YOHANE 4
4
Mkazi wa ku Samariya
1 #
Yoh. 3.22, 26 Chifukwa chake pamene Ambuye anadziwa kuti Afarisi adamva kuti Yesu anayesa anthu ophunzira, nawabatiza koposa Yohane 2(angakhale Yesu sanabatize yekha koma ophunzira ake), 3anachokera ku Yudeya, namukanso ku Galileya. 4Ndipo anayenera kupita pakati pa Samariya. 5#Yos. 24.32Chifukwa chake anadza kumzinda wa Samariya, dzina lake Sikari, pafupi pa kadziko kamene Yakobo adapatsa mwana wake Yosefe; 6ndipo pamenepo panali chitsime cha Yakobo. Ndipo Yesu, popeza analema ndi ulendo wake, motero anakhala pachitsime. 7Kunali ngati ora lachisanu ndi chimodzi. Kunadza mkazi wotuluka mu Samariya kudzatunga madzi. Yesu ananena naye, Undipatse Ine ndimwe. 8Pakuti ophunzira ake adachoka kunka kumzinda kuti akagule chakudya. 9#Mac. 10.28Pamenepo mkazi wa mu Samariya ananena ndi Iye, Bwanji Inu, muli Myuda, mupempha kwa ine kumwa, ndine mkazi Msamariya? (Pakuti Ayuda sayenderana nao Asamariya). 10#Yes. 44.3Yesu anayankha nati kwa iye, Ukadadziwa mtulo wa Mulungu, ndi Iye amene alinkunena ndi iwe, Undipatse Ine ndimwe; ukadapempha Iye, ndipo akadakupatsa madzi amoyo. 11Mkaziyo ananena ndi Iye, Ambuye, mulibe chotungira madzi, ndi chitsime chili chakuya; ndipo mwatenga kuti madzi amoyo? 12Kodi muli wamkulu ndi atate wathu Yakobo amene anatipatsa ife chitsimechi, namwamo iye yekha, ndi ana ake, ndi zoweta zake? 13Yesu anayankha nati kwa iye, Yense wakumwako madzi awa adzamvanso ludzu; 14#Yoh. 6.35; 7.38koma iye wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene Ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira kumoyo wosatha. 15Mkaziyo ananena kwa Iye, Ambuye, ndipatseni madzi amene, kuti ndisamve ludzu, kapena ndisadze kuno kudzatunga. 16Yesu ananena kwa iye, Muka, kamuitane mwamuna wako, nudze kuno. 17Mkazi anayankha nati kwa Iye, Ndilibe mwamuna. Yesu ananena naye, Wanena bwino, kuti mwamuna ndilibe; 18pakuti wakhala nao amuna asanu; ndipo iye amene ukhala naye tsopano sali mwamuna wako; ichi wanena zoona. 19#Luk. 7.16Mkazi ananena ndi Iye, Ambuye, ndizindikira kuti muli Mneneri. 20#Yos. 8.33; Ower. 9.7; 1Maf. 9.3Makolo athu analambira m'phiri ili; ndipo inu munena, kuti mu Yerusalemu muli malo oyenera kulambiramo anthu. 21#Mala. 1.11Yesu ananena naye, Tamvera Ine, mkazi iwe, kuti ikudza nthawi, imene simudzalambira Atate kapena m'phiri ili, kapena mu Yerusalemu. 22#2Maf. 17.29; Aro. 9.4-5Inu mulambira chimene simuchidziwa; ife tilambira chimene tichidziwa; pakuti chipulumutso chichokera kwa Ayuda. 23#Afi. 3.3Koma ikudza nthawi, ndipo tsopano ilipo, imene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m'choonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake. 24#2Ako. 3.17Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira Iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m'choonadi. 25#Yoh. 4.29, 39Mkazi ananena ndi Iye, Ndidziwa kuti Mesiya adza (wotchedwa Khristu): akadzadza Iyeyu, adzatiuza zonse. 26#Mrk. 14.61-62Yesu ananena naye, Ine wakulankhula nawe ndine amene.
27Ndipo pamenepo anadza ophunzira ake; nazizwa kuti analinkulankhula ndi mkazi; koma panalibe wina anati, Mufuna chiyani? Kapena, mulankhula naye chiyani? 28Pamenepo mkazi anasiya mtsuko wake, namuka mumzinda, nanena ndi anthu, 29#Yoh. 4.25Tiyeni, mukaone munthu, amene anandiuza zinthu zilizonse ndinazichita: ameneyu sali Khristu nanga? 30Anatuluka iwo m'mzinda ndipo analinkudza kwa Iye.
Za masika ndi antchito
31Pa mphindikati iyi ophunzira ake anampempha Iye, ndi kunena, Rabi, idyani. 32Koma Iye anati kwa iwo, Ine ndili nacho chakudya chimene inu simuchidziwa. 33Chifukwa chake ophunzira ananena wina ndi mnzake, Kodi pali wina anamtengera Iye kanthu kakudya? 34#Yoh. 6.38Yesu ananena nao, Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake. 35#Mat. 9.37Kodi simunena inu, kuti, Yatsala miyezi inai, ndipo kudza kumweta? Onani ndinena kwa inu, Kwezani maso anu, nimuyang'ane m'minda, kuti mwayera kale kufikira kumweta. 36Wakumweta alandira kulipira, nasonkhanitsira chobala kumoyo wosatha; kuti wofesayo akakondwere pamodzi ndi womwetayo. 37Pakuti m'menemo chonenacho chili choona, Wofesa ndi wina, womweta ndi winanso. 38Ine ndinatuma inu kukamweta chimene simunagwirirapo ntchito: ena anagwira ntchito, ndipo inu mwalowa ntchito yao.
Yesu ndi Asamariya
39 #
Yoh. 4.29
Ndipo m'mzinda muja anthu Asamariya ambiri anamkhulupirira Iye chifukwa cha mau a mkazi, wochita umboniyo, kuti, Anandiuza ine zinthu zilizonse ndinazichita. 40Chifukwa chake pamene Asamariya anadza kwa Iye, anamfunsa akhale nao; ndipo anakhala komweko masiku awiri. 41Ndipo ambiri oposa anakhulupirira chifukwa cha mau ake; 42#Yoh. 17.8; 1Yoh. 4.14ndipo ananena kwa mkazi, kuti, Tsopano sitikhulupirira chifukwa cha kulankhula kwako: pakuti tamva tokha, ndipo tidziwa kuti Mpulumutsi wa dziko lapansi ndi Iyeyu ndithu.
Yesu achiritsa mwana wa Mkulu
43Koma atapita masiku awiriwo anachoka komweko kunka ku Galileya. 44#Mat. 13.57Pakuti Yesu mwini anachita umboni kuti, Mneneri alibe ulemu m'dziko la kwao. 45#Yoh. 2.23Chifukwa chake pamene anadza ku Galileya, Agalileya anamlandira Iye, atakaona zonse zimene anazichita mu Yerusalemu pachikondwerero; pakuti iwonso ananka kuchikondwerero.
46 #
Yoh. 2.7-9
Chifukwa chake Yesu anadzanso ku Kana wa mu Galileya, kumene anasandutsa madzi vinyo. Ndipo kunali mkulu wina wa mfumu, mwana wake anadwala mu Kapernao. 47Iyeyu, pamene anamva kuti Yesu wachokera ku Yudeya nafika ku Galileya, ananka kwa Iye, nampempha kuti atsike kukachiritsa mwana wake; pakuti anali pafupi imfa. 48#1Ako. 1.22Pamenepo Yesu anati kwa iye, Ngati simuona zizindikiro ndi zozizwa, simudzakhulupirira. 49Mkuluyo ananena kwa Iye, Ambuye, tsikani asanafe mwana wanga. 50Yesu ananena naye, Muka, mwana wako ali ndi moyo. Munthuyo anakhulupirira mau amene Yesu anatero naye, namuka. 51Ndipo m'mene analikutsika, akapolo ake anakomana naye, nanena, kuti, Mwana wanu ali ndi moyo. 52Chifukwa chake anawafunsa ora lake anayamba kuchiralo. Pamenepo anati kwa iye, kuti, Dzulo, ora lachisanu ndi chiwiri malungo anamsiya. 53Chifukwa chake atateyo anadziwa kuti ndi ora lomwelo limene Yesu anati kwa iye, Mwana wako ali ndi moyo; ndipo anakhulupirira iye yekha ndi a pa banja lake onse. 54Ichi ndi chizindikiro chachiwiri Yesu anachita, atachokera ku Yudeya, ndi kulowa mu Galileya.
Currently Selected:
YOHANE 4: BLP-2018
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi