YouVersion Logo
Search Icon

Genesis 27

27
Yakobo Alandira Madalitso kwa Isake
1Isake atakalamba maso ake anachita khungu mwakuti sankatha kuona. Iye anayitana mwana wake wamkulu Esau nati kwa iye, “Mwana wanga.”
Iye anayankha, “Ine abambo.”
2Isake anati, “Tsopano ine ndakalamba, ndipo sindidziwa tsiku langa lakufa. 3Tsono tenga zida zako, muvi wako ndi uta, pita kuthengo ukandiphere nyama. 4Undikonzere chakudya chabwino monga muja ndimakonderamu ndipo ubwere nacho kwa ine kuti ndidye ndi kuti ndikudalitse ndisanamwalire.”
5Koma Rebeka amamvetsera pamene Isake amayankhula ndi mwana wake Esau. Esau atanyamuka kupita kuthengo kukaphera abambo ake nyama, 6Rebeka anati kwa mwana wake Yakobo, “Taona ndamva abambo ako akuwuza mʼbale wako Esau kuti, 7‘Bweretsere nyama yakutchire ndipo undikonzere chakudya chokoma kuti ndidye; kuti ndikudalitse pamaso pa Yehova ndisanamwalire.’ 8Tsopano mwana wanga, mvetsetsa ndipo uchite zimene ndikuwuze: 9Pita ku khola, ukatenge ana ambuzi abwino awiri, kuti ndikonzere abambo ako chakudya chokoma monga amakondera. 10Kenaka upite nacho chakudyacho kwa abambo ako kuti adye ndi kukudalitsa asanafe.”
11Koma Yakobo anati kwa Rebeka amayi ake, “Komatu mʼbale wanga Esau ndi munthu wa khungu la ubweya zedi, ndipo ine ndine munthu wa khungu losalala. 12Mwina abambo anga adzandikhudza, ndipo ndidzaoneka kuti ndawapusitsa. Tsono ndizadzitengera temberero mʼmalo mwa madalitso.”
13Amayi ake anati kwa iye, “Mwana wanga, temberero limenelo ligwere ine. Iwe ungochita zimene ine ndikukuwuza; pita kanditengere timbuzito.”
14Choncho anapita nakatenga timbuzito ndi kubwera nato kwa amayi ake. Choncho Rebeka anaphika chakudya chokoma monga momwe Isake amakondera. 15Tsono Rebeka anatenga zovala zabwino kwambiri za Esau mwana wake wamkulu zimene zinali mʼnyumba namuveka Yakobo. 16Anamuvekanso manja ake ndi khosi lake ndi zikopa za mwana wambuzi. 17Kenaka, anamupatsa Yakobo chakudya chokoma chija chimene anaphika pamodzi ndi buledi.
18Yakobo anapita kwa abambo ake ndipo anati, “Abambo anga.”
Ndipo anayankha, “Eya, kodi ndiwe mwana wanga uti?”
19Yakobo anati kwa abambo ake, “Ndine Esau mwana wanu woyamba. Ndachita monga munandiwuzira. Chonde dzukani ndi kukhala tsonga kuti mudyeko nyama ndakukonzeraniyi kuti tsono mundidalitse.”
20Isake anafunsa mwana wake, “Wayipeza msanga chotere bwanji mwana wanga?”
Iye anayankha, “Yehova Mulungu wanu anandithandiza kuti ndiyipeze.”
21Pamenepo Isake anati kwa Yakobo, “Tabwera pafupi ndikukhudze mwana wanga, kuti ndidziwedi ngati uli mwana wanga Esau kapena ayi.”
22Yakobo anasendera kufupi ndi abambo ake Isake ndipo anamukhudza nati, “Mawuwa ndi mawu a Yakobo koma mikonoyi ndi mikono ya Esau.” 23Sanamuzindikire, popeza mikono yake inali ndi ubweya ngati ya mʼbale wake Esau; choncho anamudalitsa. 24Isake anafunsa, “Kodi ndiwedi mwana wanga Esau?”
Yakobo anayankha, “Inde ndine.”
25Ndipo iye anati, “Mwana wanga, patseko nyama yakoyo ndidye kuti ndikudalitse.”
Yakobo anabwera ndi nyama ija kwa Isake ndipo anadya. Kenaka anamupatsanso vinyo ndipo anamwa. 26Tsono Isake anati kwa Yakobo, “Bwera kuno mwana wanga undipsompsone.”
27Choncho anapita namupsompsona. Apa Isake anamva fungo la zovala zake, ndipo anamudalitsa nati,
“Haa, fungo la mwana wanga
lili ngati fungo la munda
umene Yehova waudalitsa.
28Mulungu akugwetsere mame akumwamba
ndipo minda yako ibale tirigu wambiri
ndi vinyo watsopano.
29Mitundu ya anthu ikutumikire iwe
ndipo anthu akugwadire iwe.
Ukhale wolamula abale ako,
ndipo ana aamuna a amayi ako akugwadire.
Amene akutemberera iwe atembereredwe
ndipo amene adalitsa iwe adalitsike.”
30Isake atatsiriza kudalitsa Yakobo, atangochoka pamaso pa abambo akewo, Esau anabwera kuchokera kosaka kuja. 31Nayenso anakonza chakudya chokoma nabwera nacho kwa abambo ake. Ndipo anati kwa iye, “Chonde abambo, dzukani mukhale tsonga kuti mudye nyamayi ndi kuti mundidalitse.”
32Abambo ake, Isake, anamufunsa kuti, “Ndiwe yani?”
Iye anayankha, “Ndine mwana wanu woyamba Esau.”
33Isake ananjenjemera kwambiri nati, “Nanga ndani uja anakapha nyama kutchire nʼkudzandipatsa? Ine ndadya kale, ndadya nyamayo iwe utangotsala pangʼono kubwera ndipo ndamudalitsa ndipo adzakhaladi wodalitsika.”
34Esau atamva mawu a abambo ake, analira mokweza ndi mowawidwa mtima nati kwa abambo ake, “Inenso dalitseni abambo anga!”
35Koma iye anati, “Mʼbale wako anabwera mwachinyengo ndipo watenga madalitso ako.”
36Esau anati, “Kodi nʼchifukwa chake iyeyu dzina lake lili Yakobo eti? Aka nʼkachiwiri kundinyenga: Anatenga ukulu wanga, pano watenga madalitso anga!” Kenaka anafunsa, “Kodi simunandisungireko ena madalitsowo?”
37Koma Isake anamuyankha nati, “Ndamudalitsa iye kuti akhale wokulamulira iwe. Ndaperekanso abale ake onse kuti akhale omutumikira iye, ndipo ndamudalitsa ndi tirigu wambiri, ndi vinyo watsopano. Ndiye ndingakuchitirenso chiyani mwana wanga?”
38Esau anati kwa abambo ake, “Kodi muli ndi dalitso limodzi lokhali, abambo anga? Inenso mundidalitse chonde abambo anga!” Pomwepo Esau analira mokuwa.
39Tsono Isake abambo ake anamuyankha kuti,
“Malo ako okhalapo
sadzabala dzinthu,
ndipo mvula sidzagwa pa minda yako.
40Udzakhala ndi moyo podalira lupanga
ndipo udzatumikira mʼbale wako.
Koma idzafika nthawi
pamene udzakhala mfulu
udzachotsa goli lake mʼkhosi mwako.”
Yakobo Athawira kwa Labani
41Ndipo Esau anamusungira chiwembu Yakobo chifukwa cha madalitso amene abambo ake anamupatsa. Esau anati kwa iye yekha, “Masiku olira abambo anga ayandikira; pambuyo pake ndidzamupha mʼbale wangayu Yakobo.”
42Pamene Rebeka anamva zimene mwana wake wamkulu Esau ankaganiza, anayitanitsa Yakobo nati kwa iye, “Mʼbale wako Esau akulingalira zakuti akuphe kuti akulipsire. 43Tsopano mwana wanga, chita zimene ndinene: Nyamuka tsopano, uthawire kwa mlongo wanga Labani ku Harani. 44Ukakhale naye kwa kanthawi mpaka mkwiyo wa mʼbale wako utatsika. 45Tsono mkwiyo wa mʼbale wakoyo ukadzatsika ndi kuyiwala zonse wamuchitirazi, ndidzatuma munthu kuti adzakutenge. Nanga nditayirenji nonse awiri nthawi imodzi?”
46Tsono Rebeka anati kwa Isake, “Ine sindikukondwera nawo anamwali a Chihiti. Ndipo ngati Yakobo angapeze mbeta kuno mwa anamwali a Chihitiwa, ndiye kuli bwino kungofa.”

Currently Selected:

Genesis 27: CCL

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in