1
Genesis 26:3
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Khala mʼdziko lino ndipo ndidzakhala nawe ndi kukudalitsa. Pakuti kwa iwe ndi zidzukulu zako ndidzapereka mayiko onsewa. Choncho ndidzakwaniritsa pangano limene ndinalumbira kwa Abrahamu, abambo ako.
Compare
Explore Genesis 26:3
2
Genesis 26:4-5
Zidzukulu zako ndidzazichulukitsa ngati nyenyezi za mu mlengalenga ndi kuzipatsa mayiko onsewa. Ndiponso anthu onse a pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa zidzukulu zako, chifukwa Abrahamu anandimvera, nasunga malamulo anga onse.”
Explore Genesis 26:4-5
3
Genesis 26:22
Anachokapo pamenepo nakakumba china. Koma apa sanakanganiranenso ndi munthu. Iye anachitcha Kutakasuka, nati, “Tsopano Yehova watipatsa ife malo otakasukirako ndipo tilemera muno.”
Explore Genesis 26:22
4
Genesis 26:2
Yehova anadza kwa Isake nati, “Usapite ku Igupto; koma ukhale mʼdziko limene ndidzakuwuza kuti ukakhalemo.
Explore Genesis 26:2
5
Genesis 26:25
Isake anamanga guwa lansembe pamenepo ndipo anapembedza Yehova. Pomwepo anamanga tenti yake, ndipo antchito ake anakumba chitsime.
Explore Genesis 26:25
Home
Bible
Plans
Videos