1
Gen. 32:28
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
Munthu uja adati, “Dzina lako silidzakhalanso Yakobe. Walimbana ndi Mulungu ndi anthu, ndipo wapambana. Motero dzina lako lidzakhala Israele.”
Compare
Explore Gen. 32:28
2
Gen. 32:26
Apo munthuyo adati, “Taye ndizipita, chifukwa kulikucha.” Koma Yakobe adayankha kuti, “Sindikulola kuti upite mpaka utandidalitsa.”
Explore Gen. 32:26
3
Gen. 32:24
Iye adangotsala yekha. Tsono kudadza munthu wina amene adalimbana naye mpaka m'matandakucha.
Explore Gen. 32:24
4
Gen. 32:30
Yakobe adati, “Ndamuwona Mulungu maso ndi maso, ndipo ndili moyobe.” Tsono malowo adaŵatcha Penuwele.
Explore Gen. 32:30
5
Gen. 32:25
Munthuyo ataona kuti sakuphulapo kanthu, adamenya Yakobe m'nyung'unyu, nyung'unyuyo nkuguluka polimbanapo.
Explore Gen. 32:25
6
Gen. 32:27
Munthuyo adamufunsa kuti, “Dzina lako ndiwe yani?” Yakobe adayankha kuti, “Dzina langa ndine Yakobe.”
Explore Gen. 32:27
7
Gen. 32:29
Pomwepo Yakobe adati, “Choncho nanunso tandiwuzani dzina lanu.” Koma munthuyo adati, “Chifukwa chiyani ukundifunsa dzina?” Ndipo pompo munthu uja adadalitsa Yakobe.
Explore Gen. 32:29
8
Gen. 32:10
Ine sindiyenera kulandira chifundo ndi chikhulupiriro chonse chimene mwandiwonetsa ine mtumiki wanu. Ndidaoloka Yordani ndilibe nkanthu komwe, koma ndodo yokha, koma tsopano ndabwerera ndi magulu aŵiri aŵa.
Explore Gen. 32:10
9
Gen. 32:32
Nchifukwa chake mpaka lero lino zidzukulu zonse za Israele sizidya nyama yapanyung'unyu, chifukwa ndi pa mtsempha wa panyung'unyu pomwe Yakobe adaamenyedwa.
Explore Gen. 32:32
10
Gen. 32:9
Pamenepo Yakobe adayamba kupemphera. Adati, “Mulungu wa kholo langa Abrahamu, Mulungu wa bambo wanga Isaki, mundimve ine! Inu Chauta mudandiwuza kuti, ‘Bwerera ku dziko lako, dziko la abale ako, ndidzasamala kuti zinthu zikuyendere bwino.’
Explore Gen. 32:9
11
Gen. 32:11
Ndapota nanu, pulumutseni ku mphamvu za mbale wanga Esau. Ndikuwopa kuti mwina akubwera kudzatithira nkhondo, ndipo tonsefe adzatiwononga pamodzi ndi akazi ndi ana omweŵa.
Explore Gen. 32:11
Home
Bible
Plans
Videos