YOHANE 15

15
Mpesa ndi nthambi zake
1Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye wam'munda. 2#Mat. 15.13Nthambi iliyonse ya mwa Ine yosabala chipatso, aichotsa; ndi iliyonse yakubala chipatso, aisadza, kuti ikabale chipatso chochuluka. 3#Yoh. 17.17Mwakhala okonzeka tsopano inu chifukwa cha mau amene ndalankhula ndi inu. 4Khalani mwa Ine, ndi Ine mwa inu. Monga nthambi siingathe kubala chipatso pa yokha, ngati siikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala mwa Ine. 5#Afi. 1.11Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zake: wakukhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye, ameneyo abala chipatso chambiri; pakuti kopanda Ine simungathe kuchita kanthu. 6#Mat. 7.19Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto, nazitentha. 7#Yoh. 14.13-14Ngati mukhala mwa Ine, ndi mau anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene muchifuna ndipo chidzachitika kwa inu. 8#Mat. 5.16Mwa ichi alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale chipatso chambiri; ndipo mudzakhala ophunzira anga. 9Monga momwe Atate wandikonda Ine, Inenso ndakonda inu; khalani m'chikondi changa. 10#Yoh. 14.15, 21, 23Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'chikondi changa; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'chikondi chake. 11#Yoh. 16.24Izi ndalankhula ndi inu, kuti chimwemwe changa chikhale mwa inu, ndi kuti chimwemwe chanu chidzale. 12#1Yoh. 3.11Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzake, monga ndakonda inu. 13#Yoh. 10.11, 15Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. 14Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulani inu.
Chiyanjano chatsopano
15 # Mac. 20.27 Sinditchanso inu akapolo; chifukwa kapolo sadziwa chimene mbuye wake achita; koma ndatcha inu abwenzi; chifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziwitsani. 16#1Yoh. 4.10, 19; Yoh. 15.7Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala chipatso, ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chilichonse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu. 17#1Yoh. 3.11Zinthu izi ndilamula inu, kuti mukondane wina ndi mnzake.
Wokhulupirira pokhala padziko lapansi
18 # 1Yoh. 3.1, 13 Ngati dziko lapansi lida inu, mudziwa kuti lidada Ine lisanayambe kuda inu. 19#Yoh. 17.14; 1Yoh. 4.5Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zake za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu. 20#Mat. 10.24Kumbukirani mau amene Ine ndinanena kwa inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulondalondani inunso; ngati anasunga mau anga, adzasunga anunso. 21#Mat. 10.22Koma izi zonse adzakuchitirani chifukwa cha dzina langa, chifukwa sadziwa wondituma Ine. 22#Yoh. 9.41Sindikadadza ndi kulankhula nao sakadakhala nalo tchimo; koma tsopano alibe chowiringula pa machimo ao. 23#1Yoh. 2.23Iye wondida Ine, adanso Atate wanga. 24#Yoh. 9.32Sindikadachita mwa iwo ntchito zosachita wina, sakadakhala nalo tchimo; koma tsopano anaona, nada Ine ndi Atate wanganso. 25#Mas. 69.4Koma chitero, kuti mau olembedwa m'chilamulo chao akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda chifukwa.
Mzimu Woyera ndi ophunzira omwe adzachita umboni
26 # Yoh. 14.17, 26; 16.7, 13 Koma pamene wafika Nkhoswe, amene Ine ndidzamtuma kwa inu kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu wa choonadi, amene atuluka kwa Atate, Iyeyu adzandichitira Ine umboni. 27#Luk. 1.2; Mac. 1.8Ndipo inunso muchita umboni, pakuti muli ndi Ine kuyambira chiyambi.

المحددات الحالية:

YOHANE 15: BLP-2018

تمييز النص

شارك

نسخ

None

هل تريد حفظ أبرز أعمالك على جميع أجهزتك؟ قم بالتسجيل أو تسجيل الدخول