Genesis 27:28-29
Genesis 27:28-29 CCL
Mulungu akugwetsere mame akumwamba ndipo minda yako ibale tirigu wambiri ndi vinyo watsopano. Mitundu ya anthu ikutumikire iwe ndipo anthu akugwadire iwe. Ukhale wolamula abale ako, ndipo ana aamuna a amayi ako akugwadire. Amene akutemberera iwe atembereredwe ndipo amene adalitsa iwe adalitsike.”