YouVersion Logo
Search Icon

Ntc. 13

13
Barnabasi ndi Saulo atumidwa
1Mu mpingo wa ku Antiokeya munali alaliki ndi aphunzitsi#13.1: aphunzitsi: Mu mpingo ena anali ndi luso lophunzitsa anthu, ndipo adaapatsidwa udindo wophunzitsa ophunzira (1 Akor. 12.28-30; Aef. 4.11). aŵa: Barnabasi, Simeoni (wotchedwa Wakuda), Lusio wa ku Kirene, Manaene (amene adaaleredwa pamodzi ndi bwanamkubwa Herode), ndiponso Saulo. 2Tsiku lina pamene iwo adasonkhana kuti apembedze Ambuye ndi kuti asale zakudya, Mzimu Woyera adaŵauza kuti, “Mundipatulire Barnabasi ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndaŵaitanira.” 3Tsono atasala zakudya ndi kupemphera adaŵasanjika manja naŵatuma.
Za ku Kipro
4Barnabasi ndi Saulo, otumidwa ndi Mzimu Woyera aja, adapita ku Seleukiya. Kuchokera kumeneko adayenda m'chombo nakafika ku chilumba cha Kipro. 5Atafika ku mzinda wa Salami, adalalika mau a Mulungu m'nyumba zamapemphero za Ayuda. Analinso ndi Yohane#13.5: Yohane: Ameneyu ndi Yohane Marko (Ntch. 12.25). womaŵathandiza. 6Iwo adabzola chilumba chonse mpaka kukafika ku mzinda wa Pafosi. Kumeneko adapezako munthu wina wamasenga, dzina lake Barayesu, Myuda amene ankadziyesa mneneri. 7Iyeyu ankakhala kwa bwanamkubwa Sergio Paulo, munthu wanzeru. Sergio Pauloyo adaitana Barnabasi ndi Saulo, chifukwa iye ankafunitsitsa kumva mau a Mulungu. 8Koma kumeneko adapezanako ndi Elimasi, wamasenga uja (Elimasi ndiye kuti Wamasenga). Iyeyo adatengana nawo, kuwopa kuti bwanamkubwa uja angakhulupirire. 9Koma Saulo, amene ankatchedwanso Paulo, atadzazidwa ndi Mzimu Woyera, adampenyetsetsa 10nati, “Iwe mwana wa Satana, mdani wa chilungamo, wa mtima wa kunyenga kulikonse ndi kuchenjeretsa kwamtundumtundu, udzaleka liti kupotoza njira zolungama za Ambuye? 11Ona dzanja la Ambuye likukantha tsopano apa. Ukhala wakhungu osaonanso dzuŵa pa kanthaŵi.” Nthaŵi yomweyo khungu ndi mdima zidamgweradi, ndipo adayamba kufunafuna anthu oti amgwire dzanja ndi kumtsogolera. 12Pamene bwanamkubwa uja adaona zimene zidachitikazo, adakhulupirira. Adaadabwa nazo zimene iwo adaaphunzitsa za Ambuye.
Za ku Antiokeya m'dera la Pisidiya
13Paulo ndi anzake adayenda m'chombo kuchokera ku Pafosi kukafika ku Perga m'dera la Pamfiliya. Koma Yohane#13.13: Yohane: Ameneyu ndi Yohane Marko amene watchulidwa kale pa Ntc. 13.5. Onaninso pa Ntc. 12.25. adaŵasiya nabwerera ku Yerusalemu. 14Kuchokera ku Perga iwo adapitirira nakafika ku Antiokeya m'dera la Pisidiya. Pa tsiku la Sabata adaloŵa m'nyumba yamapempherero ya Ayuda, nakhala pansi. 15Ataŵerengedwa mau a m'buku la Malamulo a Mose ndi m'buku la aneneri, akulu a nyumba yamapemphero ija adaŵatumira mau oŵauza kuti, “Abale, ngati muli ndi mau olimbikitsa nawo anthuŵa, nenani.” 16Apo Paulo adaimirira nakweza dzanja kuti anthu akhale chete, ndipo adayamba kulankhula. Adati,
“Inu Aisraele, ndi ena nonse oopa Mulungu, mverani. 17#Eks. 1.7; Eks. 12.51 Mulungu wa mtundu wathu wa Aisraele, adasankha makolo athu, ndipo adaŵakuza pamene anali alendo ku dziko la Ejipito. Adaŵatulutsa m'dzikomo ndi dzanja lake lamphamvu, 18#Num. 14.34; Deut. 1.31adaŵasamalabe mopirira m'chipululu zaka makumi anai. 19#Deut. 7.1; Yos. 14.1 Iye adaononga mitundu isanu ndi iŵiri ya anthu m'dziko la Kanani, napereka dziko lao kwa Aisraele kuti likhale laolao. Zonsezi zidatenga zaka ngati 450.
20 # Owe. 2.16; 1Sam. 3.20 “Pambuyo pake adaŵapatsa oweruza kufikira nthaŵi ya mneneri Samuele. 21#1Sam. 8.5; 1Sam. 10.21 Kenaka anthu adapempha kuti aŵapatse mfumu, ndipo Mulungu adaŵapatsa Saulo, mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini, iye nkuŵalamulira pa zaka makumi anai. 22#1Sam. 13.14; 1Sam. 16.12; Mas. 89.20 Pambuyo pake Mulungu adamchotsa Sauloyo, naika Davide kuti akhale mfumu yao. Za iyeyu Mulungu adanena kuti, ‘Ndapeza Davide, mwana wa Yese, ndiye munthu wanga wapamtima, amene adzachita zonse zimene Ine ndifuna.’ 23Mwa zidzukulu za Davideyo Mulungu adasankha Yesu kuti akhale Mpulumutsi wa Aisraele, monga momwe adaalonjezera kale. 24#Mk. 1.4; Lk. 3.3Iyeyo asanayambe ntchito, Yohane ankalalikira Aisraele onse kuti atembenuke mtima ndi kubatizidwa. 25#Yoh. 1.20; Mt. 3.11; Mk. 1.7; Lk. 3.16; Yoh. 1.27 Pamene Yohane anali pafupi kutsiriza ntchito yake, adafunsa anthu kuti, ‘Kodi inu mumayesa kuti ine ndine yani? Inetu sindine amene mukumuyembekezayo ai. Koma pakubwera wina pambuyo panga amene ine sindili woyenera ngakhale kumvula nsapato zake.’
26“Ine abale, zidzukulu za Abrahamu, ndi ena nonse oopa Mulungu, uthenga wa chipulumutsowu Mulungu watumizira ife. 27Anthu okhala ku Yerusalemu ndi akulu ao sadamzindikire Yesu, ndipo sadamvetse mau a aneneri amene amaŵerengedwa tsiku la Sabata lililonse. Komabe pakumzenga mlandu Yesuyo kuti aphedwe, adachitadi zimene aneneri adaaneneratu. 28#Mt. 27.22, 23; Mk. 15.13, 14; Lk. 23.21-23; Yoh. 19.15 Ngakhale sadapeze konse chifukwa chomuphera, komabe adapempha Pilato kuti Yesuyo aphedwe. 29#Mt. 27.57-61; Mk. 15.42-47; Lk. 23.50-56; Yoh. 19.38-42 Ndipo atachita zonse zimene zidalembedwa za Iye, adamtsitsapo pa mtanda paja namuika m'manda. 30Koma Mulungu adamuukitsa kwa akufa, 31#Ntc. 1.3ndipo pa masiku ambiri adakhala akuwonekera kwa anthu aja amene adaamperekeza ku Yerusalemu kuchokera ku Galileya. Amenewo ndiwo amene akumchitira umboni kwa anthu tsopano. 32#Mas. 2.7 Ndipo ife tikukulalikirani Uthenga Wabwino wakuti zilipo zimene Mulungu adaaŵalonjeza makolo athu. 33Tsono zimene adaalonjezazo Iye watichitire ifeyo, zidzukulu zao, pakuukitsa Yesu kwa akufa. Monganso mudalembedwera m'Salimo lachiŵiri kuti,
“ ‘Iwe ndiwe Mwana wanga,
Ine lero ndakubala.’
34 # Yes. 55.3 Ndipo zakuti adamuukitsa kwa akufa kuti asaole konse, Mulungu adati, ‘Ndidzakupatsani madalitso opatulika ndi okhulupirika amene ndidalonjeza Davide.’ 35#Mas. 16.10 Nchifukwa chake m'Salimo lina akutinso,
“ ‘Simudzalekerera Woyera wanu kuti aole.’
36Paja Davide adati atakwaniritsa zimene Mulungu adaakonzeratu pa masiku a mbadwo wake, adamwalira naikidwa m'manda pamodzi ndi makolo ake, ndipo thupi lake lidaola. 37Koma uja Mulungu adamuukitsa kwa akufayu sadaole ai. 38Tsono abale, dziŵani kuti chifukwa cha Yesuyo tikukulalikirani zakuti machimo amakhululukidwa. 39Ndipo kudzera mwa Iye yemweyo aliyense wokhulupirira amapeza chipulumutso chathunthu chimene simukadatha kuchipata potsata malamulo a Mose. 40Ndiye inu chenjerani kuti zingakugwereni zimene aneneri aja adanena kuti,
41 # Hab. 1.5 “ ‘Mvetsani inu anthu onyoza,
zizwani ndipo muwonongeke,
pakuti pa nthaŵi ya moyo wanu
Ine ndidzachita chinthu
chimene simungakhulupirire konse,
ngakhale wina akuuzeni.’ ”
42Pamene ankatuluka, anthu aja adapempha Paulo ndi Barnabasi kuti adzaŵakambirenso zomwezi tsiku la Sabata linalo. 43Anthu osonkhana aja atamwazikana, Ayuda ambiri, ndiponso anthu a mitundu ina otembenuka nkumatsata zachiyuda,#13.43: otembenuka nkumatsata zachiyuda: Onani mau ofotokozera Ntc. 2.11. adatsatira Paulo ndi Barnabasi. Aŵiriŵa adalankhula ndi anthu aja, naŵapempha kuti alimbikire kutsata zimene Mulungu adaŵachitira mwa kukoma mtima kwake.
44Pa tsiku la Sabata linalo pafupi anthu onse amumzindamo adasonkhana kuti amve mau a Ambuye. 45Pamene Ayuda aja adaona anthu ambiriwo, adachita nsanje kwambiri. Adayamba kutsutsa zimene Paulo ankanena, ndipo adamchita chipongwe. 46Koma Paulo ndi Barnabasi adalankhula molimbika, adati, “Kudaayenera ndithu kuti tiyambe talalika mau a Mulungu kwa inu. Tsono popeza kuti mwaŵakana, ndipo potero mwaonetsa nokha kuti ndinu osayenera kulandira moyo wosatha, ife tikusiyani, tipita kwa anthu akunja. 47#Yes. 42.6; 49.6 Paja Ambuye adatilamula kuti,
“ ‘Ndakuika kuti uunikire anthu akunja,
kuti mwa iwe ndipulumutse dziko lonse lapansi.’ ”
48Pamene anthu a mitundu ina aja adamva zimenezi, adakondwa, nayamikira wawu a Ambuye. Ndipo onse amene Mulungu adaaŵasankha kuti alandira moyo wosatha, adakhulupirira.
49Mau a Ambuye adafalikira m'dziko monse muja. 50Koma Ayuda aja adautsa mitima ya akazi ena apamwamba opembedza Mulungu, ndiponso ya atsogoleri achimuna amumzindamo. Tsono adayambitsa mazunzo osautsa Paulo ndi Barnabasi, naŵapirikitsa m'dziko mwaomo. 51#Mt. 10.14; Mk. 6.11; Lk. 9.5; 10.11Koma iwo adasansa fumbi la kumapazi kwao moŵatsutsa, napita ku Ikonio. 52Ndipo ophunzira a ku Antiokeya adadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo adakhala ndi chimwemwe chachikulu.

Currently Selected:

Ntc. 13: BLY-DC

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in