MALAKI 2
2
Mau akutsutsa ansembe
1Ndipo tsono, ansembe inu, lamulo ili ndi la kwa inu. 2#Deut. 28.15-68Mukapanda kumvera, mukapanda kuliika mumtima mwanu, kupatsa dzina langa ulemerero, ati Yehova wa makamu, ndidzakutumizirani temberero, ndi kutemberera madalitso anu; inde, ndawatemberera kale chifukwa simuliika mumtima. 3Taonani, ndidzaipsa mbeu chifukwa cha inu, ndi kuwaza ndowe pankhope panu, ndizo ndowe za nsembe zanu, ndipo adzakuchotsani pamodzi nacho. 4Ndipo mudzadziwa kuti ndatumiza lamulo ili kwa inu, kuti chipangano changa chikhale ndi Levi, ati Yehova wa makamu. 5#Num. 25.12-13Chipangano changa chinali naye cha moyo ndi cha mtendere; ndipo ndinampatsa izi kuti aope; nandiopa, naopsedwa chifukwa cha dzina langa. 6#Deut. 33.10; Yak. 5.20Chilamulo cha zoona chinali m'kamwa mwake, ndi chosalungama sichinapezeke m'milomo mwake; anayenda nane mumtendere ndi moongoka, nabweza ambiri aleke mphulupulu. 7#Ezr. 7.10; Agal. 4.14Pakuti milomo ya wansembe iyenera kusunga chidziwitso, ndi anthu ayenera kufunafuna chilamulo pakamwa pake; pakuti iye ndiye mthenga wa Yehova wa makamu. 8#1Sam. 2.17; Neh. 13.29Koma inu mwapatuka m'njira; mwakhumudwitsa ambiri m'chilamulo; mwaipsa chipangano cha Levi, ati Yehova wa makamu. 9#1Sam. 2.30Chifukwa chake Inenso ndakuikani onyozeka ndi ochepseka kwa anthu onse, popeza simunasunge njira zanga, koma munaweruza mwankhope pochita chilamulo.
Za kukwatira akazi achilendo. Za kuleka mkazi kosayenera
10 #
1Ako. 8.6; Aef. 4.6 Kodi sitili naye Atate mmodzi ife tonse? Sanatilenge kodi Mulungu mmodzi? Tichita monyengezana yense ndi mnzake chifukwa ninji, ndi kuipsa chipangano cha makolo athu? 11Yuda wachita monyenga, ndi mu Israele ndi mu Yerusalemu mwachitika chonyansa; pakuti Yuda waipsa chipatuliko cha Yehova chimene achikonda, nakwatira mwana wamkazi wa mulungu wachilendo. 12Yehova adzalikha munthu wakuchita ichi, wogalamutsa ndi wovomereza m'mahema a Yakobo, ndi iye wopereka chopereka kwa Yehova wa makamu. 13Ndi ichi mubwereza kuchichita: mukuta guwa la nsembe la Yehova ndi misozi, ndi kulira, ndi kuusa moyo; momwemo Iye sasamaliranso chopereka, kapena kulandira mokondwera m'dzanja lanu. 14Koma mukuti, Chifukwa ninji? Chifukwa kuti Yehova anali mboni pakati pa iwe ndi mkazi wa ubwana wako, amene unamchitira chosakhulupirika, chinkana iye ndiye mnzako, mkazi wa pangano lako. 15Ndipo sanatero kodi wina womtsalira mzimu? Ndipo winayo anatero bwanji? Anatero pofuna mbeu ya Mulungu. Koma sungani mzimu wanu; ndipo asamchitire monyenga mkazi wa ubwana wake ndi mmodzi yense. 16Pakuti ndidana nako kuleka kumene, ati Yehova Mulungu wa Israele, ndi iye wakukuta chovala chake ndi chiwawa, ati Yehova wa makamu; chifukwa chake sungani mzimu wanu kuti musachite mosakhulupirika.
17 #
Yes. 43.24
Mwalemetsa Yehova ndi mau anu. Koma mukuti, Tamlemetsa ndi chiyani? Ndi ichi chakuti munena, Yense wakuchita choipa ali wokoma pamaso pa Mulungu, ndipo akondwera nao; kapena, Ali kuti Mulungu wa chiweruzo?
Currently Selected:
MALAKI 2: BLP-2018
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi