Luka 9
9
Yesu Atuma Ophunzira ake Khumi ndi Awiri
1Yesu atawayitana khumi ndi awiriwo pamodzi, Iye anawapatsa mphamvu ndi ulamuliro wotulutsa ziwanda zonse ndi kuchiritsa matenda. 2Ndipo Iye anawatumiza kukalalikira za ufumu wa Mulungu ndi kukachiritsa odwala. 3Iye anawawuza kuti, “Musatenge kanthu paulendo. Musatenge ndodo, thumba, buledi, ndalama, ndi malaya apadera. 4Nyumba iliyonse imene mulowa, mukhale momwemo kufikira mutachoka mu mzindawo. 5Ngati anthu sakulandirani, sasani fumbi la kumapazi anu pomwe mukuchoka mu mzinda wawo ngati umboni owatsutsa.” 6Ndipo iwo ananyamuka napita, mudzi ndi mudzi, kulalikira Uthenga Wabwino ndi kuchiritsa anthu paliponse.
7Tsopano Herode olamulirayo anamva zonse zimachitikazi. Ndipo iye anavutika kwambiri chifukwa ena amati Yohane waukitsidwa kwa akufa, 8ena amati Eliya waonekera, ndipo ena anatinso mmodzi wa aneneri akalekale waukanso. 9Koma Herode anati, “Ine ndinamudula mutu Yohane. Nanga uyu ndani amene ndikumva zinthu zotere za Iye?” Ndipo iye anayesetsa kuti amuone Iye.
Yesu Adyetsa Anthu 5,000
10Atumwi atabwerera, anamuwuza Yesu zimene anachita. Kenaka Iye anawatenga napita kwa okha ku mudzi wa Betisaida. 11Koma gulu la anthu linadziwa ndipo anamutsatira. Iye anawalandira ndi kuyankhula nawo za ufumu wa Mulungu, ndi kuchiritsa amene amafuna machiritso.
12Chakumadzulo dzuwa litapita, khumi ndi awiriwo anabwera kwa Iye ndipo anati, “Uzani gulu la anthuli lichoke kuti apite ku midzi yotizungulira ndi madera a ku mudzi kuti akapeze chakudya ndi pogona, chifukwa kuno ndi kuthengo.”
13Iye anayankha kuti, “Apatseni chakudya kuti adye.”
Iwo anayankha kuti, “Ife tili ndi malofu a buledi asanu okha ndi nsomba ziwiri, pokhapokha titapita kukagula chakudya cha gulu la anthu onsewa.” 14(Pamenepo panali amuna pafupifupi 5,000).
Koma Iye anati kwa ophunzira ake, “Akhazikeni pansi mʼmagulu a anthu pafupifupi makumi asanu.” 15Ophunzira ake anachita zomwezo ndipo aliyense anakhala pansi. 16Atatenga malofu a buledi asanu ndi nsomba ziwiri zija anayangʼana kumwamba, nayamika ndipo anazigawa. Kenaka anazipereka kwa ophunzira ake kuti azipereke kwa anthu. 17Onse anadya nakhuta, ndipo ophunzira ake anatolera madengu khumi ndi awiri odzaza ndi nyenyeswa zomwe zinatsala.
Petro Avomereza Khristu
18Nthawi ina pamene Yesu amapemphera malo a yekha ali ndi ophunzira ake, Iye anawafunsa kuti, “Kodi anthu amati Ine ndine yani?”
19Iwo anayankha kuti, “Ena amati Yohane Mʼbatizi; ena amati Eliya; ndipo enanso amati mmodzi wa aneneri akalekale waukanso.”
20Iye anafunsa kuti, “Koma nanga inu mumati Ine ndine yani?”
Petro anayankha kuti, “Mpulumutsi wolonjezedwa uja wa Mulungu.”
Yesu Aneneratu za Imfa yake
21Yesu anawachenjeza kwambiri kuti asawuze wina aliyense za izi. 22Ndipo Iye anati, “Mwana wa Munthu ayenera kuzunzika kwambiri ndi kukanidwa ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, Iye ayenera kuphedwa ndipo tsiku lachitatu adzauka kwa akufa.”
23Ndipo Iye anawuza onse kuti, “Ngati wina aliyense akufuna kutsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kusenza mtanda wake tsiku ndi tsiku nʼkumanditsata Ine. 24Popeza aliyense amene akufuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene adzataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupulumutsa. 25Kodi chabwino ndi chiti kwa munthu, kupata zonse zapansi pano, koma ndi kutaya moyo wake kapena kudziwononga iye mwini? 26Ngati wina aliyense achita nane manyazi ndi ndiponso mawu anga, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wake ndi mu ulemerero wa Atate ndi angelo oyera. 27Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti ena mwa inu amene mwayima pano simudzalawa imfa musanaone ufumu wa Mulungu.”
Maonekedwe a Ulemerero wa Yesu pa Phiri
28Patatha pafupifupi masiku asanu ndi atatu Yesu atanena izi, Iye anatenga Petro, Yohane ndi Yakobo ndi kukwera ku phiri kukapemphera. 29Pamene Iye ankapemphera, maonekedwe a nkhope yake, ndi zovala zake zinawala monyezimira kwambiri. 30Anthu awiri, Mose ndi Eliya, 31anaonekera mu ulemerero opambana akuyankhulana ndi Yesu. Iwo amayankhulana za kuchoka kwake, kumene Iye anali pafupi kukakwaniritsa ku Yerusalemu. 32Petro ndi anzake anali ndi tulo tambiri, koma atadzuka, iwo anaona ulemerero wake ndi anthu awiri atayima pamodzi ndi Iye. 33Pamene anthuwo ankamusiya Yesu, Petro anati kwa Iye, “Ambuye, ndi chabwino kwa ife kuti tikhale pano. Tiloleni kuti timange misasa itatu, umodzi wanu, umodzi wa Mose ndi umodzi wa Eliya.” (Iye sanadziwe chimene amayankhula).
34Pamene Iye ankayankhula, mtambo unaonekera ndi kuwaphimba iwo, ndipo anachita mantha pamene mtambowo unawakuta. 35Mawu anachokera mu mtambomo nati, “Uyu ndi Mwana wanga amene ndamusankha; mumvereni Iye.” 36Atamveka mawuwa, anaona kuti Yesu anali yekha. Ophunzirawo anazisunga izi mwa iwo okha ndipo sanawuze wina aliyense pa nthawiyi za zomwe iwo anaziona.
Kuchiritsidwa kwa Mwana Wogwidwa ndi Chiwanda
37Mmawa mwake, akutsika ku phiri, anthu ambiri anakumana naye. 38Munthu wina mʼgulu la anthulo anayitana kuti, “Aphunzitsi, ndikupemphani kuti muone mwana wangayu, pakuti ndi mmodzi yekhayu. 39Chiwanda chikamugwira amafuwula mwadzidzidzi; chimamugwedeza kolimba mpaka kutuluka thovu kukamwa. Sichimusiya ndipo chikumuwononga. 40Ine ndinapempha ophunzira anu kuti achitulutse, koma alephera.”
41Yesu anayankha kuti, “Haa! Anthu osakhulupirira ndi mʼbado wokhota. Kodi Ine ndidzakhala nanu nthawi yayitali yotani ndi kukupirirani? Bweretsa mwana wako kuno.”
42Ngakhale pamene mnyamata amabwera kwa Yesu, chiwandacho chinamugwetsa pansi ndi kumugwedeza. Koma Yesu anadzudzula mzimu woyipawo nachiritsa mwa mnyamatayo ndi kumuperekanso kwa abambo ake. 43Ndipo iwo onse anadabwa ndi ukulu wa Mulungu.
Yesu Abwereza Kunena za Imfa yake
Aliyense akudabwa ndi zimene Yesu anachita, Iyeyo anati kwa ophunzira ake, 44“Tamvetsetsani zimene ndikufuna kukuwuzani: Mwana wa Munthu akupita kukaperekedwa mʼmanja mwa anthu.” 45Koma iwo sanazindikire zimene amatanthauza. Izi zinawadabwitsa kotero sanathe kuzimvetsa ndipo anaopa kumufunsa.
Wamkulu Ndani?
46Mkangano unayambika pakati pa ophunzira wa kuti wamkulu koposa akanakhala ndani mwa iwo. 47Yesu podziwa maganizo awo, anatenga kamwana nakayimika pambali pake. 48Ndipo Iye anawawuza kuti, “Aliyense wolandira bwino kamwana aka mʼdzina langa, ndiye kuti akulandiranso bwino Ine; ndipo aliyense wolandira bwino Ine, ndiye kuti akulandiranso bwino amene anandituma Ine. Pakuti amene ndi wamngʼono pakati panu, ndiye amene ali wamkulu koposa.”
49Yohane anati, “Ambuye, ife tinaona munthu akutulutsa ziwanda mʼdzina lanu ndipo tinayesa kumuletsa, chifukwa iyeyo si mmodzi wa ife.”
50Yesu anati, “Wosamuletsa, pakuti amene satsutsana nanu ali mbali yanu.”
A Samariya Akana Yesu
51Nthawi itayandikira yoti Iye atengedwe kupita kumwamba, Yesu anatsimikiza zopita ku Yerusalemu, 52ndipo anatuma nthumwi kuti zitsogole. Iwo anapita mʼmudzi wa Asamariya kuti akonzekere kumulandira, 53koma anthu kumeneko sanamulandire chifukwa Iye ankapita ku Yerusalemu. 54Ophunzira awa, Yohane ndi Yakobo ataona zimenezi, anafunsa kuti, “Ambuye, kodi mukufuna ife tiyitane moto kuchokera kumwamba kuti uwawononge?” 55Koma Yesu anatembenuka ndi kuwadzudzula, 56ndipo iwo anapita ku mudzi wina.
Kutsatira Yesu
57Pamene iwo ankayenda mu msewu, munthu wina anati kwa Iye, “Inu ndikutsatirani kulikonse kumene mudzapita.”
58Yesu anayankha kuti, “Nkhandwe zili ndi mapanga ake, mbalame zili ndi zisa zake, koma Mwana wa Munthu alibe malo wogonekapo mutu wake.”
59Iye anati kwa wina, “Nditsate Ine.”
Koma munthuyo anayankha kuti, “Ambuye, choyamba loleni ndipite kuti ndikayike maliro a abambo anga.”
60Yesu anati kwa iye, “Aleke akufa ayikane akufa okhaokha, koma iwe pita ukalalikire ufumu wa Mulungu.”
61Koma winanso anati, “Ine ndidzakutsatani Ambuye; koma choyamba ndiloleni ndibwerere kuti ndikatsanzikane nalo banja langa.”
62Yesu anayankha kuti, “Munthu amene akulima ndi khasu lokokedwa nʼkumayangʼana mʼmbuyo, si woyenera kugwira ntchito mu ufumu wa Mulungu.”
Currently Selected:
Luka 9: CCL
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Word of God in Contemporary Chichewa
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®
Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®
Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.