Nayankha Daniele pamaso pa mfumu, nati, Chinsinsi inachitira liuma mfumu, angakhale anzeru, openduza, alembi, kapena alauli, sakhoza kuchiululira mfumu; koma kuli Mulungu Kumwamba wakuvumbulutsa zinsinsi; Iye ndiye wadziwitsa mfumu Nebukadinezara chimene chidzachitika masiku otsiriza. Loto lanu, ndi masomphenya a m'mtima mwanu pakama panu, ndi awa