Tsiku lina pamene iwo adasonkhana kuti apembedze Ambuye ndi kuti asale zakudya, Mzimu Woyera adaŵauza kuti, “Mundipatulire Barnabasi ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndaŵaitanira.” Tsono atasala zakudya ndi kupemphera adaŵasanjika manja naŵatuma.