Ndipo iwo, pochenjezedwa m'kulota kuti asabwerere kwa Herode, anachoka kupita ku dziko lao pa njira ina.
Ndipo pamene iwo anachoka, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe m'kulota, nati, Tauka, nutenge kamwanako ndi amake, nuthawire ku Ejipito, nukakhale kumeneko kufikira ndidzakuuza iwe; pakuti Herode adzafuna kamwana kukaononga Iko.