YouVersion Logo
Search Icon

MATEYU 3

3
Yohane Mbatizi
(Mrk. 1.1-8; Luk. 3.1-18; Yoh. 1.19-28)
1 # Mrk. 1.4, 15; Luk. 3.2-3; Yoh. 1.28 Ndipo masiku aja anadza Yohane Mbatizi, nalalikira m'chipululu cha Yudeya, 2#Mat. 4.17nanena, Tembenukani mitima; chifukwa Ufumu wa Kumwamba wayandikira. 3#Yes. 40.3; Mrk. 1.3; Luk. 1.76; 3.4; Yoh. 1.23Pakuti uyu ndiye ananenayo Yesaya mneneri, kuti,
Mau a wofuula m'chipululu,
konzani khwalala la Ambuye,
lungamitsani njira zake.
4 # 2Maf. 1.8 Ndipo Yohane yekhayo anali nacho chovala chake cha ubweya wangamira, ndi lamba lachikopa m'chuuno mwake; ndi chakudya chake chinali dzombe ndi uchi wakuthengo. 5#Mrk. 1.5Pamenepo panamtulukira iye a ku Yerusalemu, ndi Yudeya yense, ndi dziko lonse loyandikana ndi Yordani; 6#Mac. 19.4, 18nabatizidwa ndi iye mu mtsinjewo wa Yordani, alikuwulula machimo ao. 7Ndipo iye pakuona ambiri a Afarisi ndi a Asaduki akudza ku ubatizo wake, anati kwa iwo, Obadwa a njoka inu, ndani anakulangizani kuthawa mkwiyo ulinkudza? 8Onetsani inu zipatso zakuyenera kutembenuka mtima: 9#Yoh. 8.33, 39; Mac. 13.26; Aro. 4.1, 11, 16ndipo musamayesa kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye Abrahamu; pakuti ndinena kwa inu kuti mwa miyala iyi Mulungu akhoza kuukitsira Abrahamu ana. 10#Luk. 13.7, 9Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo: chifukwa chake mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino udulidwa nuponyedwa pamoto. 11#Mac. 1.5; 2.3-4Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto: 12#Mala. 3.3chouluzira chake chili m'dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m'nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.
Abatizidwa Yesu
(Mrk. 1.9-11; Luk. 3.21-22; Yoh. 1.31-34)
13 # Mrk. 1.9; Luk. 3.21 Pamenepo Yesu anachokera ku Galileya nadza ku Yordani kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye. 14Koma Yohane anati amkanize, nanena, Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi? 15Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye.
16 # Mrk. 1.10 Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m'madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye; 17#Mas. 2.7; Mrk. 1.11; Luk. 9.35; Akol. 1.13ndipo onani, mau akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.

Currently Selected:

MATEYU 3: BLP-2018

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in