Luka 19
19
Zakeyu Apulumutsidwa
1Yesu analowa mu Yeriko napitirira. 2Kunali munthu kumeneko dzina lake Zakeyu; iye anali mkulu wa wolandira msonkho ndipo anali wolemera. 3Iye ankafuna kuona Yesu kuti ndani, koma pokhala wamfupi sanathe chifukwa cha gulu la anthu. 4Choncho iye anathamangira patsogolo ndipo anakwera mu mtengo wamkuyu kuti amuone Iye, pakuti Yesu ankadutsa njira imeneyo.
5Yesu atafika pa malopo, anayangʼana mmwamba ndipo anati kwa iye, “Zakeyu, tsika msangamsanga. Ine ndiyenera kukhala mʼnyumba mwako lero.” 6Ndipo nthawi yomweyo anatsika ndipo anamulandira mosangalala.
7Anthu onse ataona zimenezi anayamba kungʼungʼudza, nati, “Iye akupita kuti akakhale mlendo wa wochimwa.”
8Koma Zakeyu anayimirira ndipo anati kwa Ambuye, “Taonani Ambuye! Theka la chuma changa ndipereka kwa osauka ndipo ngati ndinamubera wina aliyense pa chilichonse, ndidzamubwezera mochulukitsa kanayi.”
9Yesu anati kwa iye, “Lero chipulumutso chafika mʼnyumba ino, chifukwa munthu uyu nayenso ndi mwana wa Abrahamu. 10Pajatu Mwana wa Munthu anabwera kudzafunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.”
Antchito Opindula Mosiyana
11Pamene iwo ankamvera izi, Iye anapitiriza kuwawuza fanizo, chifukwa Iye anali kufupi ndi Yerusalemu ndipo anthu ankaganiza kuti ufumu wa Mulungu ukanaoneka nthawi yomweyo. 12Iye anati, “Munthu wa banja laufumu anapita ku dziko lakutali kukadzozedwa ufumu ndipo kenaka abwerenso kwawo. 13Tsono iye anayitana antchito ake khumi ndi kuwapatsa ndalama khumi. Iye anati, ‘Gwiritsani ntchito ndalama izi mpaka nditabwerera.’
14 “Koma anthu ake anamuda ndipo anatuma nthumwi pambuyo pake kukanena kuti, ‘Sitikufuna munthuyu kuti akhale mfumu yathu.’
15 “Iye analandira ufumuwo ngakhale zinali zotero, ndipo anabwerera kwawo. Kenaka iye anatumiza uthenga kwa antchito ake amene anawapatsa ndalama aja, ndi cholinga chakuti adziwe chimene anapindula nazo.
16 “Woyamba anabwera ndipo anati, ‘Bwana ndalama zanu zapindula khumi zina.’
17 “Bwana wakeyo anayankha kuti, Wachita bwino wantchito wabwino. ‘Chifukwa wakhulupirika pa zinthu zazingʼono, lamulira mizinda khumi.’
18 “Wachiwiri anabwera ndipo anati, ‘Bwana, ndalama zanu zapindula zisanu zina.’
19 “Bwana anayankha kuti, ‘Iwe lamulira mizinda isanu.’
20 “Kenaka wantchito wina anabwera ndipo anati, ‘Bwana, ndalama yanu nayi; ine ndinayibisa ndi kuyisunga mʼkansalu. 21Ine ndimakuopani, chifukwa ndinu munthu wowuma mtima. Inu mumatenga chimene simunachiyike ndi kukolola chimene simunadzale.’
22 “Bwana wake anayankha kuti, ‘Ine ndikukuweruza iwe ndi mawu ako omwewo. Ndiwe wantchito woyipa. Kani umadziwa kuti ndine munthu wowuma mtima ndi wotenga chimene sindinasungitse, ndi kukolola chimene sindinadzale? 23Nanga nʼchifukwa chiyani sunasungitse ndalama yanga, kuti ine pobwera, ndidzayitenge ndi chiwongoladzanja?’
24 “Ndipo iye anawuza amene anayimirira pafupi kuti, ‘Tengani ndalama yake ndi kumupatsa amene ali ndi ndalama khumiyo!’ ”
25 Iwo anati, “Bwana iyeyu ali nazo kale khumi!”
26 Iye anayankha kuti, “Ndikukuwuzani kuti, aliyense amene ali nazo, adzapatsidwa zambiri, koma amene alibe, adzalandidwa ngakhale chimene ali nacho. 27Tsono adani anga aja amene sankafuna kuti ndikhale mfumu yawo, abweretseni pano ndi kuwapha ine ndikuona.”
Yesu Alowa mu Yerusalemu Mwaulemerero
28Yesu atatha kunena izi, anayendabe kupita ku Yerusalemu. 29Iye atayandikira ku Betifage ndi Betaniya pa phiri lotchedwa Olivi, Iye anatuma awiri a ophunzira nati kwa iwo, 30“Pitani mʼmudzi uli patsogolo panu, mukakalowa mʼmudzimo, mukapeza mwana wabulu womangiriridwa amene wina aliyense sanakwerepo. Mukamumasule ndi kubwera naye kuno. 31Ngati wina aliyense akakufunsani kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mukumumasula mwana buluyo?’ Mukamuwuze kuti, ‘Ambuye akumufuna.’ ”
32Otumidwawo anapita nakamupeza mwana wabulu monga momwe Yesu anawawuzira. 33Pamene ankamasula mwana wabuluyo, eni ake anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukumasula mwana wabuluyo?”
34Iwo anayankha kuti, “Ambuye akumufuna.”
35Iwo anabweretsa buluyo kwa Yesu, naponya zovala zawo pa bulupo ndi kumukwezapo Yesu. 36Pamene ankapita, anthu anayala zovala zawo mu msewu.
37Iye atafika pafupi ndi pamene msewu umatsikira ku phiri la Olivi, gulu lonse la ophunzira linayamba kuyamika Mulungu mwachimwemwe ndi mawu ofuwula chifukwa cha zodabwitsa zonse anaziona.
38“Yodala mfumu imene ikubwera mʼdzina la Ambuye!”
“Mtendere kumwamba ndi ulemerero mmwambamwamba!”
39Ena mwa Afarisi mʼgulumo anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, adzudzuleni ophunzira anu!”
40Iye anayankha kuti, “Ine ndikukuwuzani kuti, ngati atakhala chete, miyala idzafuwula.”
41Iye atayandikira ku Yerusalemu ndi kuona mzindawo, anawulirira 42nati, “Iwe ukanadziwa lero lino zinthu zokubweretsera mtendere, koma tsopano zabisikira maso ako. 43Pakuti masiku adzabwera pamene adani ako adzamanga mitumbira yankhondo nakuzungulira, nadzakutsekereza mbali zonse. 44Iwo adzakugwetsera pansi, iwe, ana ako onse a mʼkati mwako. Iwo sadzasiya mwa iwe mwala wina pa unzake, chifukwa sunazindikire nthawi ya kubwera kwa Mulungu.”
Yesu mʼNyumba ya Mulungu
45Kenaka Iye analowa mʼdera la Nyumba ya Mulungu ndi kuyamba kutulutsa kunja amene amachita malonda. 46Iye anawawuza kuti, “Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzakhala nyumba ya mapemphero, koma inu mwayisadutsa phanga la achifwamba.”
47Tsiku lililonse amaphunzitsa mʼNyumba ya Mulungu. Koma akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo ndi atsogoleri pakati pa anthu amayesetsa kuti amuphe. 48Komabe iwo sanathe kupeza njira ina iliyonse kuti achite izi, chifukwa anthu onse anakhulupirira mawu ake.
Currently Selected:
Luka 19: CCL
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Word of God in Contemporary Chichewa
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®
Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®
Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.