YouVersion Logo
Search Icon

GENESIS 8

8
Nowa atuluka m'chingalawa
1 # Gen. 19.29; Eks. 2.24; 14.21 Ndipo Mulungu anakumbukira Nowa ndi zamoyo zonse, ndi nyama zonse zimene zinali pamodzi naye m'chingalawamo; ndipo Mulungu anapititsa mphepo padziko lapansi, naphwa madzi; 2ndipo anatsekedwa akasupe a madzi aakulu ndi mazenera a kumwamba, niletsedwa mvula ya kumwamba; 3ndipo madzi anaphweraphwerabe padziko lapansi: pamene anatha masiku zana limodzi kudza makumi atatu madzi anachepa. 4Ndipo chingalawa chinaima pamapiri a Ararati, mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi ndi asanu ndi awiri la mwezi. 5Ndipo madzi analinkuchepa kufikira mwezi wakhumi; mwezi wakhumi tsiku loyamba mwezi ndipo padaoneka mitu ya mapiri.
6Ndipo panali atapita masiku makumi anai, Nowa anatsegula pa zenera la chingalawa limene analipanga: 7ndipo anatulutsa khwangwala, ndipo anatuluka kunka kwina ndi kwina kufikira adaphwa madzi padziko lapansi. 8Ndipo anatulutsa njiwa imchokere, kuti aone kapena madzi anaphwa pamwamba padziko lapansi; 9koma njiwayo siinapeze popondapo phazi lake, nibwera kwa iye kuchingalawako, pakuti madzi analipo padziko lonse lapansi; ndipo anatulutsa dzanja lake, naitenga, nailowetsa kwa iye m'chingalawamo. 10Ndipo analinda masiku ena asanu ndi awiri; natulutsanso njiwayo m'chingalawamo; 11ndipo njiwa inadza kwa iye madzulo; ndipo, taonani, m'kamwa mwake munali tsamba la azitona lothyoledwa: ndipo anadziwa Nowa kuti madzi analimkuphwa padziko lapansi. 12Ndipo analindanso masiku ena asanu ndi awiri; natulutsa njiwayo: ndipo siinabwerenso konse kwa iye. 13Ndipo panali chaka cha mazana asanu ndi limodzi kudza chimodzi, mwezi woyamba, tsiku loyamba mwezi, madzi anaphwa padziko lapansi; ndipo Nowa anachotsa tsindwi lake pachingalawa, nayang'ana, ndipo taonani, padauma padziko lapansi. 14Mwezi wachiwiri tsiku la makumi awiri kudza asanu ndi awiri la mwezi, lidauma dziko lapansi.
15Mulungu ndipo ananena kwa Nowa, kuti, 16Tulukamoni m'chingalawamo, iwe ndi ana ako, ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe. 17#Gen. 1.22, 28; 9.1Tulutsa pamodzi ndi iwe zamoyo zonse zili ndi iwe za nyama zonse, zouluka, ndi zinyama, ndi zokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi; kuti ziswane padziko lapansi, zibalane, zichuluke padziko lapansi. 18Ndipo anatuluka Nowa ndi ana ake, ndi mkazi wake, ndi akazi a ana ake, pamodzi naye: 19zinyama zonse, zokwawa zonse, zouluka zonse, ndi zonse zokwawa padziko lapansi, monga mwa mitundu yao, zinatuluka m'chingalawamo.
Nowa amanga guwa la nsembe
20 # Lev. 11 Ndipo Nowa anamanga guwa la nsembe la Yehova; natengapo nyama zodyedwa zonse ndi mbalame zodyedwa zonse napereka nsembe zopsereza paguwapo. 21#Eks. 29.18, 25; Yes. 54.9; Ezk. 16.19; Aef. 5.2; Afi. 4.18Ndipo Yehova anamva chonunkhira chakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwake, Sindidzatembereranso konse nthaka chifukwa cha munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndachitiramo. 22#Yer. 5.24; 33.20, 25Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthawi yakubzala ndi yakukunkha, chisanu ndi mafundi, malimwe ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekai.

Currently Selected:

GENESIS 8: BLP-2018

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in