Ndipo ulemerero wa Mulungu wa Israele unakwera kuchoka pa kerubi, pamene unakhalira kunka kuchiundo cha nyumba, naitana munthu wovala bafutayo wokhala ndi zolembera nazo m'chuuno mwake. Ndipo Yehova ananena naye, Pita pakati pa mudzi, pakati pa Yerusalemu, nulembe chizindikiro pa mphumi zao za anthu akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zichitidwa pakati pake.