LUKA 19
19
Zakeyo asandulika mtima
1Ndipo analowa, napyola pa Yeriko. 2Ndipo taonani, mwamuna wotchedwa dzina lake Zakeyo; ndipo iye anali mkulu wa amisonkho, nali wachuma. 3Ndipo anafuna kuona Yesu ndiye uti, ndipo sanathe, chifukwa cha khamulo, pakuti anali wamfupi msinkhu. 4Ndipo anathamanga, natsogola, nakwera mumkuyu kukamuona Iye; pakuti anati apite njira yomweyi. 5Ndipo m'mene anadza pamalopo Yesu anakweza maso nati kwa iye, Zakeyo, fulumira, nutsike; pakuti lero ndiyenera kukhala m'nyumba mwako. 6Ndipo anafulumira, natsika, namlandira Iye wokondwera. 7#Mat. 9.11Ndipo m'mene anachiona anadandaula onse, nanena, Analowa amchereze munthu ali wochimwa. 8#2Sam. 12.6Ndipo Zakeyo anaimirira nati kwa Ambuye, Taonani, Ambuye, gawo limodzi la zanga zonse zogawika pakati ndipatsa osauka; ndipo ngati ndalanda kanthu kwa munthu monyenga, ndimbwezera kanai. 9#Luk. 13.16Ndipo Yesu anati kwa iye, Lero chipulumutso chagwera nyumba iyi, popeza iyenso ndiye mwana wa Abrahamu. 10Pakuti Mwana wa Munthu anadza kufunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.
Fanizo la ndalama khumi za mina
(Mat. 25.14-30)
11Ndipo pakumva izi iwo, Iye anaonjeza nanena fanizo, chifukwa anali Iye pafupi pa Yerusalemu, ndipo iwo anayesa kuti Ufumu wa Mulungu ukuti uonekere pomwepo. 12#Mrk. 13.34Pamenepo anati, Munthu wa fuko lomveka ananka kudziko lakutali, kudzilandirira yekha ufumu, ndi kubwerako. 13Ndipo anaitana akapolo ake khumi, nawapatsa iwo ndalama khumi za mina, nati kwaiwo, Chita nazoni malonda kufikira ndibweranso. 14#Yoh. 1.11Koma mfulu za pamudzi pake zinamuda, nkutuma akazembe amtsate m'mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyo akhale mfumu yathu. 15Ndipo kunali, pakubwera iye, atalandira ufumuwo, anati aitanidwe kwa iye akapolo aja, amene adawapatsa ndalamazo, kuti adziwe umo anapindulira pochita malonda. 16Ndipo anafika woyamba, nanena, Mbuye, mina yanu inachita nionjeza mina khumi. 17#Mat. 25.21Ndipo anati kwa iye, Chabwino, kapolo wabwino iwe; popeza unakhala wokhulupirika m'chaching'onong'ono, khala nao ulamuliro pa mizinda khumi. 18Ndipo anadza wachiwiri, nanena, Mbuye, mina yanu yapindula mina zisanu. 19Ndipo anati kwa iyenso, Khala iwenso woweruza mizinda isanu. 20Ndipo wina anadza, nanena, Mbuye, taonani, siyi mina yanu, ndaisunga m'kansalu; 21#Mat. 25.24pakuti ndinakuopani, popeza inu ndinu munthu wouma mtima: munyamula chimene simunachiike pansi, mututa chimene simunachifese. 22#2Sam. 1.16; Mat. 12.37; 25.26Ananena kwa iye, Pakamwa pako ndikuweruza, kapolo woipa iwe. Unadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wonyamula chimene sindinachiike, ndi wotuta chimene sindinachifese; 23ndipo sunapereke bwanji ndalama yanga pokongoletsa, ndipo ine pakudza ndikadaitenga ndi phindu lake? 24Ndipo anati kwa iwo akuimirirapo, Mchotsereni minayo, nimuipatse kwa iye wakukhala nazo mina khumi. 25Ndipo anati kwa iye, Mbuye, ali nazo mina khumi. 26#Mat. 13.12; 25.29Ndinena ndi inu, kuti kwa yense wakukhala nacho kudzapatsidwa; koma kwa iye amene alibe kanthu, chingakhale chimene ali nacho chidzachotsedwa. 27Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga.
28Ndipo m'mene adanena izi anawatsogolera nakwera ku Yerusalemu.
Yesu alowa mu Yerusalemu
(Mat. 21.1-9; Mrk. 11.1-10; Yoh. 12.12-19)
29Ndipo kunali, m'mene anayandikira ku Betefage ndi Betaniya, paphiri lotchedwa la Azitona, anatuma awiri a ophunzira, 30nati, Mukani kumudzi uli pandunji panu; m'menemo, polowa, mudzapeza mwana wa bulu womangidwa, pamenepo palibe munthu anakwerapo nthawi iliyonse; mummasule iye nimumtenge. 31Ndipo munthu akati kwa inu, Mummasuliranji? Mudzatero naye, Ambuye amfuna iye. 32Ndipo anachoka otumidwawo, napeza monga adanena kwa iwo. 33Ndipo pamene anamasula mwana wa bulu, eni ake anati kwa iwo, Mumasuliranji mwana wa bulu? 34Ndipo anati, Ambuye amfuna iye. 35#2Maf. 9.13; Mrk. 11.7Ndipo anadza naye kwa Yesu; ndipo anayalika zovala zao pa mwana wa buluyo, nakwezapo Yesu. 36Ndipo pakupita Iye, anayala zovala zao m'njira. 37Ndipo pakuyandikira Iye tsono potsetsereka pake paphiri la Azitona, unyinji wonse wa ophunzira anayamba kukondwera ndi kuyamika Mulungu ndi mau aakulu, chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu anaziona; 38#Mas. 118.26nanena, Wolemekezeka Mfumuyo ikudza m'dzina la Ambuye; mtendere mu Mwamba, ndi ulemerero mu Mwambamwamba. 39Ndipo Afarisi ena a m'khamu la anthu anati kwa Iye, Mphunzitsi, dzudzulani ophunzira anu. 40#Hab. 2.9-11Ndipo anayankha nati, Ndinena ndi inu, ngati awa khala chete miyala idzafuula.
Yesu alirira Yerusalemu
(Luk. 13.34-35)
41 #
Yoh. 11.35
Ndipo m'mene anayandikira, anaona mzindawo naulirira, 42nanena, Ukadazindikira tsiku ili, inde iwetu zinthu za mtendere! Koma tsopano zibisika pamaso pako. 43#Yes. 29.3-4Pakuti masiku adzakudzera, ndipo adani ako adzakuzingira linga, nadzakuzungulira iwe kwete, nadzakutsekereza ponsepo; 44#1Maf. 9.7-8; Mat. 24.2ndipo adzakupasula iwe, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala wina pamwala unzake; popeza sunazindikire nyengo ya mayang'aniridwe ako.
Ayeretsa Kachisi kachiwiri
(Mat. 21.23-27; Mrk. 11.15-19; Yoh. 2.13-22)
45Ndipo analowa mu Kachisi, nayamba kutulutsa iwo akugulitsa malonda, nanena nao, 46#Yes. 56.7; Yer. 7.11Kwalembedwa, Ndipo nyumba yanga idzakhala nyumba yakupemphera; koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba.
47 #
Yoh. 7.19; 8.37 Ndipo analikuphunzitsa mu Kachisi tsiku ndi tsiku. Koma ansembe aakulu, ndi alembi ndi akulu a anthu anafunafuna kumuononga Iye; 48ndipo sanapeze chimene akachita; pakuti anthu onse anamlendewera Iye kuti amve.
Currently Selected:
LUKA 19: BLP-2018
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi