MATEYU 5
5
Chiphunzitso cha paphiri. Madalitso
(Luk. 6.20-49)
1 #
Mat. 15.29
Ndipo m'mene Iye anaona makamu, anakwera m'phiri; ndipo m'mene Iye anakhala pansi, anadza kwa Iye ophunzira ake; 2ndipo anatsegula pakamwa, nawaphunzitsa iwo, nati:
3 #
Miy. 29.23; Yes. 66.2; Luk. 6.20 Odala ali osauka mumzimu; chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.
4 #
Yes. 61.2-3; Luk. 6.21; Yoh. 16.20 Odala ali achisoni; chifukwa adzasangalatsidwa.
5 #
Mas. 37.11
Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.
6 #
Mas. 42.1-2; Yes. 55.1-2 Odala ali akumva njala ndi ludzu la chilungamo; chifukwa adzakhuta.
7 #
Mat. 6.14; Mrk. 11.25; Aheb. 6.10 Odala ali akuchitira chifundo; chifukwa adzalandira chifundo.
8 #
Aheb. 12.14; 1Yoh. 3.2, 3 Odala ali oyera mtima; chifukwa adzaona Mulungu.
9 #
Yak. 3.18
Odala ali akuchita mtendere; chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.
10 #
2Ako. 4.17
Odala ali akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo: chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba. 11#Luk. 6.22; 1Pet. 4.14Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha Ine.
12 #
Luk. 6.23; Mac. 7.52 Sekerani, sangalalani: chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu mu Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.
Ophunzira ake ali mchere wa dziko ndi kuunika kwa dziko
13 #
Luk. 14.34, 35 Inu ndinu mchere wa dziko lapansi; koma mcherewo ngati ukasukuluka, adzaukoleretsa ndi chiyani? Pamenepo sungakwanirenso kanthu konse, koma kuti ukaponyedwe kunja, nupondedwe ndi anthu.
14 #
Aef. 5.8
Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mzinda wokhazikika pamwamba paphiri sungathe kubisika. 15#Luk. 8.16Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m'nyumbamo. 16#1Pet. 2.12Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.
Makwaniridwe a Malamulo ndi Aneneri
17 #
Aro. 3.31
Musaganize kuti ndinadza Ine kudzapasula chilamulo kapena aneneri: sindinadze kupasula, koma kukwaniritsa. 18#Luk. 16.17Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang'ono kamodzi kapena kansonga kake kamodzi sikadzachokera kuchilamulo, kufikira zitachitidwa zonse. 19#Yak. 2.10Chifukwa chake yense wakumasula limodzi la malamulo amenewa ang'onong'ono, nadzaphunzitsa anthu chomwecho, adzatchulidwa wamng'onong'ono mu Ufumu wa Kumwamba; koma yense wakuchita ndi kuphunzitsa awa, iyeyu adzatchulidwa wamkulu mu Ufumu wa Kumwamba. 20Pakuti ndinena ndi inu, ngati chilungamo chanu sichichuluka choposa cha alembi ndi Afarisi, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.
21 #
Eks. 20.13
Munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usaphe; koma yense wakupha adzakhala wopalamula mlandu: 22#1Yoh. 3.15koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.
23Chifukwa chake ngati ulikupereka mtulo wako paguwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe, 24usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nuchoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako. 25#Luk. 12.58-59Fulumira kuyanjana ndi mnzako wamlandu, pamene uli naye panjira; kapena mnzako wamlandu angakupereke iwe kwa woweruza mlandu, ndi woweruzayo angapereke iwe kwa msilikali, nuponyedwe iwe m'nyumba yandende. 26#Luk. 12.58-59Indetu ndinena ndi iwe, sudzatulukamo konse, koma utalipa kakobiri kakumaliza ndiko.
27 #
Eks. 20.14
Munamva kuti kunanenedwa, Usachite chigololo; 28#2Sam. 11.2koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.
29 #
Mat. 18.8-9
Koma ngati diso lako lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe, kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losaponyedwa thupi lako lonse mu Gehena. 30#Mat. 18.8-9Ndipo ngati dzanja lako lamanja likulakwitsa iwe, ulidule, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losamuka thupi lako lonse ku Gehena.
31 #
Deut. 24.1
Kunanenedwanso, Yense wakuchotsa mkazi wake ampatse iye kalata yachilekaniro: 32#Mat. 19.9koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuchotsa mkazi wake, kosati chifukwa cha chigololo, amchititsa chigololo: ndipo amene adzakwata wochotsedwayo achita chigololo.
33 #
Lev. 19.12
Ndiponso, munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usalumbire konama, koma udzapereka kwa Ambuye zolumbira zako: 34#Yak. 5.12koma Ine ndinena kwa inu, Musalumbire konse, kapena kutchula Kumwamba, chifukwa kuli chimpando cha Mulungu; 35#Yak. 5.12kapena kutchula dziko lapansi, chifukwa lili popondapo mapazi ake; kapena kutchula Yerusalemu, chifukwa kuli mzinda wa Mfumu yaikulukulu. 36#Yak. 5.12Kapena usalumbire kumutu wako, chifukwa sungathe kuliyeretsa mbuu kapena kulidetsa bii tsitsi limodzi. 37#Yak. 5.12Koma manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iai, iai; ndipo choonjezedwa pa izo chichokera kwa woipayo.
38 #
Eks. 21.24
Munamva kuti kunanenedwa, Diso kulipa diso, ndi dzino kulipa dzino: 39#Miy. 20.22; Aro. 12.17, 19koma ndinena kwa inu, Musakanize munthu woipa; koma amene adzakupanda iwe pa tsaya lako lamanja, umtembenuzire linanso. 40Ndipo kwa iye wofuna kupita nawe kumlandu ndi kutenga malaya ako, umlolezenso chofunda chako. 41#Mrk. 15.21Ndipo amene akakukakamiza kumperekeza njira imodzi, upite naye ziwiri. 42#Deut. 15.8, 10Kwa iye wopempha iwe umpatse, ndipo kwa iye wofuna kukukongola usampotolokere.
43 #
Aro. 12.14, 20 Munamva kuti kunanenedwa, Uzikondana ndi mnansi wako, ndi kumuda mdani wako: 44#Mac. 7.60; Aro. 12.14, 20koma Ine ndinena kwa inu, Kondanani nao adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu; 45kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa Kumwamba; chifukwa Iye amakwezera dzuwa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama. 46#Luk. 6.32Chifukwa kuti ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho? 47Ndipo ngati mupatsa moni abale anu okhaokha, muchitanji choposa ena? Kodi angakhale anthu akunja sachita chomwecho? 48#Akol. 4.12; Aef. 5.1; 1Pet. 1.15-16Chifukwa chake inu mukhale angwiro, monga Atate wanu wa Kumwamba ali wangwiro.
Currently Selected:
MATEYU 5: BLP-2018
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi