa anthu a mitundu ina
kuti tithe kuyamika dzina lanu loyera
ndi kunyadira mʼmatamando anu.
48Atamandike Yehova, Mulungu wa Israeli,
Kuyambira muyaya mpaka muyaya.
Anthu onse anene kuti, “Ameni!”
Tamandani Yehova.
Currently Selected:
Masalimo 106: CCL
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Word of God in Contemporary Chichewa
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®
Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®
Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.