1
YAKOBO 1:2-3
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
BLPB2014
Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero a mitundumitundu; pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro.
Compare
Explore YAKOBO 1:2-3
2
YAKOBO 1:5
Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.
Explore YAKOBO 1:5
3
YAKOBO 1:19
Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.
Explore YAKOBO 1:19
4
YAKOBO 1:4
Koma chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda chilema, osasowa kanthu konse.
Explore YAKOBO 1:4
5
YAKOBO 1:22
Khalani akuchita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha.
Explore YAKOBO 1:22
6
YAKOBO 1:12
Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye.
Explore YAKOBO 1:12
7
YAKOBO 1:17
Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.
Explore YAKOBO 1:17
8
YAKOBO 1:23-24
Pakuti ngati munthu ali wakumva mau, wosati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang'anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m'kalirole; pakuti wadziyang'anira yekha, nachoka, naiwala pompaja nali wotani.
Explore YAKOBO 1:23-24
9
YAKOBO 1:27
Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.
Explore YAKOBO 1:27
10
YAKOBO 1:13-14
Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu: koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, nichimnyenga.
Explore YAKOBO 1:13-14
11
YAKOBO 1:9
Koma mbale woluluka adzitamandire pa ukulu wake
Explore YAKOBO 1:9
Home
Bible
Plans
Videos