YOHANE 17
17
Yesu apempherera ophunzira ake
1 #
Yoh. 12.13
Zinthu izi analankhula Yesu; ndipo m'mene anakweza maso ake Kumwamba, anati, Atate, yafika nthawi; lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanu akulemekezeni Inu; 2#Mat. 11.27monga mwampatsa Iye ulamuliro pa thupi lililonse, kuti onse amene mwampatsa Iye, awapatse iwo moyo wosatha. 3#Yoh. 3.34; 1Yoh. 5.20Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Khristu amene munamtuma. 4#Yoh. 5.36; 9.3Ine ndalemekeza Inu padziko lapansi, m'mene ndinatsiriza ntchito imene munandipatsa ndichite. 5#Yoh. 1.1-2Ndipo tsopano, Atate Inu, lemekezani Ine ndi Inu nokha ndi ulemerero umene ndinali nao ndi Inu lisanakhale dziko lapansi. 6#Yoh. 17.2, 9, 11Ndalionetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa Ine m'dziko lapansi; anali anu, ndipo mwandipatsa Ine iwo; ndipo adasunga mau anu. 7Azindikira tsopano kuti zinthu zilizonse zimene mwandipatsa Ine zichokera kwa Inu; 8#Yoh. 8.28; 16.27, 30chifukwa mau amene munandipatsa Ine ndinapatsa iwo; ndipo analandira, nazindikira koona kuti ndinatuluka kwa Inu, ndipo anakhulupirira kuti Inu munandituma Ine. 9Ine ndiwapempherera iwo; sindipempherera dziko lapansi, koma iwo amene mwandipatsa Ine, 10#Yoh. 16.15chifukwa ali anu: ndipo zanga zonse zili zanu, ndi zanu zili zanga; ndipo ndilemekezedwa mwa iwo. 11#1Pet. 1.5; Yud. 1Sindikhalanso m'dziko lapansi, koma iwo ali m'dziko lapansi, ndipo Ine ndidza kwa Inu. Atate Woyera, sungani awa m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine, kuti akhale mmodzi, monga Ife. 12#Yoh. 6.39, 70; 18.9; Mac. 1.20Pamene ndinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayike mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko, kuti lembo likwaniridwe. 13Koma tsopano ndidza kwa Inu; ndipo izi ndilankhula m'dziko lapansi, kuti akhale nacho chimwemwe changa chokwaniridwa mwa iwo okha. 14#Yoh. 15.18-19; 17.8Ine ndawapatsa iwo mau anu; ndipo dziko lapansi, linadana nao, chifukwa sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi. 15#Mat. 6.13; Agal. 1.4Sindipempha kuti muwachotse iwo m'dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo. 16Siali a dziko lapansi monga Ine sindili wa dziko lapansi. 17#Aef. 5.26Patulani iwo m'choonadi; mau anu ndi choonadi. 18#Yoh. 20.21Monga momwe munandituma Ine kudziko lapansi, Inenso ndinatuma iwo kudziko lapansi. 19#1Ako. 1.2, 30Ndipo chifukwa cha iwo Ine ndidzipatula ndekha kuti iwonso akhale opatulidwa m'choonadi. 20Koma sindipempherera iwo okha, komanso iwo akukhulupirira Ine chifukwa cha mau ao; 21#Yoh. 10.16, 38; Aro. 12.5kuti onse akakhale amodzi, monga Inu Atate mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, kuti iwonso akakhale mwa Ife: kuti dziko lapansi likakhulupirire kuti Inu munandituma Ine. 22#1Yoh. 1.3Ndipo ulemerero umene mwandipatsa Ine ndapatsa iwo; kuti akhale amodzi, monga Ife tili mmodzi; 23#Akol. 3.14Ine mwa iwo, ndi Inu mwa Ine, kuti akhale angwiro mwa mmodzi; kuti dziko lapansi lizindikire kuti Inu munandituma Ine, nimunawakonda iwo, monga momwe munakonda Ine. 24#Yoh. 12.26; 14.3; 17.5; 1Ate. 4.17Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndili Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang'anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi. 25#Yoh. 7.29; 15.21; 16.27Atate wolungama, dziko lapansi silinadziwe Inu, koma Ine ndinadziwa Inu; ndipo iwo anazindikira kuti munandituma Ine; 26#Yoh. 15.9, 15ndipo ndinazindikiritsa iwo dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa; kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndi Ine mwa iwo.
Currently Selected:
YOHANE 17: BLP-2018
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi