1
Genesis 25:23
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Yehova anati kwa iye, “Udzabala mafuko awiri a anthu olimbana, ndipo magulu awiri a anthu ochokera mwa iwe adzasiyana; fuko limodzi lidzakhala la mphamvu kuposa linzake, ndipo wamkulu adzatumikira wamngʼono.”
Compare
Explore Genesis 25:23
2
Genesis 25:30
Iye anati kwa Yakobo, “Tandipatsako phala lofiiralo, ndimwe! Ndalefuka ndi njala.” (Nʼchifukwa chake amatchedwanso Edomu).
Explore Genesis 25:30
3
Genesis 25:21
Isake anapempherera mkazi wake kwa Yehova popeza iye anali wosabereka. Yehova anayankha pemphero lake ndipo mkazi wake Rebeka anatenga pathupi.
Explore Genesis 25:21
4
Genesis 25:32-33
Esau anati, “Chabwino, ine ndatsala pangʼono kufa, ukulu undithandiza chiyani?” Koma Yakobo anati, “Lumbira kwa ine choyamba.” Kotero Esau analumbiradi, ndipo anagulitsa ukulu wake kwa Yakobo.
Explore Genesis 25:32-33
5
Genesis 25:26
Kenaka mʼbale wake anabadwa atagwira chidendene cha Esau; choncho anamutcha Yakobo. Isake anali ndi zaka 60 pamene Rebeka anabereka mapasawa.
Explore Genesis 25:26
6
Genesis 25:28
Isake ankakonda Esau chifukwa cha nyama za kutchire zomwe ankakonda kudya, koma Rebeka ankakonda Yakobo.
Explore Genesis 25:28
Home
Bible
Plans
Videos